Add parallel Print Page Options

Bowazi Akwatira Rute

Nthawi yomweyo Bowazi anapita ku chipata cha mzinda ndi kukhala pansi kumeneko pabwalo losonkhanira. Tsono anangoona wachibale woyenera kulowa chokolo uja akufika. Ndipo Bowazi anati, “Patukirani kuno, bwenzi langa. Mubwere mudzakhale apa.” Choncho anapatuka nakakhala pansi.

Bowazi anayitananso akuluakulu khumi a mu mzindamo nati, “Dzakhaleni pansi apa,” ndipo anadzakhala pansi.

Kenaka anamuwuza oyenera kulowa chokolo uja kuti, “Naomi amene wabwera kuchoka ku Mowabu akugulitsa malo amene anali a malemu Elimeleki, mʼbale wathu uja. Choncho ndinaganiza zokuwuza zimenezi kuti ugule mundawu pamaso pa anthu amene ali panowa, ndi pamaso pa akuluakulu mwa abale athu. Ngati ukufuna kuwuwombola, uwombole. Koma ngati sukufuna, undiwuze kuti ndidziwe, pakuti palibe wina angawuwombole koma iweyo, ndipo pambuyo pa iwe pali ine.” Iye anati, “Ine ndidzawuwombola.”

Tsono Bowazi anati, “Tsiku limene ukagule mundawo kwa Naomi, udzatenganso Rute Mmowabu, mkazi wamasiye uja, kuti dzina la malemu lisungike pa cholowa chake.”

Pamenepo wachibaleyo anati, “Sindingathe kuwuwombola mundawu kuti ukhale wanga, kuopa kuti kutaya cholowa changa. Mugule ndinu. Ine sindingathe.”

(Kale mu Israeli zinkatere ngati munthu afuna kuwombola kanthu kapena kusinthana kanthu ndi mnzake kuti chikhale chakechake. Iye ankavula nsapato imodzi namupatsa mnzakeyo. Imeneyo ndiyo inali njira yochitira umboni mu Israeli).

Choncho wachibale uja atawuza Bowazi kuti, “Gulani ndinu mundawu.” Iye anavula nsapato yake namupatsa Bowazi.

Ndipo Bowazi anawuza akuluakuluwo ndi anthu onse aja kuti, “Nonsenu ndinu mboni lero, kuti ine ndagula kwa Naomi zonse zimene zinali za malemu Elimeleki, zonse zimene zinali za malemu Kiliyoni ndiponso za malemu Maloni. 10 Ndatenganso Rute Mmowabu uja mkazi wa malemu Maloni, kuti akhale mkazi wanga, kuti dzina la malemu Maloni lisungike pa cholowa chake, ndipo lisafafanizike pakati pa abale ake ngakhalenso mʼmudzi mwake. Nonsenu ndinu mboni lero lino.”

11 Ndipo akuluakulu aja ndi anthu onse amene anali pa chipata anati, “Ife ndife mboni, ndipo Yehova amusandutsa mkazi amene akudzalowa mʼnyumba yakoyu kuti akhale ngati Rakele ndi Leya, amene anamanga banja la Israeli. Ukhale munthu wosasowa kanthu mu Efurata ndi munthu wotchuka mu Betelehemu. 12 Ana amene Yehova adzakupatsa mwa mkaziyu adzamange banja lako kukhala la Perezi, amene Tamara anamubalira Yuda.”

Makolo a Davide

13 Choncho Bowazi anakwatira Rute. Yehova anamudalitsa nakhala ndi pakati, ndipo anabereka mwana wamwamuna.

14 Ndipo amayi osiyanasiyana anati kwa Naomi. “Alemekezeke Yehova, amene lero lino sanakusiyeni nokha wopanda wachibale. Mwanayu dzina lake likhale lotchuka mu Israeli. 15 Mwanayo adzakupatseni moyo watsopano ndi kukuthandizani pa ukalamba wanu. Inde, mpongozi wanu amene amakukondani, amenenso waonetsa kuti ali wopambana kwa inu kuposa ana aamuna asanu ndi awiri, ndiye wakubalirani mwanayu.”

16 Kenaka Naomi anatenga mwanayo namufukata ndipo anakhala mlezi.

17 Amayi achinansi ake anati, “Naomi ali ndi mwana wamwamuna.” Ndipo anamutcha dzina lake Obedi. Iye anali abambo a Yese abambo ake a Davide.

