Add parallel Print Page Options

Phindu Lina la Nzeru

Mwana wanga, usayiwale malangizo anga,
    mtima wako usunge malamulo anga.
Ukatero zaka za moyo wako zidzachuluka
    ndipo udzakhala pa mtendere.

Makhalidwe ochitira ena chifundo ndi owonetsa kukhulupirika asakuchokere.
    Uwamangirire mʼkhosi mwako ngati mkanda
    ndi kuwalemba pa mtima pako.
Ukatero udzapeza kuyanja ndi mbiri yabwino
    pamaso pa Mulungu ndi anthu.

Uzikhulupirira Yehova ndi mtima wako wonse
    ndipo usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu.
Pa zochita zako zonse uvomereze kuti Mulungu alipo,
    ndipo Iye adzawongola njira zako.

Usamadzione ngati wa nzeru.
    Uziopa Yehova ndi kupewa zoyipa.
Ukatero thupi lako lidzakhala la moyo wabwino
    ndi mafupa ako adzakhala olimba.

Uzilemekeza Yehova ndi chuma chako chonse;
    zokolola zonse zoyamba kucha uzilemekeza nazonso Yehova.
10 Ukatero nkhokwe zako zidzadzaza ndi zinthu zambiri,
    ndiponso mitsuko yako idzadzaza ndi vinyo.

11 Mwana wanga usanyoze malangizo a Yehova,
    ndipo usayipidwe ndi chidzudzulo chake.
12 Paja Yehova amadzudzula amene amamukonda,
    monga abambo achitira mwana amene amakondwera naye.

13 Wodala munthu amene wapeza nzeru,
    munthu amene walandira nzeru zomvetsa zinthu,
14 pakuti phindu la nzeru ndi labwino kuposa la siliva,
    phindu lakelo ndi labwino kuposanso golide.
15 Nzeru ndi yoposa miyala yamtengowapatali;
    ndipo zonse zimene umazikhumba sizingafanane ndi nzeru.
16 Mʼdzanja lake lamanja muli moyo wautali;
    mʼdzanja lake lamanzere muli chuma ndi ulemu.
17 Njira zake ndi njira zosangalatsa,
    ndipo mu njira zake zonse muli mtendere.
18 Nzeru ili ngati mtengo wopatsa moyo kwa oyigwiritsitsa;
    wodala munthu amene amayigwiritsa kwambiri.

19 Yehova anakhazikitsa dziko lapansi pogwiritsa ntchito nzeru.
    Anagwiritsanso ntchito nzeru zakudziwa bwino zinthu pamene ankakhazikitsa zakumwamba.
20 Mwa nzeru zake Yehova anatumphutsa madzi kuchokera mʼnthaka
    ndiponso mitambo inagwetsa mvula.

21 Mwana wanga usunge nzeru yeniyeni ndi khalidwe lomalingarira zinthu bwino.
    Zimenezi zisakuchokere.
22 Zimenezi zidzakupatsa moyo,
    moyo wake wosangalatsa ndi wabwino ngati mkanda wa mʼkhosi.
23 Choncho udzayenda pa njira yako mosaopa kanthu,
    ndipo phazi lako silidzapunthwa;
24 pamene ugona pansi, sudzachita mantha;
    ukadzagona pansi tulo tako tidzakhala tokoma.
25 Usaope tsoka lobwera mwadzidzidzi
    kapena chiwonongeko chimene chidzagwera anthu oyipa,
26 pakuti Yehova adzakulimbitsa mtima
    ndipo adzasunga phazi lako kuti lisakodwe mu msampha.

27 Usaleke kuchitira zabwino amene ayenera kulandira zabwino,
    pamene uli nazo mphamvu zochitira zimenezi.
28 Usanene kwa mnansi wako kuti,
    “Pita, uchite kubweranso. Ndidzakupatsa mawa”
    pamene uli nazo tsopano.

29 Usamukonzere chiwembu mnansi wako,
    amene anakhala nawe pafupi mokudalira.
30 Usakangane ndi munthu wopanda chifukwa
    pamene iye sanakuchitire zoyipa.

31 Usachite naye nsanje munthu wachiwawa
    kapena kutsanzira khalidwe lake lililonse.
32 Pakuti Yehova amanyansidwa ndi munthu woyipa
    koma amayanjana nawo anthu olungama.

33 Yehova amatemberera nyumba ya munthu woyipa,
    koma amadalitsa nyumba ya anthu olungama.
34 Anthu onyoza, Iye amawanyoza,
    koma amakomera mtima anthu odzichepetsa.
35 Anthu anzeru adzalandira ulemu,
    koma zitsiru adzazichititsa manyazi.