Add parallel Print Page Options

Za Kulangidwa kwa Igupto

19 Uthenga onena za Igupto:

Taonani, Yehova wakwera pa mtambo waliwiro,
    ndipo akupita ku Igupto.
Mafano a ku Igupto akunjenjemera pamaso pake,
    ndipo mitima ya Aigupto yachokamo ndi mantha.

“Ine ndidzadzutsa Aigupto kuti amenyane okhaokha;
    mʼbale adzamenyana ndi mʼbale wake,
    mnansi ndi mnansi wake,
    mzinda ndi mzinda unzake,
    ndiponso ufumu ndi ufumu unzake.
Aigupto adzataya mtima
    popeza ndidzalepheretsa zolinga zawo;
adzapempha nzeru kwa mafano awo ndiponso kwa woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa,
    kwa amawula ndi kwa oyankhula ndi mizimu.
Ndidzawapereka Aigupto
    kwa olamulira ankhanza,
ndipo mfumu yoopsa idzawalamulira,”
    akutero Ambuye Yehova Wamphamvuzonse.

Madzi a mu mtsinje wa Nailo adzaphwa,
    ndipo mʼmbali mwa mtsinje mudzangʼaluka ndi kuwuma.
Ngalande zake zidzanunkha;
    ndipo mitsinje ya Igupto idzayamba kuchepa ndi kuwuma.
Bango ndi dulu zidzafota,
    ndiponso zomera za mʼmphepete mwa Nailo
    ndi ku mathiriro a mtsinjewo.
Zonse zodzalidwa mʼmbali mwa Nailo
    zidzawuma, zidzawuluzika ndipo sizidzaonekanso.
Asodzi adzabuwula ndi kudandaula,
    onse amene amaponya mbedza mu Nailo;
onse amene amaponya makoka mʼmadzi
    adzalira.
Amene amagwira ntchito yopota thonje adzataya mtima,
    anthu oluka nsalu zofewa zabafuta adzataya chiyembekezo.
10 Akatswiri opanga nsalu adzangoti kakasi,
    ndipo anthu onse ogwira ntchito yolipidwa adzatheratu mphamvu.

11 Akuluakulu a ku Zowani ndi zitsiru;
    aphungu a nzeru a Farao amalangiza zopusa.
Kodi mungathe kunena bwanji kwa Farao kuti,
    “Ine ndine mmodzi mwa anthu anzeru,
    wophunzira wa mafumu akale?”

12 Iwe Farao, anthu ako anzeru ali kuti?
    Abweretu kuti akuwuze ndi kukudziwitsa
zimene Yehova Wamphamvuzonse
    wakonza kuchitira dziko la Igupto.
13 Akuluakulu a ku Zowani asanduka zitsiru,
    atsogoleri a ku Mefisi anamizidwa;
atsogoleri a dziko la Igupto
    asocheretsa anthu a dzikolo.
14 Yehova wasocheretsa
    anthu a ku Igupto.
Iwo akuchita kudzandira pa zonse zimene akuchita,
    ngati chidakwa choterereka pa masanzi ake.
15 Palibe chimene munthu wa mu Igupto angachite,
    mtsogoleri kapena wotsatira, nthambi ya kanjedza kapena bango.

16 Tsiku limenelo Aigupto adzakhala ngati amayi. Adzanjenjemera ndi kuchita mantha akadzaona Yehova Wamphamvuzonse, atakweza dzanja lake kufuna kuwalanga. 17 Ndipo dziko la Yuda lidzaopsa dziko la Aigupto. Aliyense amene adzamve dzina la Yuda adzaopsedwa chifukwa cha zimene Yehova Wamphamvuzonse wakonzekera kuchitira dziko la Igupto.

18 Tsiku limenelo ku dziko la Igupto kudzakhala mizinda isanu yoyankhula chiyankhulo cha Akanaani, ndipo anthu ake adzalumbira kwa Yehova Wamphamvuzonse kuti adzamutumikira. Umodzi mwa mizindayo udzatchedwa Mzinda Wachilungamo.

19 Tsiku limenelo mʼkati mwa dziko la Igupto mudzakhala guwa lansembe la Yehova, ndipo mʼmalire mwake adzayikira Yehova mwala wachikumbutso. 20 Zimenezo zidzakhala umboni wozindikiritsa kuti Yehova Wamphamvuzonse alimo mʼdziko la Igupto. Pamene Aigupto adzalirira Yehova chifukwa cha owapondereza, Iye adzawatumizira mpulumutsi ndi mtetezi ndipo adzawalanditsa. 21 Kotero Yehova adzadziulula yekha kwa Aigupto, ndipo tsiku limenelo adzadziwa Yehova. Adzapembedza Yehova popereka nsembe ndi popereka zopereka zachakudya; Adzalumbira kwa Yehova ndipo adzachita zimene alumbirazo. 22 Yehova adzakantha Aigupto ndi mliri. Iye adzawakanthadi ndipo kenaka adzawachiritsa. Aigupto adzatembenukira kwa Yehova ndipo Iye adzamva madandawulo awo ndi kuwachiritsa.

23 Tsiku limenelo kudzakhala msewu waukulu wochoka ku Igupto kupita ku Asiriya. Aasiriya adzapita ku Igupto ndi Aigupto ku Asiriya. Aigupto ndi Aasiriya adzapembedza pamodzi. 24 Tsiku limenelo Israeli adzakhala pamodzi ndi Igupto ndi Asiriya, mayiko atatuwa adzakhala dalitso pa dziko lapansi. 25 Yehova Wamphamvuzonse adzawadalitsa, ndi mawu awa, “Adalitsike anthu anga Aigupto, Aasiriya, ntchito ya manja anga, ndi Aisraeli osankhidwa anga.”