Add parallel Print Page Options

Mawu a Elihu

32 Tsono anthu atatuwa analeka kumuyankha Yobu, chifukwa chakuti iyeyo ankadziona kuti ndi wolungama. Koma Elihu, mwana wa Barakeli, wa fuko la Buzi, wa banja la Ramu, anapsera mtima kwambiri Yobu chifukwa choti Yobuyo anakana kuvomera kuti anachimwa ndi kuti Mulungu anakhoza pomulanga. Anapseranso mtima abwenzi ake atatu aja chifukwa sanapeze njira yomutsutsira Yobu, ngakhale iwo anamupeza kuti anali wolakwa. Tsono Elihu anadikira kuti ayankhule ndi Yobu chifukwa choti abwenziwo anali akuluakulu kupambana iyeyo. Koma Elihu ataona kuti anthu atatuwo analibe mawu oti ayankhulenso, iye anapsa mtima.

Choncho Elihu mwana wa Barakeli wa fuko la Buzi anati:

“Ine ndine wamngʼono,
    inuyo ndinu akuluakulu,
nʼchifukwa chake ndimaopa,
    ndimachita mantha kuti ndikuwuzeni zimene ndimadziwa.
Ndimaganiza kuti, ‘Ayambe ndi akuluakulu kuyankhula;
    anthu amvulazakale ndiwo amaphunzitsa nzeru.’
Koma mzimu wa Mulungu mwa munthu,
    mpweya wa Wamphamvuzonse, ndi umene umapereka nzeru zomvetsa zinthu.
Si okalamba amene ali ndi nzeru,
    si amvulazakale okha amene ali ndi nzeru zomvetsa zinthu zimene zili zoyenera.

10 “Nʼchifukwa chake ndikuti, ‘Mvereni;
    inenso ndikukuwuzani zimene ndikuzidziwa.’
11 Ndadikira nthawi yonseyi,
    ndimamvetsera mwachidwi zimene mumayankhula,
pamene mumafunafuna mawu oti muyankhule,
12     ineyo ndinakumvetseranidi.
Koma palibe ndi mmodzi yemwe wa inu amene anatsutsa Yobu;
    palibe aliyense wa inu amene anamuyankha mawu ake.
13 Musanene kuti, ‘Ife tapeza nzeru;
    Mulungu ndiye amutsutse, osati munthu.’
14 Koma Yobu sanayankhule motsutsana ndi ine,
    ndipo ine sindimuyankha monga mmene inu mwamuyankhira.

15 “Iwo asokonezeka ndipo alibe choti ayankhulenso;
    mawu awathera.
16 Kodi ine ndidikire chifukwa iwo sakuyankhula tsopano,
    pakuti angoyima phee wopanda yankho?
17 Inenso ndiyankhulapo tsopano;
    nanenso ndinena zimene ndikudziwa.
18 Pakuti ndili nawo mawu ambiri,
    ndipo mtima wanga ukundikakamiza;
19 mʼkati mwanga ndili ngati botolo lodzaza ndi vinyo,
    ngati matumba a vinyo watsopano amene ali pafupi kuphulika.
20 Ndiyenera kuyankhula kuti mtima utsike;
    ndiyenera kutsekula pakamwa panga ndi kuyankha.
21 Sindidzakondera munthu wina aliyense,
    kapena kuyankhula zoshashalika,
22 pakuti ndikanakhala wa luso loyankhula moshashalika,
    Mlengi wanga akanandilanga msanga.”