Add parallel Print Page Options

BUKU LACHINAYI

Masalimo 90–106

Pemphero la Mose munthu wa Mulungu.

90 Ambuye, mwakhala muli malo athu okhalamo
    pa mibado yonse.
Mapiri asanabadwe,
    musanalenge nʼkomwe dziko lapansi ndi dziko lonse,
    kuyambira muyaya mpaka muyaya Inu ndinu Mulungu.

Inu mumabwezera anthu ku fumbi,
    mumati, “Bwerera ku fumbi iwe mwana wa munthu.”
Pakuti zaka 1,000 pamaso panu
    zili ngati tsiku limene lapita
    kapena ngati kamphindi ka usiku.
Inu mumasesa anthu mʼtulo ta imfa,
    iwo ali ngati udzu watsopano wa mmawa,
ngakhale kuti mmawa umaphuka watsopano,
    pofika madzulo wauma ndi kufota.

Ife tathedwa ndi mkwiyo wanu;
    ndipo taopsezedwa ndi kuyipidwa kwanu.
Mwayika mphulupulu zathu pamaso panu,
    machimo athu obisika poonekera pamaso panu.
Masiku athu onse amatha ali pansi pa ukali wanu;
    timatsiriza zaka zathu ndi kubuwula.
10 Kuchuluka kwa masiku athu ndi 70,
    kapena 80 ngati tili ndi mphamvu;
komabe zaka zonsezi ndi za mavuto ndi nkhawa,
    zimatha mofulumira ndipo ife timawulukira kutali.

11 Kodi ndani amadziwa mphamvu ya mkwiyo wanu?
    Pakuti ukali wanu ndi waukulu ngati ulemu umene uyenera Inu.
12 Tiphunzitseni kuwerenga masiku athu molondola,
    kuti tikhale ndi mtima wanzeru.

13 Lezani mtima Inu Yehova! Kodi mudzatikwiyira mpaka liti?
    Achitireni chifundo atumiki anu.
14 Mutikhutitse mmawa ndi chikondi chanu chosatha,
    kuti tiyimbe ndi chimwemwe ndi kukhala okondwa masiku athu onse.
15 Tisangalatseni masiku ambiri monga masiku amene mwatisautsa,
    kwa zaka zambiri monga momwe tinaonera mavuto.
16 Ntchito zanu zionetsedwe kwa atumiki anu,
    kukongola kwanu kwa ana awo.

17 Kukoma mtima kwa Ambuye Mulungu wathu kukhale pa ife;
    tikhazikitsireni ntchito ya manja athu;
    inde, khazikitsani ntchito ya manja athu.
91 Iye amene amakhala mu mthunzi wa Wammwambamwamba
    adzapuma mu mthunzi wa Wamphamvuzonse.
Ndidzanena za Yehova, “Iye ndiye pothawira panga ndi linga langa,
    Mulungu wanga amene ndimadalira.”

Ndithu, Iye adzakupulumutsa ku msampha wa mlenje
    ndi ku mliri woopsa;
Adzakuphimba ndi nthenga zake,
    ndipo udzapeza malo othawira mʼmapikomo;
    kukhulupirika kwake kudzakhala chishango chako ndi lihawo.
Sudzachita mantha ndi zoopsa za usiku,
    kapena muvi wowuluka masana,
kapena mliri umene umayenda mu mdima,
    kapena zowononga za pa nthawi ya masana.
Anthu 1,000 atha kufa pambali pako,
    anthu 10,000 kudzanja lako lamanja,
    koma zoopsazo sizidzafika pafupi ndi iwe.
Udzapenya ndi maso ako
    ndipo udzaona mmene anthu oyipa amalangidwira.

Pakuti wasankha Wammwambamwamba kukhala malo ako okhalamo;
    wavomera Yehova kukhala kothawira kwako.
10 Choncho palibe choyipa chimene chidzakugwera,
    zoopsa sizidzafika pafupi ndi tenti yako.
11 Pakuti adzalamulira angelo ake za iwe,
    kuti akutchinjirize mosamala pa njira zako zonse;
12 ndipo adzakunyamula ndi manja awo,
    kuti phazi lako lisagunde pa mwala.
13 Udzapondaponda mkango ndi njoka,
    udzapondereza mkango wamphamvu ndiponso chinjoka.

14 “Chifukwa iye amandikonda,” akutero Yehova, “Ndidzamulanditsa;
    ndidzamuteteza pakuti wavomereza dzina langa.
15 Adzandiyitana, ndipo ndidzamuyankha;
    ndidzakhala naye pa mavuto,
    ndidzamupulumutsa ndi kumulemekeza.
16 Ndidzamupatsa moyo wautali
    ndi kumupulumutsa.”

Salimo. Nyimbo ya pa tsiku la Sabata.

92 Nʼkwabwino kutamanda Yehova
    ndi kuyimbira nyimbo dzina lanu, Inu Wammwambamwamba,
Kulengeza chikondi chanu mmawa,
    ndi kukhulupirika kwanu nthawi ya usiku,
kuyimbira nyimbo choyimbira cha zingwe khumi
    ndi mayimbidwe abwino a zeze.

Pakuti Inu mumandisangalatsa ndi ntchito zanu, Inu Yehova;
    Ine ndikuyimba mwachimwemwe pa ntchito ya manja anu.
Ndi yayikuludi ntchito yanu Yehova,
    maganizo anu ndi ozamadi!
Munthu wopanda nzeru sadziwa,
    zitsiru sizizindikira,
kuti ngakhale anthu oyipa aphuka ngati udzu
    ndipo anthu onse ochita zoyipa apindula,
adzawonongedwa kwamuyaya.

