Add parallel Print Page Options

Yeremiya Agula Munda

32 Yehova anayankhula ndi Yeremiya mʼchaka chakhumi cha Zedekiya mfumu ya Yuda, chimene chinalinso chaka cha 18 cha ulamuliro wa Nebukadinezara. Pa nthawi imeneyi nʼkuti ankhondo a mfumu ya ku Babuloni atazinga Yerusalemu, ndipo mneneri Yeremiya ndiye anamutsekera mʼbwalo la alonda mʼnyumba yaufumu ya ku Yuda.

Tsono Zedekiya mfumu ya Yuda nʼkuti itamutsekera mʼmenemo, ndipo inati, “Nʼchifukwa chiyani ukulosera motero? Iwe ukunena kuti, ‘Yehova akuti: Ndidzapereka mzinda uno kwa mfumu ya ku Babuloni, ndipo idzawulanda. Zedekiya mfumu ya Yuda sidzapulumuka mʼmanja mwa Ababuloni, koma idzaperekedwa kwa mfumu ya ku Babuloni. Adzayankhula naye ndi kuonana naye maso ndi maso. Zedekiya adzatengedwa kupita naye ku Babuloni, kumene adzakhale mpaka nditamukhawulitsa, akutero Yehova. Ngakhale iye adzamenyane ndi Babuloni, koma sadzapambana.’ ”

Yeremiya anati, “Yehova wandiwuza kuti: Taonani, Hanameli mwana wa Salumu, amalume ako akubwera ndipo adzakuwuza kuti, ‘Gula munda wanga wa ku Anatoti, chifukwa iwe ndiwe mʼbale wanga ndipo ndiwe woyenera kuwuwombola.’ ”

Ndipo monga momwe Yehova ananenera, Hanameli, msuweni wanga anabweradi ku bwalo la alonda ndipo anati, “Gula munda wanga wa ku Anatoti mʼdziko la Benjamini. Popeza ndiwe woyenera kuwugula ndi kukhala wako, gula munda umenewu kuti ukhale wako.”

“Ine ndinadziwa kuti amenewa anali mawu a Yehova aja; choncho ndinagula munda wa ku Anatoti kwa Hanameli msuweni wanga, ndipo ndinamupatsa masekeli asiliva 17. 10 Ndinasayina panganolo ndikulimata pamaso pa mboni, kenaka ndinayeza ndalama zasilivazo pa sikelo.” 11 Pambuyo pake ndinatenga makalata anga a pangano, imodzi yomatidwa mʼmene munali malamulo onse a panganolo ndi ina yosamatidwa. 12 Ndinapereka makalatawo kwa Baruki mwana wa Neriya, mdzukulu wa Maseya pamaso pa Hanameli msuweni wanga, pamaso pa mboni zimene zinasayina panganoli ndiponso pamaso pa Ayuda onse okhala mʼbwalo la alonda.

13 “Ndinamulangiza Baruki pamaso pa onsewo kuti, 14 ‘Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti: Tenga makalata awa a umboni wapangano, iyi yokhala ndi chizindikiro ndi yopanda chizindikiro, uwasunge mʼmbiya kuti akhale nthawi yayitali. 15 Pakuti Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti: Anthu adzagulanso nyumba, minda ndi mitengo yamphesa mʼdziko lino.’ ”