18 Izi tsono ndizo zidzukulu za Perezi:

Perezi anali abambo a Hezironi.

19 Hezironi anali abambo a Ramu,

Ramu anali abambo a Aminadabu,

20 Aminadabu abambo a Naasoni,

Naasoni anali abambo a Salimoni,

21 Salimoni abambo a Bowazi,

Bowazi abambo a Obedi.

22 Obedi anali abambo a Yese,

ndipo Yese anali abambo a Davide.

Boaz Marries Ruth

Meanwhile Boaz went up to the town gate(A) and sat down there just as the guardian-redeemer[a](B) he had mentioned(C) came along. Boaz said, “Come over here, my friend, and sit down.” So he went over and sat down.

Boaz took ten of the elders(D) of the town and said, “Sit here,” and they did so.(E) Then he said to the guardian-redeemer, “Naomi, who has come back from Moab, is selling the piece of land that belonged to our relative Elimelek.(F) I thought I should bring the matter to your attention and suggest that you buy it in the presence of these seated here and in the presence of the elders of my people. If you will redeem it, do so. But if you[b] will not, tell me, so I will know. For no one has the right to do it except you,(G) and I am next in line.”

“I will redeem it,” he said.

Then Boaz said, “On the day you buy the land from Naomi, you also acquire Ruth the Moabite,(H) the[c] dead man’s widow, in order to maintain the name of the dead with his property.”(I)

At this, the guardian-redeemer said, “Then I cannot redeem(J) it because I might endanger my own estate. You redeem it yourself. I cannot do it.”(K)

(Now in earlier times in Israel, for the redemption(L) and transfer of property to become final, one party took off his sandal(M) and gave it to the other. This was the method of legalizing transactions(N) in Israel.)(O)

So the guardian-redeemer said to Boaz, “Buy it yourself.” And he removed his sandal.(P)

Then Boaz announced to the elders and all the people, “Today you are witnesses(Q) that I have bought from Naomi all the property of Elimelek, Kilion and Mahlon. 10 I have also acquired Ruth the Moabite,(R) Mahlon’s widow, as my wife,(S) in order to maintain the name of the dead with his property, so that his name will not disappear from among his family or from his hometown.(T) Today you are witnesses!(U)

11 Then the elders and all the people at the gate(V) said, “We are witnesses.(W) May the Lord make the woman who is coming into your home like Rachel and Leah,(X) who together built up the family of Israel. May you have standing in Ephrathah(Y) and be famous in Bethlehem.(Z) 12 Through the offspring the Lord gives you by this young woman, may your family be like that of Perez,(AA) whom Tamar(AB) bore to Judah.”

Naomi Gains a Son

13 So Boaz took Ruth and she became his wife. When he made love to her, the Lord enabled her to conceive,(AC) and she gave birth to a son.(AD) 14 The women(AE) said to Naomi: “Praise be to the Lord,(AF) who this day has not left you without a guardian-redeemer.(AG) May he become famous throughout Israel! 15 He will renew your life and sustain you in your old age. For your daughter-in-law,(AH) who loves you and who is better to you than seven sons,(AI) has given him birth.”

16 Then Naomi took the child in her arms and cared for him. 17 The women living there said, “Naomi has a son!” And they named him Obed. He was the father of Jesse,(AJ) the father of David.(AK)

The Genealogy of David(AL)

18 This, then, is the family line of Perez(AM):

Perez was the father of Hezron,(AN)

19 Hezron the father of Ram,

Ram the father of Amminadab,(AO)

20 Amminadab the father of Nahshon,(AP)

Nahshon the father of Salmon,[d]

21 Salmon the father of Boaz,(AQ)

Boaz the father of Obed,

22 Obed the father of Jesse,

and Jesse the father of David.

Footnotes

  1. Ruth 4:1 The Hebrew word for guardian-redeemer is a legal term for one who has the obligation to redeem a relative in serious difficulty (see Lev. 25:25-55); also in verses 3, 6, 8 and 14.
  2. Ruth 4:4 Many Hebrew manuscripts, Septuagint, Vulgate and Syriac; most Hebrew manuscripts he
  3. Ruth 4:5 Vulgate and Syriac; Hebrew (see also Septuagint) Naomi and from Ruth the Moabite, you acquire the
  4. Ruth 4:20 A few Hebrew manuscripts, some Septuagint manuscripts and Vulgate (see also verse 21 and Septuagint of 1 Chron. 2:11); most Hebrew manuscripts Salma