Koma Inu Yehova, ndinu wokwezedwa kwamuyaya.

Zoonadi adani anu Yehova,
    zoonadi adani anu adzawonongeka;
    onse ochita zoyipa adzabalalitsidwa.
10 Inu mwakweza nyanga yanga ngati nyanga ya njati;
    mafuta abwino akhuthulidwa pamutu wanga.
11 Maso anga aona kugonjetsedwa kwa olimbana nane,
    makutu anga amva za kugwa kwa amaliwongo anga oyipa.

12 Anthu olungama adzaphuka ngati mtengo wa mgwalangwa,
    adzakula ngati mkungudza wa ku Lebanoni;
13 odzalidwa mʼnyumba ya Yehova,
    adzakula bwino mʼmabwalo a Mulungu wathu.
14 Iwo adzaberekabe zipatso mu ukalamba wawo,
    adzakhala anthete ndi obiriwira,
15 kulengeza kuti, “Yehova ndi wolungama;
    Iye ndiye Thanthwe langa, ndipo mwa Iye mulibe choyipa.”
93 Yehova akulamulira, wavala ulemerero;
    Yehova wavala ulemerero ndipo wadzimangirira mphamvu,
    dziko lonse lakhazikika kolimba; silingasunthidwe.
Mpando wanu waufumu unakhazikika kalekale;
    Inu ndinu wamuyaya.

Nyanja zakweza Inu Yehova,
    nyanja zakweza mawu ake;
    nyanja zakweza mafunde ake ochita mkokomo.
Yehova ndi wamphamvu kupambana mkokomo wa madzi ambiri,
    ndi wamphamvu kupambana mafunde a nyanja,
    Yehova mmwamba ndi wamphamvu.

Malamulo anu Yehova ndi osasinthika;
    chiyero chimakongoletsa nyumba yanu
    mpaka muyaya.
94 Inu Yehova, ndinu Mulungu wobwezera chilango,
    Inu Mulungu amene mumabwezera chilango, wonetsani kuwala kwanu.
Nyamukani, Inu woweruza wa dziko lapansi;
    bwezerani kwa odzikuza zowayenera.
Kodi mpaka liti anthu oyipa Inu Yehova,
    mpaka liti anthu oyipa adzalumpha ndi chimwemwe?

Amakhuthula mawu onyada;
    onse ochita zoyipa ndi odzaza ndi kudzikuza.
Amaphwanya anthu anu, Inu Yehova;
    amapondereza cholowa chanu.
Amaphanso amayi a masiye ndi alendo okhala nawo mʼdziko;
    amapha ana amasiye.
Iwo amati, “Yehova sakuona;
    Mulungu wa Yakobo salabadirako.”

Samalani, inu anthu opanda nzeru pakati pa anthu;
    zitsiru inu, kodi mudzakhala liti anzeru?
Kodi Iye amene anapanga khutu sangathe kumva?
    Kodi Iye amene anapanga diso sangathe kuona?
10 Kodi Iye amene amalangiza mitundu ya anthu sangathenso kulanga?
    Kodi Iye amene amaphunzitsa munthu angasowe nzeru?
11 Yehova amadziwa maganizo a munthu;
    Iye amadziwa kuti maganizowo ndi achabechabe.

12 Wodala munthu amene Inu Yehova mumamulangiza,
    munthu amene mumamuphunzitsa kuchokera mulamulo lanu;
13 mumamupumitsa pa nthawi ya mavuto,
    mpaka woyipa atakumbiridwa dzenje.
14 Pakuti Yehova sadzawakana anthu ake;
    Iye sadzasiya cholowa chake.
15 Chiweruzo chidzakhazikikanso pa chilungamo,
    ndipo onse olungama mtima adzachitsata.

16 Ndani adzadzuka chifukwa cha ine kulimbana ndi anthu oyipa?
    Ndani adzayimirira mʼmalo mwanga kulimbana ndi anthu ochita zoyipa?
17 Yehova akanapanda kundithandiza,
    bwenzi nditakakhala msanga ku malo achete a imfa.
18 Ndikanena kuti, “Phazi langa likuterereka,”
    chikondi chanu, Inu Yehova, chimandichirikiza.
19 Pamene nkhawa inakula mʼkati mwanga,
    chitonthozo chanu chinabweretsa chimwemwe mʼmoyo mwanga.

20 Kodi mpando waufumu woyipa ungathe kugwirizana nanu
    umene umabweretsa masautso chifukwa cha malamulo ake?
21 Iwo amasonkhana pamodzi kulimbana ndi wolungama
    ndi kugamula kuti wosalakwa aphedwe.
22 Koma Yehova wakhala linga langa,
    ndipo Mulungu ndiye thanthwe limene ndimathawirako.
23 Iye adzawabwezera chifukwa cha machimo awo
    ndi kuwawononga chifukwa cha kuyipa kwawo;
    Yehova Mulungu wathu adzawawononga.
95 Bwerani, tiyeni timuyimbire Yehova mwachimwemwe,
    tiyeni tifuwule kwa Thanthwe la chipulumutso chathu
Tiyeni tibwere pamaso pake ndi chiyamiko
    ndipo mupembedzeni Iyeyo ndi zida zoyimbira ndi nyimbo.

Pakuti Yehova ndi Mulungu wamkulu,
    mfumu yayikulu pamwamba pa milungu yonse.
Mʼmanja mwake muli maziko ozama a dziko lapansi,
    ndipo msonga za mapiri ndi zake.
Nyanja ndi yake, pakuti anayilenga ndi Iye,
    ndipo manja ake anawumba mtunda wowuma.