16 Nditamupatsa makalata a panganowa Baruki mwana wa Neriya, ndinapemphera kwa Yehova:

17 “Aa, inu Ambuye Yehova, munalenga dziko lakumwamba ndi dziko lapansi. Munazilenga ndi dzanja lanu lamphamvu ndipo palibe chokulakani. 18 Mumaonetsa chikondi chanu kwa anthu osawerengeka koma mumalanga ana chifukwa cha machimo a makolo awo. Inu ndinu Mulungu Wamkulu ndi Wamphamvu. Dzina lanu ndinu Yehova Wamphamvuzonse. 19 Zolinga zanu ndi zazikulu ndipo zochita zanu ndi zamphamvu. Maso anu amaona zonse zimene anthu amachita. Mumapereka mphotho kwa munthu aliyense molingana ndi makhalidwe ake ndi ntchito zake. 20 Inu munachita zizindikiro zozizwitsa ku Igupto, ndipo mwakhala mukuzichita mpaka lero, pakati pa Aisraeli ndiponso pakati pa anthu onse. Choncho mwadzitchukitsa mpaka lero lino. 21 Munatulutsa Aisraeli mʼdziko la Igupto ndi dzanja lanu lamphamvu pochita zizindikiro zozizwitsa ndi zodabwitsa zimene zinaopseza adani anu. 22 Munawapatsa dziko lino limene munalonjeza mwalumbiro kulipereka kwa makolo awo, dziko loyenda mkaka ndi uchi. 23 Iwo analowa nʼkulitenga kukhala lawo, koma sanamvere Inu kapena kutsatira lamulo lanu; ndipo sanachite zomwe munawalamula. Choncho inu mwawagwetsera masautso onsewa.”

24 “Onani momwe adani azingira ndi mitumbira yankhondo mzindawu kuti awulande ndipo akuwuthira nkhondo. Chifukwa cha lupanga, njala ndi mliri. Mzindawu udzaperekedwa kwa Ababuloni anthu atafowoka ndi nkhondo, njala ndi mliri. Zimene munkanena zija zachitikadi monga mukuzionera tsopano. 25 Ngakhale mzindawu udzaperekedwa kwa Ababuloni, komabe Inu Ambuye Yehova, munandiwuza kuti, ‘Gula munda ndi siliva ndipo upereke ndalamazo pali mboni.’ ”

26 Tsono Yehova anawuza Yeremiya kuti, 27 “Taonani, Ine ndine Yehova, Mulungu wa anthu onse. Kodi chilipo chinthu choti Ine nʼkundikanika? 28 Nʼchifukwa chake ine Yehova ndikuti: Ndidzawupereka mzinda uno kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni, amene adzawulanda. 29 Ndipo Ababuloni amene akuwuthira nkhondo mzinda uno adzalowa ndi kuwutentha; adzatentha ndi kugwetsa nyumba zimene pa denga pake anthu ankandipsetsa mtima pofukiza lubani kwa Baala ndi popereka chopereka cha chakumwa kwa milungu ina.

30 “Aisraeli ndi Ayuda akhala akuchita zoyipa zokhazokha pamaso panga kuyambira ubwana wawo. Kunena zoona Aisraeli akumandikwiyitsa ndi ntchito zawo zoyipa, akutero Yehova. 31 Kuyambira tsiku limene mzindawu unamangidwa mpaka lero, wakhala ukuwutsa mkwiyo wanga ndi ukali wanga. Nʼchifukwa chake ndiyenera kuwuchotsa pamaso panga. 32 Aisraeli ndi Ayuda, anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu, mafumu awo, nduna zawo, ansembe ndi aneneri awo anandikwiyitsa ndi ntchito zawo zoyipa. 33 Anandifulatira ndipo ngakhale ndinakhala ndikuwaphunzitsa kawirikawiri, sanamve kapena kuphunzirapo kanthu. 34 Iwo anayika mafano awo onyansa mʼnyumba imene imadziwika ndi dzina langa ndipo anayipitsa. 35 Anamanga malo opembedzerapo Baala mʼChigwa cha Hinomu kuti aziperekapo ana awo aamuna ndi aakazi ngati nsembe kwa Moleki. Ine sindinawalamulire kutero, ndipo sindinaganizepo nʼkomwe kuti iwo angachite chinthu chonyansa chotero, ndi kuchimwitsa anthu a ku Yuda.

36 “Anthu ponena za mzindawu akuti udzaperekedwa kwa mfumu ya ku Babuloni mwa nkhondo, njala ndi mliri, koma Yehova Mulungu wa Israeli akuti, 37 Ine ndidzawasonkhanitsadi anthuwa kuchokera ku mayiko onse kumene ndinawapirikitsira ndili wokwiya ndi waukali kwambiri. Ndidzabwera nawo ku malo ano ndipo ndidzawalola kukhala mwamtendere. 38 Iwo adzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wawo. 39 Ndidzawapatsa mtima umodzi ndi khalidwe limodzi kotero kuti azidzandiopa nthawi zonse ndipo iwo pamodzi ndi zidzukulu zawo zinthu zidzawayendera bwino. 40 Ndidzachita nawo pangano losatha: sindidzaleka kuwachitira zabwino, ndipo ndidzawapatsa mtima woti azidzandiopa, kuti asadzandisiyenso. 41 Ndidzakondwera powachitira zabwino, ndipo ndidzawakhazikitsa ndithu mʼdziko lino ndi mtima wanga wonse ndi moyo wanga wonse.

