Add parallel Print Page Options

Ku Nyumba ya Wowumba Mbiya

18 Yehova anawuza Yeremiya kuti, “Pita ku nyumba ya munthu wowumba mbiya, ndipo kumeneko ndikakuwuza mawu anga.” Choncho ndinatsikira ku nyumba ya wowumba mbiya, ndipo ndinamuona akuwumba mbiya pa mkombero. Tsono amati ngati mbiya imene waumba ikhala yosawumbika bwino ankayiphwanya nʼkuwumbanso ina monga mmene afunira ndi dothi lake lomwe lija.

Kenaka Yehova anandiwuza kuti, “Inu Aisraeli, kodi Ine sindingathe kuchita nanu monga amachitira wowumba mbiya?” akutero Yehova. “Inu muli mʼmanja mwanga ngati mtapo mʼmanja mwa wowumba mbiya. Ngati nditalengeza kuti mtundu wina wa anthu kapena ufumu wina ndiwuzula, kuwugwetsa ndi kuwuwononga, ndipo ngati mtundu wa anthu umene ndawuchenjezawo ulapa zoyipa zawo, ndiye kuti Ine ndidzaleka ndipo sindidzabweretsa pa anthuwo mavuto amene ndinakonzekera kuwachitira. Ndipo ngati ndilengeza kuti ndikufuna kumanga ndi kukhazikitsa mtundu wa anthu kapena ufumu. 10 Koma mtunduwo ukachita choyipa pamaso panga nʼkusandimvera, ndiye kuti sindidzawuchitiranso zabwino zimene ndimafuna ndiwuchitire.

11 “Ndipo tsopano kawawuze anthu a ku Yuda ndi amene akukhala mu Yerusalemu kuti, ‘Yehova akuti, Taonani! Ndikukukonzerani mavuto, ndi kuganizira zoti ndikulangeni. Kotero siyani makhalidwe anu oyipa aliyense wa inu, ndipo mukonzenso makhalidwe anu ndi zochita zanu.’ 12 Koma iwo adzayankha kuti, ‘Zimenezo nʼzosathandiza. Ife tidzapitiriza kuchita zomwe takonzekera; aliyense wa ife adzatsatira zoyipa za mtima wake wokanika.’ ”

13 Yehova akuti,

“Uwafunse anthu a mitundu ina kuti:
    Kodi ndani anamvapo zinthu zofanana ndi zimenezi?
Israeli amene anali ngati namwali wanga wachita
    chinthu choopsa kwambiri.
14 Kodi chisanu chimatha pa matanthwe
    otsetsereka a phiri la Lebanoni?
Kodi madzi ozizira amitsinje ochokera
    ku phiri la Lebanoni adzamphwa?
15 Komatu anthu anga andiyiwala;
    akufukiza lubani kwa mafano achabechabe.
Amapunthwa mʼnjira
    zawo zakale.
Amayenda mʼnjira zachidule
    ndi kusiya njira zabwino.
16 Dziko lawo amalisandutsa chipululu,
    chinthu chochititsa manyazi nthawi zonse;
onse odutsapo adzadabwa kwambiri
    ndipo adzapukusa mitu yawo.
17 Ngati mphepo yochokera kummawa,
    ndidzawabalalitsa pamaso pa adani awo;
ndidzawafulatira osawathandiza
    pa tsiku la mavuto awo.”

18 Anthuwo anati, “Tiyeni, tipangane zoti timuchitire Yeremiya; pakuti ansembe otiphunzitsa malamulo tidzakhala nawobe. Anthu anzeru otilangiza tidzakhala nawo, ndiponso aneneri otilalikira mawu. Choncho tiyeni timupezere chifukwa ndipo tisamvere chilichonse chimene akunena.”

19 Ndipo ndinapemphera kwa Yehova kuti, “Inu Yehova, ndimvereni;
    imvani zimene adani anga akunena za ine!
20 Kodi chinthu choyipa nʼkukhala dipo la chinthu chabwino?
    Komabe iwo andikumbira dzenje.
Kumbukirani kuti ndinadzayima pamaso panu
    kudzawapempherera
    kuti muwachotsere mkwiyo wanu.
21 Choncho langani ana awo ndi njala;
    aperekeni kuti aphedwe ndi lupanga.
Akazi awo asanduke opanda ana ndi amasiye;
    amuna awo aphedwe ndi mliri,
    anyamata awo aphedwe ndi lupanga ku nkhondo.
22 Kulira kumveke kuchokera mʼnyumba zawo
    mutawatumizira gulu lankhondo mwadzidzidzi kuti liwakanthe.
Iwo andikumbira dzenje kuti ndigweremo
    ndipo atchera msampha mapazi anga.
23 Koma Inu Yehova, mukudziwa
    ziwembu zawo zonse zofuna kundipha.
Musawakhululukire zolakwa zawo
    kapena kufafaniza machimo awo pamaso panu.
Agonjetsedwe pamaso panu;
    muwalange muli wokwiya.”