Bwerani, tiyeni tiwerame pomulambira,
    tiyeni tigwade pamaso pa Yehova Mlengi wathu;
pakuti Iye ndiye Mulungu wathu
    ndipo ife ndife anthu a pabusa pake,
    ndi nkhosa za mʼdzanja lake.

Lero ngati inu mumva mawu ake,
    musawumitse mitima yanu monga momwe munachitira pa Meriba,
    monga munachitira tsiku lija pa Masa mʼchipululu.
Kumene makolo anu anandiyesa ndi kundiputa,
    ngakhale anaona zimene Ine ndinazichita.
10 Kwa zaka makumi anayi ndinali wokwiya ndi mʼbado umenewo;
    ndipo ndinati, “Iwo ndi anthu amene mitima yawo imasochera
    ndipo sanadziwe njira zanga.”
11 Choncho ndili chikwiyire, ndinalumbira kuti,
    “Iwowa sadzalowa ku malo anga a mpumulo.”
96 Imbirani Yehova nyimbo yatsopano;
    Imbirani Yehova dziko lonse lapansi.
Imbirani Yehova, tamandani dzina lake;
    lalikirani chipulumutso chake tsiku ndi tsiku.
Lengezani ulemerero wake pakati pa mayiko,
    ntchito zake zodabwitsa pakati pa mitundu yonse ya anthu.

Pakuti wamkulu ndi Yehova ndipo ndi woyenera kwambiri kumutamanda;
    ayenera kuopedwa kupambana milungu yonse.
Pakuti milungu yonse ya anthu a mitundu ina ndi mafano,
    koma Yehova analenga mayiko akumwamba.
Ulemu ndi ufumu zili pamaso pake,
    mphamvu ndi ulemerero zili mʼmalo ake opatulika.

Perekani kwa Yehova, inu mabanja a anthu a mitundu ina,
    perekani kwa Yehova ulemerero ndi mphamvu.
Perekani kwa Yehova ulemerero woyenera dzina lake;
    bweretsani chopereka ndipo mulowe mʼmabwalo ake.
Lambirani Yehova mu ulemerero wa chiyero chake;
    njenjemerani pamaso pake, dziko lonse lapansi.

10 Nenani pakati pa mitundu ya anthu, “Yehova akulamulira.”
    Dziko lonse lakhazikika molimba, silingasunthidwe;
    Iye adzaweruza mitundu ya anthu molungama.
11 Mayiko akumwamba asangalale, dziko lapansi likondwere;
    nyanja ikokome, ndi zonse zili mʼmenemo;
12     minda ikondwere pamodzi ndi chilichonse chili mʼmenemo.
Pamenepo mitengo yonse ya mʼnkhalango idzayimba ndi chimwemwe;
13     idzayimba pamaso pa Yehova,
    pakuti Iye akubwera kudzaweruza dziko lapansi;
adzaweruza dziko lonse mwachilungamo
    ndi mitundu ya anthu onse mʼchoonadi.
97 Yehova akulamulira, dziko lapansi lisangalale;
    magombe akutali akondwere.

Mitambo ndi mdima waukulu zamuzungulira;
    chilungamo ndi kuweruza molungama ndiwo maziko a mpando wake waufumu.
Moto umapita patsogolo pake
    ndi kunyeketsa amaliwongo kumbali zonse.
Zingʼaningʼani zake zimawalitsa dziko lonse;
    dziko lapansi limaona ndipo limanjenjemera.
Mapiri amasungunuka ngati phula pamaso pa Yehova,
    pamaso pa Ambuye a dziko lonse lapansi.
Mayiko akumwamba amalengeza za chilungamo chake,
    ndipo mitundu yonse ya anthu imaona ulemerero wake.

Onse amene amalambira mafano osema amachititsidwa manyazi,
    iwo amene amanyadira mafano;
    mulambireni, inu milungu yonse!

Ziyoni akumva ndipo akukondwera,
    midzi ya Yuda ikusangalala
    chifukwa cha maweruzo anu Yehova.
Pakuti Inu Yehova ndi Wammwambamwamba pa dziko lonse lapansi;
    ndinu wokwezeka kupambana milungu yonse.

10 Iwo amene amakonda Yehova adane ndi zoyipa
    pakuti Iye amayangʼanira miyoyo ya amene amamukhulupirira
    ndipo amawapulumutsa mʼdzanja la anthu oyipa
11 Kuwala kumafika pa anthu olungama,
    ndi chimwemwe kwa olungama mtima.
12 Kondwerani mwa Yehova Inu olungama
    ndipo tamandani dzina lake loyera.

Salimo.

98 Imbirani Yehova nyimbo yatsopano,
    pakuti Iyeyo wachita zinthu zodabwitsa;
dzanja lake lamanja ndi mkono wake woyera
    zamuchitira chipulumutso.
Yehova waonetsa chipulumutso chake
    ndipo waulula chilungamo chake kwa anthu a mitundu ina.
Iye wakumbukira chikondi chake
    ndi kukhulupirika kwake pa Aisraeli;
malekezero onse a dziko lapansi aona
    chipulumutso cha Mulungu wathu.

Fuwulani mwachimwemwe kwa Yehova, dziko lonse lapansi,
    muyimbireni nyimbo mofuwula ndi mokondwera.
Imbirani Yehova nyimbo ndi zeze,
    ndi zeze ndi mawu a kuyimba,
ndi malipenga ndi kuliza kwa nyanga ya nkhosa yayimuna
    fuwulani mwachimwemwe pamaso pa Yehova Mfumu.

