Add parallel Print Page Options

Yehova Ayankhula

38 Apo Yehova anamuyankha Yobu mʼkamvuluvulu. Ndipo anati:

“Kodi uyu ndani amene akusokoneza uphungu wanga
    poyankhula mawu opanda nzeru?
Onetsa chamuna;
    ndikufunsa
    ndipo undiyankhe.

“Kodi unali kuti pamene ndinkayika maziko a dziko lapansi?
    Ndiwuze ngati ukudziwa.
Ndani amene analemba malire ake? Ndithudi iwe ukudziwa!
    Ndani amene anayeza ndi chingwe dzikoli?
Kodi maziko ake anawakumba potani,
    kapena ndani anayika mwala wake wapangodya,
pamene nyenyezi za kummawa zinkayimba pamodzi
    ndipo angelo onse a Mulungu ankafuwula mokondwa?

“Kodi ndani amene anatsekera nyanja pamene inkalengedwa,
    pamene inkachita ngati kutumphuka pansi pa dziko,
pamene ndinasandutsa mitambo kukhala chovala chake
    ndi kuyikulunga mu mdima wandiweyani,
10 pamene ndinayilembera malire ake
    ndikuyikira zitseko ndi mipiringidzo yake.
11 Pamene ndinati, ‘Ufike mpaka apa ndipo usapitirire
    apa ndiye pamene mafunde ako amphamvuwo azilekezera?’

12 “Kodi chibadwire chako unalamulapo dzuwa kuti lituluke mmawa,
    kapena kuti mʼbandakucha ukhalepo pa nthawi yake,
13 kuti kuwalako kuwunikire dziko lonse lapansi
    ndi kuthamangitsa anthu oyipa?
14 Chifukwa cha kuwala kwa usana mapiri ndi zigwa zimaonekera bwino ngati zilembo za chidindo pa mtapo;
    zimaonekera bwino ngati makwinya a chovala.
15 Kuwala kwa dzuwako sikuwafikira anthu oyipa,
    ndipo dzanja lawo silingathe kuchita kanthu.

16 “Kodi unayendapo pansi penipeni pa nyanja
    kapena pa magwero ake ozama?
17 Kodi anakuonetsapo zipata za imfa?
    Kodi unaonako ku dziko la anthu akufa kumene kuli mdima wandiweyani?
18 Kodi kukula kwa dziko lapansi umakudziwa?
    Undiwuze ngati ukuzidziwa zonsezi.

19 “Kodi njira yopita kumene kumakhala kuwala ili kuti?
    Nanga mdima umakhala kuti?
20 Kodi iwe ungathe kuziperekeza kwawoko zimenezi?
    Kodi ukuyidziwa njira yopita kwawoko?
21 Ndithu, iwe ukuyidziwa, poti paja nthawi imeneyo nʼkuti utabadwa kale!
    Wakhala ndi moyo zaka zambiridi!

22 “Kodi unalowamo mʼnyumba zosungira chisanu chowundana
    kapena unayionapo nyumba yosungira matalala,
23 zimene ndazisungira nthawi ya mavuto
    ndi nthawi yomenyana ndi ya nkhondo?
24 Kodi umadziwa njira ya kumene kumachokera chingʼaningʼani
    kapena njira ya kumene kumachokera mphepo ya kummawa imene ili pa dziko lonse lapansi?
25 Kodi ndani amene amakonza ngalande za mvula,
    nanga ndani anakonza njira yoyendamo mphenzi,
26 kuthirira madzi dziko limene sikukhala munthu,
    chipululu chopandamo munthu,
27 kukhutitsa nthaka yowuma yagwaa
    ndi kumeretsamo udzu?
28 Kodi mvula ili ndi abambo ake?
    Nanga madzi a mame anawabereka ndani?
29 Kodi madzi owundana anawabereka ndani?
    Ndani amene anabereka chisanu chochokera kumwamba
30 pamene madzi amawuma gwaa ngati mwala,
    pamene madzi a pa nyanja amazizira, nalimba kuti gwaa?

31 “Kodi iwe ungayimitse kuyenda kwa nyenyezi?
    Kodi ungathe kuletsa kuyenda kwa nsangwe ndi akamwiniatsatana?
32 Kodi ungathe kuwongolera nyenyezi pa nyengo yake
    kapena kutsogolera nyenyezi yayikulu ya chimbalangondo pamodzi ndi ana ake?
33 Kodi malamulo a mlengalenga umawadziwa?
    Kodi ungathe kukhazikitsa ulamuliro wa Mulungu pa dziko lapansi?

34 “Kodi iwe ungathe kulamula mitambo
    kuti igwetse mvula ya chigumula?
35 Kodi ungathe kutumiza zingʼaningʼani kuti zingʼanime?
    Kodi zimabwera pamaso pako ndi kuti, ‘Tili pano?’
36 Kodi ndani anayika nzeru mu mtima,
    ndani analonga mʼmaganizo nzeru zomvetsa zinthu?
37 Wanzeru ndani amene angathe kuwerenga mitambo?
    Ndani angathe kupendeketsa mitsuko ya madzi akuthambo
38 pamene fumbi limasanduka matope,
    ndipo matopewo amawumbika?

39 “Kodi ndani amawusakira chakudya mkango waukazi
    ndi kukhutitsa misona ya mikango
40 pamene ili khale mʼmapanga mwawo
    kapena pamene ikubisala pa tchire?
41 Kodi amamupatsa khwangwala chakudya chake ndani
    pamene ana ake akulirira kwa Mulungu
    ndi kumayendayenda chifukwa chosowa zakudya?