Add parallel Print Page Options

Malire a Dziko la Kanaani

34 Yehova anawuza Mose kuti, “Lamula Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Pamene mulowa mʼdziko la Kanaani, dziko lomwe lidzaperekedwa kwa inu ngati cholowa chanu, lidzakhale ndi malire awa:

“ ‘Chigawo cha kummwera kwa dziko lanu chidzayambira ku chipululu cha Zini motsatana ndi malire a Edomu. Kummawa malire anu a kummwera adzayambira kummawa, kumathero a Nyanja ya Mchere. Malirewo adzapita kummwera ndipo adzakwera phiri la Akirabimu mpaka ku Zini. Mathero ake adzakhala kummwera kwa Kadesi-Baranea. Ndipo adzapitenso ku Hazari Adari mpaka kukafika ku Azimoni, kumene malirewo adzakhote kuchokera ku Azimoni mpaka ku khwawa la ku Igupto ndi kukathera ku Nyanja Yayikulu.

“ ‘Malire anu a ku madzulo adzakhala ku gombe la Nyanja Yayikulu. Amenewo ndiwo adzakhale malire anu a ku madzulo.

“ ‘Malire anu a kumpoto, mzere wake uyambire ku Nyanja Yayikulu mpaka ku phiri la Hori ndi kuchokera ku phiri la Hori mpaka ku Lebo Hamati. Malirewa apite ku Zedadi, ndi kupitirira mpaka ku Ziforoni ndi kukathera ku Hazari-Enani. Awa ndiwo adzakhale malire anu a kumpoto.

10 “ ‘Za malire anu a kummawa, mulembe mzere kuchokera ku Hazari-Enani mpaka kukafika ku Sefamu. 11 Malirewo adzatsikire ku Sefamu mpaka ku Ribila cha kummawa kwa Aini ndi kupitirira mpaka ku matsitso a cha kummawa kwa Nyanja ya Kinereti. 12 Tsono malirewo adzatsika motsatana ndi Yorodani ndi kukathera ku Nyanja ya Mchere.

“ ‘Limeneli lidzakhala dziko lanu ndi malire ake mbali zonse.’ ”

13 Ndipo Mose analamula Aisraeli kuti, “Limeneli ndi dziko limene mudzalilandira pochita maere kuti likhale cholowa chanu. Yehova analamula kuti liperekedwe ku mafuko asanu ndi anayi ndi theka, 14 chifukwa mabanja a fuko la Rubeni, fuko la Gadi, ndi theka la fuko la Manase analandiriratu cholowa chawo. 15 Mafuko awiriwa pamodzi ndi theka la fuko la Manase analandiriratu cholowa chawo patsidya pa mtsinje wa Yorodani ku Yeriko cha kummawa kotulukira dzuwa.”

16 Yehova anawuza Mose kuti, 17 “Awa ndi mayina a anthu amene adzakugawireni dzikoli kuti likhale cholowa chanu: wansembe Eliezara ndi Yoswa mwana wa Nuni. 18 Musankhe mtsogoleri mmodzi kuchokera ku fuko lililonse kuti athandize kugawa dzikolo. 19 Mayina awo ndi awa:

Kalebe mwana wa Yefune,

wochokera ku fuko la Yuda,

20 Semueli mwana wa Amihudi,

wochokera ku fuko la Simeoni;

21 Elidadi mwana wa Kisiloni,

wochokera ku fuko la Benjamini;

22 Buki mwana wa Yogili,

mtsogoleri wochokera ku fuko la Dani;

23 Hanieli mwana wa Efodi,

mtsogoleri wochokera ku fuko la Manase, mwana wa Yosefe;

24 Kemueli mwana wa Sifitani,

mtsogoleri wochokera ku fuko la Efereimu, mwana wa Yosefe.

25 Elizafani mwana wa Parinaki,

mtsogoleri wochokera ku fuko la Zebuloni;

26 Palitieli mwana wa Azani,

mtsogoleri wochokera ku fuko la Isakara,

27 Ahihudi mwana wa Selomi,

mtsogoleri wochokera ku fuko la Aseri;

28 Pedaheli mwana wa Amihudi,

mtsogoleri wochokera ku fuko la Nafutali.”

29 Awa ndiwo mayina a anthu amene Yehova analamula kuti agawe cholowa cha Aisraeli mʼdziko la Kanaani.

Boundaries of Canaan

34 The Lord said to Moses, “Command the Israelites and say to them: ‘When you enter Canaan,(A) the land that will be allotted to you as an inheritance(B) is to have these boundaries:(C)

“‘Your southern side will include some of the Desert of Zin(D) along the border of Edom. Your southern boundary will start in the east from the southern end of the Dead Sea,(E) cross south of Scorpion Pass,(F) continue on to Zin and go south of Kadesh Barnea.(G) Then it will go to Hazar Addar and over to Azmon,(H) where it will turn, join the Wadi of Egypt(I) and end at the Mediterranean Sea.

“‘Your western boundary will be the coast of the Mediterranean Sea.(J) This will be your boundary on the west.(K)

“‘For your northern boundary,(L) run a line from the Mediterranean Sea to Mount Hor(M) and from Mount Hor to Lebo Hamath.(N) Then the boundary will go to Zedad, continue to Ziphron and end at Hazar Enan. This will be your boundary on the north.

10 “‘For your eastern boundary,(O) run a line from Hazar Enan to Shepham. 11 The boundary will go down from Shepham to Riblah(P) on the east side of Ain(Q) and continue along the slopes east of the Sea of Galilee.[a](R) 12 Then the boundary will go down along the Jordan and end at the Dead Sea.

“‘This will be your land, with its boundaries on every side.’”

13 Moses commanded the Israelites: “Assign this land by lot(S) as an inheritance.(T) The Lord has ordered that it be given to the nine and a half tribes, 14 because the families of the tribe of Reuben, the tribe of Gad and the half-tribe of Manasseh have received their inheritance.(U) 15 These two and a half tribes have received their inheritance east of the Jordan across from Jericho, toward the sunrise.”

16 The Lord said to Moses, 17 “These are the names of the men who are to assign the land for you as an inheritance: Eleazar the priest and Joshua(V) son of Nun. 18 And appoint one leader from each tribe to help(W) assign the land.(X) 19 These are their names:(Y)

Caleb(Z) son of Jephunneh,

from the tribe of Judah;(AA)

20 Shemuel son of Ammihud,

from the tribe of Simeon;(AB)

21 Elidad son of Kislon,

from the tribe of Benjamin;(AC)

22 Bukki son of Jogli,

the leader from the tribe of Dan;

23 Hanniel son of Ephod,

the leader from the tribe of Manasseh(AD) son of Joseph;

24 Kemuel son of Shiphtan,

the leader from the tribe of Ephraim(AE) son of Joseph;

25 Elizaphan son of Parnak,

the leader from the tribe of Zebulun;(AF)

26 Paltiel son of Azzan,

the leader from the tribe of Issachar;

27 Ahihud son of Shelomi,

the leader from the tribe of Asher;(AG)

28 Pedahel son of Ammihud,

the leader from the tribe of Naphtali.”

29 These are the men the Lord commanded to assign the inheritance to the Israelites in the land of Canaan.(AH)

Footnotes

  1. Numbers 34:11 Hebrew Kinnereth