Nyanja ikokome pamodzi ndi zonse zili mʼmenemo,
    dziko lonse ndi onse amene amakhala mʼmenemo.
Mitsinje iwombe mʼmanja mwawo,
    mapiri ayimbe pamodzi mwachimwemwe;
izo ziyimbe pamaso pa Yehova,
    pakuti Iye akubwera kudzaweruza dziko lapansi.
Adzaweruza dziko lonse mwachilungamo,
    ndi mitundu ya anthu mosakondera.
99 Yehova akulamulira,
    mitundu ya anthu injenjemere;
Iye wakhala pa mpando wake waufumu, pakati pa akerubi,
    dziko lapansi ligwedezeke.
Mʼziyoni wamkulu ndi Yehova;
    Iye ndi wokwezeka pamwamba pa mitundu yonse ya anthu.
Anthu atamande dzina lanu lalikulu ndi loopsa kwambiri,
    Iye ndi woyera.

Mfumu yamphamvu, iyo imakonda chilungamo
    Inu mwakhazikitsa khalidwe losakondera;
mwachita zolungama ndi zoyenera mwa Yakobo.
Kwezani Yehova Mulungu wathu
    ndipo mulambireni pa mapazi ake;
    Iye ndi woyera.

Mose ndi Aaroni anali ena mwa ansembe ake,
    Samueli anali pamodzi ndi iwo amene anayitana pa dzina lake;
iwo anayitana Yehova
    ndipo Iyeyo anawayankha.
Iye anayankhula nawo kuchokera mʼchipilala cha mtambo;
    iwo anasunga malamulo ake ndi zophunzitsa zomwe anawapatsa.

Inu Yehova Mulungu wathu,
    munawayankha iwo;
Inu kwa Israeli munali Mulungu wokhululuka,
    ngakhale munawalanga pa zochita zawo zoyipa.
Kwezani Yehova Mulungu wathu
    ndipo mumulambire pa phiri lake loyera,
    pakuti Yehova Mulungu wathu ndi woyera.

Salimo. Nyimbo yothokoza.

100 Fuwulani kwa Yehova mwachimwemwe, inu dziko lonse lapansi.
    Mulambireni Yehova mosangalala;
    bwerani pamaso pake ndi nyimbo zachikondwerero.
Dziwani kuti Yehova ndi Mulungu.
    Iye ndiye amene anatipanga ndipo ife ndife ake;
    ndife anthu ake, nkhosa za pabusa pake.

Lowani ku zipata zake ndi chiyamiko
    ndi ku mabwalo ake ndi matamando;
    muyamikeni ndi kutamanda dzina lake.
Pakuti Yehova ndi wabwino ndipo chikondi chake ndi chamuyaya;
    kukhulupirika kwake nʼkokhazikika pa mibado ndi mibado.

Salimo la Davide.

101 Ndidzayimba za chikondi ndi chiweruzo chanu cholungama;
    kwa Inu Yehova ndidzayimba matamando.
Ndidzatsata njira yolungama;
    nanga mudzabwera liti kwa ine?

Ndidzayenda mʼnyumba mwanga
    ndi mtima wosalakwa.
Sindidzayika chinthu chilichonse choyipa
    pamaso panga.

Ine ndimadana ndi zochita za anthu opanda chikhulupiriro;
    iwo sadzadziphatika kwa ine.
Anthu a mtima wokhota adzakhala kutali ndi ine;
    ine sindidzalola choyipa chilichonse kulowa mwa ine.

Aliyense wosinjirira mnansi wake mseri
    ameneyo ndidzamuletsa;
aliyense amene ali ndi maso amwano ndi mtima wodzikuza,
    ameneyo sindidzamulekerera.

Maso anga adzakhala pa okhulupirika mʼdziko,
    kuti akhale pamodzi ndi ine;
iye amene mayendedwe ake ndi wosalakwa
    adzanditumikira.

Aliyense wochita chinyengo
    sadzakhala mʼnyumba mwanga.
Aliyense woyankhula mwachinyengo
    sadzayima pamaso panga.

Mmawa uliwonse ndidzatontholetsa anthu
    onse oyipa mʼdziko;
ndidzachotsa aliyense wochita zoyipa
    mu mzinda wa Yehova.

Pemphero la munthu wosautsidwa, pamene walefuka, nakhuthulira pamaso pa Yehova kulira kwakeko.

102 Yehova imvani pemphero langa;
    kulira kwanga kopempha thandizo kufike kwa Inu.
Musandibisire nkhope yanu
    pamene ndili pa msautso.
Munditcherere khutu;
    pamene ndiyitana ndiyankheni msanga.

Pakuti masiku anga akupita ngati utsi;
    mafupa anga akunyeka ngati nkhuni zoyaka.
Mtima wanga wakanthidwa ndipo ukufota ngati udzu;
    ndipo ndimayiwala kudya chakudya changa.
Chifukwa cha kubuwula kwanga kofuwula
    ndatsala chikopa ndi mafupa okhaokha.
Ndili ngati kadzidzi wa ku chipululu,
    monga kadzidzi pakati pa mabwinja.
Ndimagona osapeza tulo; ndakhala
    ngati mbalame yokhala yokha pa denga.
Tsiku lonse adani anga amandichita chipongwe;
    iwo amene amandinyoza, amagwiritsa ntchito dzina langa ngati temberero.
Pakuti ndimadya phulusa ngati chakudya changa
    ndi kusakaniza chakumwa changa ndi misozi
10 chifukwa cha ukali wanu waukulu,
    popeza Inu mwandinyamula ndi kunditayira kumbali.
11 Masiku anga ali ngati mthunzi wa kumadzulo;
    Ine ndikufota ngati udzu.