42 “Yehova akuti: Monga momwe ndinagwetsera masautso aakulu onsewa pa anthuwa, momwemonso ndidzawapatsa zinthu zonse zabwino zimene ndinawalonjeza. 43 Adzagulanso minda mʼdziko muno, limene inu mukuti, ‘Ndi dziko losiyidwa, lopanda anthu kapena nyama, pakuti linaperekedwa kwa Ababuloni.’ 44 Adzagula minda ndi ndalama zasiliva, ndipo achita pangano, ndi kumata pamaso pa mboni. Izi zidzachitika mʼdziko la Benjamini, ku malo ozungulira Yerusalemu, mʼmizinda ya Yuda, mʼmizinda ya ku mapiri, mʼmizinda ya kuchigwa ndi yakummwera ku Negevi. Zoona, ndidzabwezera ufulu wawo, akutero Yehova.”

Jeremiah Buys a Field

32 This is the word that came to Jeremiah from the Lord in the tenth(A) year of Zedekiah king of Judah, which was the eighteenth(B) year of Nebuchadnezzar. The army of the king of Babylon was then besieging(C) Jerusalem, and Jeremiah the prophet was confined(D) in the courtyard of the guard(E) in the royal palace of Judah.

Now Zedekiah king of Judah had imprisoned him there, saying, “Why do you prophesy(F) as you do? You say, ‘This is what the Lord says: I am about to give this city into the hands of the king of Babylon, and he will capture(G) it. Zedekiah(H) king of Judah will not escape(I) the Babylonians[a](J) but will certainly be given into the hands of the king of Babylon, and will speak with him face to face and see him with his own eyes. He will take(K) Zedekiah to Babylon, where he will remain until I deal with him,(L) declares the Lord. If you fight against the Babylonians, you will not succeed.’”(M)

Jeremiah said, “The word of the Lord came to me: Hanamel son of Shallum your uncle is going to come to you and say, ‘Buy my field at Anathoth,(N) because as nearest relative it is your right and duty(O) to buy it.’

“Then, just as the Lord had said, my cousin Hanamel came to me in the courtyard of the guard and said, ‘Buy my field(P) at Anathoth in the territory of Benjamin. Since it is your right to redeem it and possess it, buy it for yourself.’

“I knew that this was the word of the Lord; so I bought the field(Q) at Anathoth from my cousin Hanamel and weighed out for him seventeen shekels[b] of silver.(R) 10 I signed and sealed the deed,(S) had it witnessed,(T) and weighed out the silver on the scales. 11 I took the deed of purchase—the sealed copy containing the terms and conditions, as well as the unsealed copy— 12 and I gave this deed to Baruch(U) son of Neriah,(V) the son of Mahseiah, in the presence of my cousin Hanamel and of the witnesses who had signed the deed and of all the Jews sitting in the courtyard of the guard.

13 “In their presence I gave Baruch these instructions: 14 ‘This is what the Lord Almighty, the God of Israel, says: Take these documents, both the sealed(W) and unsealed copies of the deed of purchase, and put them in a clay jar so they will last a long time. 15 For this is what the Lord Almighty, the God of Israel, says: Houses, fields and vineyards will again be bought in this land.’(X)

16 “After I had given the deed of purchase to Baruch(Y) son of Neriah, I prayed to the Lord:

17 “Ah, Sovereign Lord,(Z) you have made the heavens and the earth(AA) by your great power and outstretched arm.(AB) Nothing is too hard(AC) for you. 18 You show love(AD) to thousands but bring the punishment for the parents’ sins into the laps(AE) of their children(AF) after them. Great and mighty God,(AG) whose name is the Lord Almighty,(AH) 19 great are your purposes and mighty are your deeds.(AI) Your eyes are open to the ways of all mankind;(AJ) you reward each person according to their conduct and as their deeds deserve.(AK) 20 You performed signs and wonders(AL) in Egypt(AM) and have continued them to this day, in Israel and among all mankind, and have gained the renown(AN) that is still yours. 21 You brought your people Israel out of Egypt with signs and wonders, by a mighty hand(AO) and an outstretched arm(AP) and with great terror.(AQ) 22 You gave them this land you had sworn to give their ancestors, a land flowing with milk and honey.(AR) 23 They came in and took possession(AS) of it, but they did not obey you or follow your law;(AT) they did not do what you commanded them to do. So you brought all this disaster(AU) on them.

