Add parallel Print Page Options

Za Mnaziri

Yehova anawuza Mose kuti, “Yankhula ndi Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Ngati mwamuna kapena mkazi afuna kuchita lonjezo lapadera, lonjezo lodzipatula yekha kwa Yehova ngati Mnaziri, sayenera kumwa vinyo kapena zakumwa zosasa ndipo asamamwe chakumwa chilichonse cha mphesa. Asamamwe madzi a mphesa kapena kudya mphesa zaziwisi kapena zowuma. Pa nthawi yonse imene ali Mnaziri, asamadye chilichonse chopangidwa kuchokera ku mphesa ngakhale mbewu zake kapena makungu ake.’

“ ‘Pa nthawi yonse ya lonjezo lodzipatula yekhalo, asamete kumutu kwake ndi lumo. Akhale wopatulika mpaka nthawi yake yonse ya kudzipatula yekha kwa Yehova itatha. Alileke tsitsi la pamutu pake kuti likule.’ Pa nthawi yonse imene munthuyo wadzipatula yekha kwa Yehova asayandikire mtembo. Ngakhale abambo ake kapena amayi ake kapena mchimwene wake kaya mchemwali wake atamwalira, asadzidetse pokhudza mitembo yawo chifukwa kulumbira kwake kwa kudzipatula yekha kwa Yehova kuli pamutu pake. Munthuyo ndi wopatulika masiku onse odzipereka kwake kwa Yehova.

“Ngati munthu wina afa mwadzidzidzi pafupi naye ndi kudetsa tsitsi lake loperekedwalo, amete mutu wake pa tsiku lodziyeretsa, tsiku lachisanu ndi chiwiri. 10 Tsono pa tsiku lachisanu ndi chitatu abweretse nkhunda ziwiri kapena mawunda awiri anjiwa kwa wansembe pa khomo lolowera ku tenti ya msonkhano. 11 Wansembe apereke imodzi kuti ikhale nsembe yauchimo ndi ina nsembe yopsereza yotetezera tchimo chifukwa anachimwa popezeka pafupi ndi mtembo. Ndipo tsiku lomwelo apatulenso tsitsi la pamutu pake. 12 Adzipereke kwa Yehova pa nthawi yodzipatula ndipo abweretse nkhosa yayimuna ya chaka chimodzi ngati nsembe yopepesera. Masiku akale sawerengedwanso chifukwa anadzidetsa pa nthawi yodzipatulira kwake.

13 “Tsono ili ndi lamulo la Mnaziri pamene nthawi yodzipatula kwake yatha: Abwere naye pa khomo la tenti ya msonkhano. 14 Pamenepo apereke chopereka chake kwa Yehova: Nkhosa yayimuna ya chaka chimodzi yopanda chilema kuti ikhale nsembe yopsereza, mwana wankhosa wamkazi mmodzi wopanda chilema kuti ikhale nsembe yauchimo, ndi nkhosa imodzi yayikulu yayimuna kuti ikhale nsembe yachiyanjano, 15 ndipo abwere pamodzi ndi nsembe yachakudya ndi nsembe yachakumwa ndi dengu la buledi wopanda yisiti, makeke opangidwa ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, ndi timitanda ta buledi topakidwa mafuta.

16 “Wansembe apereke zimenezi pamaso pa Yehova ndi kuchita nsembe ya uchimo ndi nsembe yopsereza. 17 Apereke dengu la buledi wopanda yisiti ndiponso nsembe yachiyanjano kwa Yehova ya nkhosa yayimuna, pamodzi ndi chopereka cha chakudya ndi chopereka cha chakumwa.

18 “Mnaziriyo amete tsitsi limene analipereka lija pa khomo la tenti ya msonkhano. Atenge tsitsilo ndi kuliyika pa moto umene uli pansi pa nsembe yachiyanjano.

19 “Mnaziriyo atatha kumeta tsitsi analiperekalo, wansembe ayike mʼmanja mwake mwendo wa mmwamba wankhosa yayimuna umene waphikidwa ndipo atengenso keke ndi kamtanda ka buledi, zonse zopanda yisiti zomwe zili mʼdengu lija. 20 Wansembe aziweyule pamaso pa Yehova ngati nsembe yoweyula. Zimenezi ndi zopatulika ndipo ndi za wansembe pamodzi ndi chidale chimene anachiweyula ndi ntchafu yomwe anayipereka ija. Zitatha izi, Mnaziri akhoza kumwa vinyo.

21 “Ili ndi lamulo la Mnaziri yemwe walonjeza kudzipereka kwa Yehova podzipatula yekha kuphatikiza pa zomwe angathe kukwaniritsa. Ayenera kukwaniritsa lonjezo lomwe wachitalo potsata lamulo la Mnaziri.”