12 Koma Inu Yehova, muli pa mpando wanu waufumu kwamuyaya;
    kudziwika kwanu ndi kokhazikika ku mibado yonse.
13 Inu mudzadzuka ndi kuchitira chifundo Ziyoni
    pakuti ndi nthawi yoti muonetse kukoma mtima kwanu pa iyeyo;
    nthawi yoyikika yafika.
14 Pakuti miyala yake ndi yokondedwa kwa atumiki anu;
    fumbi lake lokha limawachititsa kuti amve chisoni.
15 Mitundu ya anthu idzaopa dzina la Yehova,
    mafumu onse a dziko lapansi adzalemekeza ulemerero wanu.
16 Pakuti Yehova adzamanganso Ziyoni
    ndi kuonekera mu ulemerero wake.
17 Iye adzayankha pemphero la anthu otayika;
    sadzanyoza kupempha kwawo.

18 Zimenezi zilembedwe chifukwa cha mibado ya mʼtsogolo,
    kuti anthu amene sanabadwe adzatamande Yehova:
19 “Yehova anayangʼana pansi kuchokera ku malo ake opatulika mmwamba,
    kuchokera kumwamba anayangʼana dziko lapansi,
20 kuti amve kubuwula kwa anthu a mʼndende,
    kuti apulumutse amene anayenera kuphedwa.”
21 Kotero dzina la Yehova lidzalengezedwa mu Ziyoni
    ndi matamando ake mu Yerusalemu,
22 pamene mitundu ya anthu ndi maufumu
    adzasonkhana kuti alambire Yehova.

23 Iye anathyola mphamvu zanga pa nthawi ya moyo wanga;
    Iyeyo anafupikitsa masiku anga.
24 Choncho Ine ndinati:
    “Musandichotse, Inu Mulungu wanga, pakati pa masiku a moyo wanga;
    zaka zanu zimakhalabe pa mibado yonse.
25 Pachiyambi Inu munakhazikitsa maziko a dziko lapansi
    ndipo mayiko akumwamba ndi ntchito ya manja anu.
26 Izi zidzatha, koma Inu mudzakhalapo;
    zidzatha ngati chovala.
Mudzazisintha ngati chovala
    ndipo zidzatayidwa.
27 Koma Inu simusintha,
    ndipo zaka zanu sizidzatha.
28 Ana a atumiki anu adzakhala pamaso panu;
    zidzukulu zawo zidzakhazikika pamaso panu.”

Salimo la Davide.

103 Tamanda Yehova, iwe moyo wanga;
    ndi zonse zamʼkati mwanga zitamande dzina lake loyera.
Tamanda Yehova, iwe moyo wanga,
    ndipo usayiwale zabwino zake zonse.
Amene amakhululuka machimo ako onse
    ndi kuchiritsa nthenda zako zonse,
amene awombola moyo wako ku dzenje
    ndi kukuveka chikondi ndi chifundo chake ngati chipewa chaufumu,
amene akwaniritsa zokhumba zako ndi zinthu zabwino,
    kotero kuti umakhala wamphamvu zatsopano ngati mphungu.

Yehova amachita chilungamo
    ndipo amaweruza molungama onse opsinjika.

Iye anadziwitsa Mose njira zake,
    ntchito zake kwa Aisraeli.
Yehova ndi wachifundo ndi wokoma mtima,
    wosakwiya msanga ndi wachikondi chochuluka.
Iye sadzatsutsa nthawi zonse,
    kapena kusunga mkwiyo wake kwamuyaya;
10 satichitira molingana ndi machimo athu,
    kapena kutibwezera molingana ndi mphulupulu zathu.
11 Pakuti monga kumwamba kuli kutali ndi dziko lapansi,
    koteronso chikondi chake nʼchachikulu kwa iwo amene amamuopa;
12 monga kummawa kutalikirana ndi kumadzulo,
    koteronso Iye watichotsera mphulupulu zathu kuti zikhale kutali nafe.
13 Monga bambo amachitira chifundo ana ake,
    choncho Yehova ali ndi chifundo ndi iwo amene amamuopa;
14 pakuti Iye amadziwa momwe tinawumbidwira,
    amakumbukira kuti ndife fumbi.
15 Kunena za munthu, masiku ake ali ngati udzu,
    amaphuka ngati duwa la mʼmunda;
16 koma mphepo imawombapo ndipo silionekanso
    ndipo malo ake sakumbukirikanso.
17 Koma kuchokera muyaya mpaka muyaya
    chikondi cha Yehova chili ndi iwo amene amamuopa,
    ndi chilungamo chake chili ndi ana a ana awo;
18 iwo amene amasunga pangano lake
    ndi kukumbukira kumvera malangizo ake.

19 Yehova wakhazikitsa mpando wake waufumu mmwamba
    ndipo ufumu wake umalamulira onse.

20 Tamandani Yehova, inu angelo ake,
    amphamvu inu amene mumachita zimene amalamula,
    amene mumamvera mawu ake.
21 Tamandani Yehova, zolengedwa zonse zakumwamba,
    inu atumiki ake amene mumachita chifuniro chake.
22 Tamandani Yehova, ntchito yake yonse
    kulikonse mu ulamuliro wake.

Tamanda Yehova, iwe moyo wanga.
104 Tamanda Yehova, iwe moyo wanga.

Inu Yehova Mulungu wanga, ndinu wamkulu kwambiri;
    mwavala ulemerero ndi ufumu.
Iye wadzifunditsa kuwala ngati chovala;
    watambasula miyamba ngati tenti
    ndipo wayika pa madzi mitanda ya chipinda chake.
Iye amasandutsa mitambo kukhala galeta lake,
    ndi kuwuluka pa mapiko a mphepo.
Amapanga mphepo kukhala amithenga ake,
    malawi amoto kukhala atumiki ake.

