Add parallel Print Page Options

26 Ngati chisanu choti mbee nthawi yachilimwe kapena mvula nthawi yokolola,
    ndi momwe zilili ndi ulemu wowulandira chitsiru.

Ngati timba wokhalira kuwuluka kapena namzeze wokhalira kuzungulirazungulira,
    ndi mmenenso limachitira temberero lopanda chifukwa, silichitika.

Mkwapulo ndi wokwapulira kavalo, chitsulo ndi cha mʼkamwa mwa bulu,
    choncho ndodo ndi yoyenera ku msana wa chitsiru.

Usayankhe chitsiru monga mwa uchitsiru wake,
    kuopa kuti ungadzakhale ngati chitsirucho.

Koma nthawi zina umuyankhe monga mwa uchitsiru wake,
    kuopa kuti angamadziyese yekha wanzeru.

Kutuma chitsiru kuti akapereke uthenga
    kuli ngati kudzidula mapazi ndipo kumakuyitanira mavuto.

Monga miyendo ya munthu wolumala imene ilibe mphamvu
    ndi mmene ulili mwambi mʼkamwa mwa chitsiru.

Kupereka ulemu kwa chitsiru
    zili ngati kukulunga mwala mʼlegeni.

Monga umachitira mtengo waminga wobaya mʼdzanja la chidakwa
    ndi mmene ulili mwambi mʼkamwa mwa chitsiru.

10 Munthu amene amalemba ntchito chitsiru chongoyendayenda,
    ali ngati woponya mivi amene angolasa anthu chilaselase.

11 Chitsiru chimene chimabwerezabwereza uchitsiru wake
    chili ngati galu amene amabwerera ku masanzi ake.

12 Munthu wa uchitsiru aliko bwino popeza pali chiyembekezo
    kuposana ndi munthu amene amadziyesa yekha kuti ndi wanzeru.

13 Munthu waulesi amati, “Mu msewu muli mkango,
    mkango woopsa ukuyendayenda mʼmisewu!”

14 Monga chitseko chimapita uku ndi uku pa zolumikizira zake,
    momwemonso munthu waulesi amangotembenukatembenuka pa bedi lake.

15 Munthu waulesi akapisa dzanja lake mu mʼbale;
    zimamutopetsa kuti alifikitse pakamwa pake.

16 Munthu waulesi amadziyesa yekha wanzeru
    kuposa anthu asanu ndi awiri amene amayankha mochenjera.

17 Munthu wongolowera mikangano imene si yake
    ali ngati munthu wogwira makutu a galu wongodziyendera.

18 Monga munthu wamisala amene
    akuponya sakali zamoto kapena mivi yoopsa,
19 ndi momwe alili munthu wonamiza mnzake,
    amene amati, “Ndimangoseka chabe!”

20 Pakasowa nkhuni, moto umazima;
    chomwechonso pakasowa anthu amiseche mkangano umatha.

21 Monga alili makala pa moto wonyeka kapena mmene zimachitira nkhuni pa moto,
    ndi mmene alili munthu wolongolola poyambitsa mikangano.

22 Mawu a munthu wamiseche ali ngati chakudya chokoma;
    chimene chimatsikira mʼmimba mwa munthu.

23 Monga mmene chiziro chimakutira chiwiya chadothi
    ndi mmene mawu oshashalika amabisira mtima woyipa.

24 Munthu wachidani amayankhula zabwino
    pamene mu mtima mwake muli chinyengo.
25 Ngakhale wotereyu mawu ake ali okoma, koma usamukhulupirire,
    pakuti mu mtima mwake mwadzaza zonyansa.
26 Ngakhale amabisa chidani mochenjera,
    koma kuyipa kwakeko kudzaonekera poyera pa gulu la anthu.

27 Ngati munthu akumba dzenje, adzagweramo yekha;
    ngati munthu agubuduza mwala, udzamupsinja iye mwini.

28 Munthu wonama amadana ndi amene anawapweteka,
    ndipo pakamwa poshashalika pamabweretsa chiwonongeko.