Kupereka Mdalitso

22 Yehova anawuza Mose kuti, 23 “Uza Aaroni ndi ana ake aamuna kuti, ‘Umu ndi mmene muzidalitsira Aisraeli. Muzinena kuti,

24 “ ‘Yehova akudalitse
    ndi kukusunga;
25 Yehova awalitse nkhope yake pa iwe,
    nakuchitira chisomo;
26 Yehova akweze nkhope yake pa iwe,
    nakupatse mtendere.’ ”

27 Choncho akadzatchula dzina langa podalitsa Aisraeli, Ine ndidzawadalitsadi.

The Nazirite

The Lord said to Moses, “Speak to the Israelites and say to them: ‘If a man or woman wants to make a special vow(A), a vow of dedication(B) to the Lord as a Nazirite,(C) they must abstain from wine(D) and other fermented drink and must not drink vinegar(E) made from wine or other fermented drink. They must not drink grape juice or eat grapes(F) or raisins. As long as they remain under their Nazirite vow, they must not eat anything that comes from the grapevine, not even the seeds or skins.

“‘During the entire period of their Nazirite vow, no razor(G) may be used on their head.(H) They must be holy until the period of their dedication to the Lord is over; they must let their hair grow long.

“‘Throughout the period of their dedication to the Lord, the Nazirite must not go near a dead body.(I) Even if their own father or mother or brother or sister dies, they must not make themselves ceremonially unclean(J) on account of them, because the symbol of their dedication to God is on their head. Throughout the period of their dedication, they are consecrated to the Lord.

“‘If someone dies suddenly in the Nazirite’s presence, thus defiling the hair that symbolizes their dedication,(K) they must shave their head on the seventh day—the day of their cleansing.(L) 10 Then on the eighth day(M) they must bring two doves or two young pigeons(N) to the priest at the entrance to the tent of meeting.(O) 11 The priest is to offer one as a sin offering[a](P) and the other as a burnt offering(Q) to make atonement(R) for the Nazirite because they sinned by being in the presence of the dead body. That same day they are to consecrate their head again. 12 They must rededicate themselves to the Lord for the same period of dedication and must bring a year-old male lamb(S) as a guilt offering.(T) The previous days do not count, because they became defiled during their period of dedication.

13 “‘Now this is the law of the Nazirite when the period of their dedication is over.(U) They are to be brought to the entrance to the tent of meeting.(V) 14 There they are to present their offerings to the Lord: a year-old male lamb without defect(W) for a burnt offering, a year-old ewe lamb without defect for a sin offering,(X) a ram(Y) without defect for a fellowship offering,(Z) 15 together with their grain offerings(AA) and drink offerings,(AB) and a basket of bread made with the finest flour and without yeast—thick loaves with olive oil mixed in, and thin loaves brushed with olive oil.(AC)

16 “‘The priest is to present all these(AD) before the Lord(AE) and make the sin offering and the burnt offering.(AF) 17 He is to present the basket of unleavened bread and is to sacrifice the ram as a fellowship offering(AG) to the Lord, together with its grain offering(AH) and drink offering.(AI)

18 “‘Then at the entrance to the tent of meeting, the Nazirite must shave off the hair that symbolizes their dedication.(AJ) They are to take the hair and put it in the fire that is under the sacrifice of the fellowship offering.

19 “‘After the Nazirite has shaved off the hair that symbolizes their dedication, the priest is to place in their hands a boiled shoulder of the ram, and one thick loaf and one thin loaf from the basket, both made without yeast.(AK) 20 The priest shall then wave these before the Lord as a wave offering;(AL) they are holy(AM) and belong to the priest, together with the breast that was waved and the thigh that was presented.(AN) After that, the Nazirite may drink wine.(AO)

21 “‘This is the law of the Nazirite(AP) who vows offerings to the Lord in accordance with their dedication, in addition to whatever else they can afford. They must fulfill the vows(AQ) they have made, according to the law of the Nazirite.’”

The Priestly Blessing

22 The Lord said to Moses, 23 “Tell Aaron and his sons, ‘This is how you are to bless(AR) the Israelites. Say to them:

24 “‘“The Lord bless you(AS)
    and keep you;(AT)
25 the Lord make his face shine on you(AU)
    and be gracious to you;(AV)
26 the Lord turn his face(AW) toward you
    and give you peace.(AX)”’

27 “So they will put my name(AY) on the Israelites, and I will bless them.”

Footnotes

  1. Numbers 6:11 Or purification offering; also in verses 14 and 16