Anakhazikitsa dziko lapansi pa maziko ake;
    silingasunthike.
Munaliphimba ndi nyanja yozama ngati chovala;
    madzi anayimirira pamwamba pa mapiri.
Koma pakudzudzula kwanu madzi anathawa,
    pa mkokomo wa bingu lanu iwo anamwazika;
Inu munamiza mapiri,
    iwo anatsikira ku zigwa
    kumalo kumene munawakonzera.
Inu munayika malire ndipo sangathe kudutsa,
    iwo sadzamizanso dziko lapansi.

10 Iye achititsa akasupe kutulutsa madzi kupita ku zigwa;
    madziwo amayenda pakati pa mapiri.
11 Iwo amapereka madzi kwa zirombo zonse zakuthengo;
    abulu akuthengo amapha ludzu lawo.
12 Mbalame zamlengalenga zimayika zisa mʼmbali mwa madzi;
    zimayimba pakati pa thambo.
13 Iye amathirira mapiri kuchokera ku zipinda zake zapamwamba;
    dziko lapansi limakhutitsidwa ndi chipatso cha ntchito yake.
14 Amameretsa udzu kuti ngʼombe zidye,
    ndi zomera, kuti munthu azilima
    kubweretsa chakudya kuchokera mʼdziko lapansi:
15 vinyo amene amasangalatsa mtima wa munthu,
    mafuta amene amachititsa nkhope yake kuwala,
    ndi buledi amene amapereka mphamvu.
16 Mitengo ya Yehova ndi yothiriridwa bwino,
    mikungudza ya ku Lebanoni imene Iye anadzala.
17 Mbalame zimamanga zisa zawo;
    kakowa ali ndi malo ake mʼmikungudzamo.
18 Mapiri ataliatali ndi a mbalale;
    mʼmingʼalu ya miyala ndi mobisalamo mbira.

19 Mwezi umasiyanitsa nyengo
    ndipo dzuwa limadziwa nthawi yake yolowera.
20 Inu mumabweretsa mdima nukhala usiku,
    ndipo zirombo zonse za ku nkhalango zimatuluka.
21 Mikango imabangula kufuna nyama,
    ndi kufunafuna chakudya chawo kuchokera kwa Mulungu.
22 Dzuwa limatuluka ndipo iyo imapita kukabisala;
    imabwerera kukagona pansi mʼmapanga awo.
23 Pamenepo munthu amapita ku ntchito yake,
    kukagwira ntchito yake mpaka madzulo.

24 Ntchito zanu ndi zochulukadi Inu Yehova!
    Munazipanga zonse mwanzeru,
    dziko lapansi ladzaza ndi zolengedwa zanu.
25 Kuli nyanja yayikulu ndi yotambalala,
    yodzaza ndi zolengedwa zosawerengeka,
    zamoyo zanu zazikulu ndi zazingʼono zomwe.
26 Kumeneko sitima zapamadzi zimayenda uku ndi uku,
    ndiponso Leviyatani amene munamulenga kuti asewere kumeneko.

27 Zonsezi zimayangʼana kwa Inu
    kuti muzipatse chakudya chawo pa nthawi yake yoyenera.
28 Mukazipatsa,
    zimachisonkhanitsa pamodzi;
mukatsekula dzanja lanu,
    izo zimakhutitsidwa ndi zinthu zabwino.
29 Mukabisa nkhope yanu,
    izo zimachita mantha aakulu;
mukachotsa mpweya wawo,
    zimafa ndi kubwerera ku fumbi.
30 Mukatumiza mzimu wanu,
    izo zimalengedwa
    ndipo mumakozanso maonekedwe a dziko lapansi.

31 Ulemerero wa Yehova ukhalebe mpaka muyaya;
    Yehova akondwere ndi ntchito ya manja ake;
32 Iye amene amayangʼana dziko lapansi ndipo limanjenjemera,
    amene amakhudza mapiri ndipo amatuluka utsi.

33 Ine ndidzayimbira Yehova moyo wanga wonse;
    ndidzayimbira matamando Mulungu wanga nthawi yonse imene ndili ndi moyo.
34 Zolingalira zanga zikhale zomukomera Iye,
    pamene ndikusangalala mwa Yehova.
35 Koma anthu ochimwa awonongeke pa dziko lapansi
    ndipo anthu oyipa asapezekenso.

Tamanda Yehova, Iwe moyo wanga.

Tamandani Yehova.
105 Yamikani Yehova, itanani dzina lake;
    lalikirani pakati pa anthu a mitundu ina zimene Iye wachita.
Imbirani Iye, imbani matamando kwa Iyeyo;
    fotokozani za machitidwe ake onse odabwitsa.
Munyadire dzina lake loyera;
    mitima ya iwo amene amafunafuna Yehova ikondwere.
Dalirani Yehova ndi mphamvu zake;
    funafunani nkhope yake nthawi yonse.

Kumbukirani zodabwitsa zimene Iye anazichita,
    zozizwitsa zake ndi maweruzo amene anapereka,
inu zidzukulu za Abrahamu mtumiki wake,
    inu ana a Yakobo, osankhika ake.
Iye ndiye Yehova Mulungu wathu;
    maweruzo ake ali pa dziko lonse lapansi.