24 “See how the siege ramps(AV) are built up to take the city. Because of the sword, famine and plague,(AW) the city will be given into the hands of the Babylonians who are attacking it. What you said(AX) has happened,(AY) as you now see. 25 And though the city will be given into the hands of the Babylonians, you, Sovereign Lord, say to me, ‘Buy the field(AZ) with silver and have the transaction witnessed.(BA)’”

26 Then the word of the Lord came to Jeremiah: 27 “I am the Lord, the God of all mankind.(BB) Is anything too hard for me?(BC) 28 Therefore this is what the Lord says: I am about to give this city into the hands of the Babylonians and to Nebuchadnezzar(BD) king of Babylon, who will capture it.(BE) 29 The Babylonians who are attacking this city will come in and set it on fire; they will burn it down,(BF) along with the houses(BG) where the people aroused my anger by burning incense on the roofs to Baal and by pouring out drink offerings(BH) to other gods.(BI)

30 “The people of Israel and Judah have done nothing but evil in my sight from their youth;(BJ) indeed, the people of Israel have done nothing but arouse my anger(BK) with what their hands have made,(BL) declares the Lord. 31 From the day it was built until now, this city(BM) has so aroused my anger and wrath that I must remove(BN) it from my sight. 32 The people of Israel and Judah have provoked(BO) me by all the evil(BP) they have done—they, their kings and officials,(BQ) their priests and prophets, the people of Judah and those living in Jerusalem. 33 They turned their backs(BR) to me and not their faces; though I taught(BS) them again and again, they would not listen or respond to discipline.(BT) 34 They set up their vile images(BU) in the house that bears my Name(BV) and defiled(BW) it. 35 They built high places for Baal in the Valley of Ben Hinnom(BX) to sacrifice their sons and daughters to Molek,(BY) though I never commanded—nor did it enter my mind(BZ)—that they should do such a detestable(CA) thing and so make Judah sin.(CB)

36 “You are saying about this city, ‘By the sword, famine and plague(CC) it will be given into the hands of the king of Babylon’; but this is what the Lord, the God of Israel, says: 37 I will surely gather(CD) them from all the lands where I banish them in my furious anger(CE) and great wrath; I will bring them back to this place and let them live in safety.(CF) 38 They will be my people,(CG) and I will be their God. 39 I will give them singleness(CH) of heart and action, so that they will always fear(CI) me and that all will then go well for them and for their children after them. 40 I will make an everlasting covenant(CJ) with them: I will never stop doing good to them, and I will inspire(CK) them to fear me, so that they will never turn away from me.(CL) 41 I will rejoice(CM) in doing them good(CN) and will assuredly plant(CO) them in this land with all my heart and soul.(CP)

42 “This is what the Lord says: As I have brought all this great calamity(CQ) on this people, so I will give them all the prosperity I have promised(CR) them. 43 Once more fields will be bought(CS) in this land of which you say, ‘It is a desolate(CT) waste, without people or animals, for it has been given into the hands of the Babylonians.’ 44 Fields will be bought for silver, and deeds(CU) will be signed, sealed and witnessed(CV) in the territory of Benjamin, in the villages around Jerusalem, in the towns of Judah and in the towns of the hill country, of the western foothills and of the Negev,(CW) because I will restore(CX) their fortunes,[c] declares the Lord.”

Footnotes

  1. Jeremiah 32:4 Or Chaldeans; also in verses 5, 24, 25, 28, 29 and 43
  2. Jeremiah 32:9 That is, about 7 ounces or about 200 grams
  3. Jeremiah 32:44 Or will bring them back from captivity