Iyeyo amakumbukira pangano lake kwamuyaya,
    mawu amene analamula kwa mibado yonse,
pangano limene Iye anapanga ndi Abrahamu,
    lumbiro limene analumbira kwa Isake.
10 Iye analitsimikiza kwa Yakobo monga zophunzitsa,
    kwa Israeli monga pangano lamuyaya:
11 “Ndidzapereka kwa iwe dziko la Kanaani
    ngati gawo la cholowa chako.”

12 Pamene iwo anali ngati anthu ochepa mʼchiwerengero,
    ochepa ndithu, ndiponso alendo mʼdzikolo,
13 ankayendayenda kuchoka ku mtundu wina wa anthu ndi kupita ku mtundu wina,
    kuchoka mu ufumu wina kupita ku wina.
14 Iye sanalole wina aliyense kuwapondereza;
    anadzudzula mafumu chifukwa cha iwo:
15 “Musakhudze odzozedwa anga;
    musachitire choyipa aneneri anga.”

16 Iye anabweretsa njala pa dziko
    ndipo anawononga chakudya chonse;
17 Iyeyo anatumiza munthu patsogolo pawo,
    Yosefe anagulitsidwa ngati kapolo.
18 Iwo anavulaza mapazi ake ndi matangadza,
    khosi lake analiyika mʼzitsulo,
19 mpaka zimene Iye ananeneratu zitakwaniritsidwa,
    mpaka mawu a Yehova ataonetsa kuti Iye ananena zoona.
20 Mfumu inatuma munthu kukamumasula,
    wolamulira wa mitundu ya anthu anamasula iyeyo.
21 Anamuyika kukhala wolamulira nyumba yake,
    wolamulira zonse zimene iye anali nazo,
22 kulangiza ana a mfumu monga ankafunira
    ndi kuphunzitsa nzeru akuluakulu.

23 Tsono Israeli analowa mu Igupto;
    Yakobo anakhala monga mlendo mʼdziko la Hamu.
24 Yehova anachulukitsa anthu ake;
    ndipo anachititsa kuti akhale ochuluka kwambiri kuposa adani awo;
25 amene mitima yawo anayitembenuza kuti idane ndi anthu ake,
    kukonzera chiwembu atumiki ake.
26 Yehova anatuma Mose mtumiki wake,
    ndi Aaroni amene Iye anamusankha.
27 Iwo anachita zizindikiro zozizwitsa pakati pawo,
    zodabwitsa zake mʼdziko la Hamu.
28 Yehova anatumiza mdima nasandutsa dziko kuti likhale la mdima.
    Koma anthuwo anakaniratu mawu a Yehova.
29 Yehova anasandutsa madzi awo kukhala magazi,
    kuchititsa kuti nsomba zawo zife.
30 Dziko lawo linadzaza ndi achule
    amene analowa mʼzipinda zogona za olamulira awo.
31 Iye anayankhula, ndipo kunabwera ntchentche zochuluka
    ndi nsabwe mʼdziko lawo lonse.
32 Iyeyo anatembenuza mvula yawo kukhala matalala,
    ndi zingʼaningʼani mʼdziko lawo lonse;
33 Anagwetsa mitengo yawo ya mpesa ndi mitengo yawo ya mkuyu,
    nawononganso mitengo ina ya mʼdziko lawolo.
34 Iye anayankhula, ndipo dzombe linabwera,
    ziwala zosawerengeka;
35 zinadya chilichonse chobiriwira cha mʼdziko lawo,
    zinadya zonse zotuluka mʼnthaka yawo.
36 Kenaka anakantha ana onse oyamba kubadwa a mʼdziko lawo,
    zipatso zoyamba za umunthu wawo wonse.

37 Yehova anatulutsa Israeli, atatenga siliva ndi golide wambiri,
    ndipo pakati pa mafuko awo palibe mmodzi amene anafowoka.
38 Dziko la Igupto linakondwa pamene iwo anachoka,
    pakuti kuopsa kwa Israeli kunawagwera iwo.
39 Iye anatambasula mitambo ngati chofunda chawo,
    ndi moto owawunikira usiku.
40 Iwo anapempha, ndipo Iye anawabweretsera zinziri
    ndipo anawakhutitsa ndi chakudya chochokera kumwamba.
41 Iye anatsekula thanthwe, ndipo madzi anatuluka;
    ngati mtsinje anayenda mʼchipululu.

42 Pakuti anakumbukira lonjezo lake loyera limene
    linaperekedwa kwa Abrahamu mtumiki wake.
43 Iye anatulutsa anthu ake akukondwera,
    osankhika ake akufuwula mwachimwemwe;
44 Iye anawapatsa mayiko a anthu a mitundu ina
    ndipo anakhala olowamʼmalo a zimene ena anazivutikira,
45 kuti iwo asunge malangizo ake
    ndi kutsatira malamulo ake.

Tamandani Yehova.
106 Tamandani Yehova.

Yamikani Yehova chifukwa ndi wabwino;
    pakuti chikondi chake ndi chosatha.
Ndani angathe kufotokoza za ntchito zamphamvu za Yehova
    kapena kumutamanda mokwanira?
Odala ndi amene amasunga chilungamo,
    amene amachita zolungama nthawi zonse.
Mundikumbukire Yehova, pamene mukuonetsa kukoma mtima kwanu kwa anthu anu,
    bwerani mudzandithandize pamene mukuwapulumutsa iwo,
kuti ndidzasangalale ndi chuma cha anthu anu osankhika,
    kuti ndidzakhale nacho chimwemwe cha anthu anu
    ndi kukhala pamodzi ndi cholowa chanu pa kukutamandani.

Ife tachimwa monga momwe anachitira makolo athu;
    tachita zolakwa ndipo tachita moyipa.
Pamene makolo athu anali mu Igupto,
    sanalingalire za zozizwitsa zanu;
iwo sanakumbukire kukoma mtima kwanu kochuluka,
    ndipo anawukira Inu pa Nyanja Yofiira.
Komabe Iye anawapulumutsa chifukwa cha dzina lake,
    kuti aonetse mphamvu zake zazikulu.
Anadzudzula Nyanja Yofiira, ndipo inawuma;
    anawatsogolera mʼnyanja yakuya ngati akuyenda mʼchipululu.
10 Anawapulumutsa mʼdzanja la amaliwongo;
    anawawombola mʼdzanja la mdani.
11 Madzi anamiza adani awo,
    palibe mmodzi wa iwo anapulumuka.
12 Kenaka iwo anakhulupirira malonjezo ake
    ndi kuyimba nyimbo zamatamando.

13 Koma posachedwa anayiwala zimene Iye anachita,
    ndipo sanayembekezere uphungu wake.
14 Mʼchipululu, anadzipereka ku zilakolako zawo;
    mʼdziko lopanda kanthu anayesa Mulungu.
15 Choncho Iye anawapatsa chimene anapempha,
    koma anatumiza nthenda yowondetsa.

16 Mʼmisasa, anachitira nsanje Mose ndi Aaroni,
    amene Yehova anadzipatulira.
17 Nthaka inatsekuka ndipo inameza Datani;
    inakwirira gulu la Abiramu.
18 Moto unayaka pakati pa otsatira awo;
    lawi lamoto linapsereza anthu oyipa.

19 Iwo anapanga mwana wangʼombe pa Horebu
    ndi kulambira fano loyengedwa kuchokera ku chitsulo.
20 Anasinthanitsa ulemerero wawo
    ndi fano la ngʼombe yayimuna imene imadya udzu.
21 Anayiwala Mulungu amene anawapulumutsa,
    amene anachita zinthu zazikulu mu Igupto,
22 zozizwitsa mʼdziko la Hamu
    ndi machitidwe ake woopsa pa Nyanja Yofiira.
23 Choncho Iye anawawuza kuti adzawawononga,
    pakanapanda Mose, mtumiki wake wosankhidwa,
kuyima pamaso pake,
    ndi kuletsa mkwiyo wake kuti usawawononge.

24 Motero iwo ananyoza dziko lokoma;
    sanakhulupirire malonjezo ake.
25 Anangʼungʼudza mʼmatenti mwawo
    ndipo sanamvere Yehova.
26 Kotero Iye analumbira atakweza dzanja lake,
    kuti adzachititsa kuti iwowo afere mʼchipululu,
27 kuchititsa kuti zidzukulu zawo zifere pakati pa anthu a mitundu ina
    ndi kuwabalalitsa mʼdziko lonse.

28 Iwo anayamba kupembedza Baala-Peori
    ndi kudya nsembe zoperekedwa kwa milungu yopanda moyo;
29 anaputa mkwiyo wa Yehova pa machitidwe awo oyipa,
    ndipo mliri unabuka pakati pawo.
30 Koma Finehasi anayimirira ndi kulowererapo,
    ndipo mliri unaleka.
31 Chimenechi ndicho chinayesedwa chilungamo chake,
    kwa mibado yosatha imene ikubwera.

32 Pa madzi a ku Meriba iwo anakwiyitsa Yehova
    ndipo mavuto anabwera kwa Mose chifukwa cha anthuwo,
33 pakuti iwowo anawukira mzimu wa Mulungu,
    ndipo pa milomo ya Mose panatuluka mawu osayenera.

34 Aisraeliwo sanawononge mitundu ya anthu
    monga momwe Yehova anawalamulira.
35 Koma anasakanizana ndi anthu a mitundu inayo
    ndi kuphunzira miyambo yawo.
36 Ndipo anapembedza mafano awo,
    amene anakhala msampha kwa iwowo.
37 Anapereka nsembe ana awo aamuna
    ndi ana awo aakazi kwa ziwanda.
38 Anakhetsa magazi a anthu osalakwa,
    magazi a ana awo aamuna ndi a ana awo aakazi,
amene anawapereka nsembe kwa mafano a ku Kanaani,
    ndipo dziko linayipitsidwa ndi magazi awo.
39 Iwo anadzidetsa okha ndi zimene anachita;
    ndi machitidwe awo amakhala ngati munthu wachigololo.

40 Tsono Yehova anakwiya ndi anthu ake
    ndipo ananyansidwa ndi cholowa chake.
41 Iye anawapereka kwa anthu a mitundu ina,
    ndipo adani awo anawalamulira.
42 Adani awo anawazunza
    ndi kuwakhazika pansi pa mphamvu yawo.
43 Iye ankawapulumutsa nthawi zambiri,
    koma iwo ankatsimikiza za kuwukira
    ndipo anawonongeka mʼmachimo awo.

44 Koma Iye anaona kuzunzika kwawo
    pamene anamva kulira kwawo;
45 Chifukwa cha iwo Iye anakumbukira pangano lake
    ndipo anawalezera mtima chifukwa cha kukula kwa chikondi chake.
46 Iye anachititsa kuti amene anawagwira iwo ukapolo
    awamvere chisoni.

47 Tipulumutseni Inu Yehova Mulungu wathu,
    ndipo mutisonkhanitse kuchoka kwa anthu a mitundu ina
kuti tithe kuyamika dzina lanu loyera
    ndi kunyadira mʼmatamando anu.

48 Atamandike Yehova, Mulungu wa Israeli,
    Kuyambira muyaya mpaka muyaya.
Anthu onse anene kuti, “Ameni!”

Tamandani Yehova.