Add parallel Print Page Options

Mlandu wa Yehova ndi Israeli

Tamverani zimene Yehova akunena:

“Nyamukani, fotokozani mlandu wanu pamaso pa mapiri;
    zitunda zimve zimene inu muti muyankhule.
Imvani mlandu wa Yehova, inu mapiri;
    tamverani, maziko amuyaya a dziko lapansi.
Pakuti Yehova ali ndi mlandu ndi anthu ake;
    Iye akutsutsa Aisraeli.

“Anthu anga, kodi ndakuchitirani chiyani?
    Kodi ndakutopetsani bwanji? Ndiyankheni.
Ine ndinakutulutsani ku dziko la Igupto
    ndi kukuwombolani ku nyumba ya ukapolo.
Ndinatuma Mose kuti akutsogolereni,
    pamodzi ndi Aaroni ndi Miriamu.
Anthu anga, kumbukirani
    zimene Balaki mfumu ya ku Mowabu inafuna kukuchitirani
    ndiponso zimene Balaamu mwana wa Beori anayankha.
Kumbukirani zomwe zinachitika pa ulendo wochoka ku Sitimu kupita ku Giligala,
    kuti mudziwe machitidwe olungama a Yehova.”

Kodi ndidzatenga chiyani kupita nacho pamaso pa Yehova
    ndi kukagwada pamaso pa Mulungu wakumwamba?
Kodi ndidzabwera pamaso pake ndi nsembe yopsereza,
    ndi ana angʼombe a chaka chimodzi?
Kodi Yehova adzakondwera ndi nkhosa zazimuna 1,000,
    kapena ndi mitsinje yosalekeza ya mafuta?
Kodi ndipereke nsembe mwana wanga woyamba kubadwa chifukwa cha zolakwa zanga?
    Chipatso cha thupi langa chifukwa cha tchimo la moyo wanga?
Munthu iwe, Yehova wakuonetsa kale chimene chili chabwino.
    Tsono kodi Yehova akuyembekezera chiyani kwa iwe?
Uzichita zolungama ndi kukonda chifundo
    ndiponso kuyenda modzichepetsa pamaso pa Mulungu wako.

Kulakwa kwa Israeli ndi Chilango chake

Tamverani! Yehova akuyitana anthu okhala mu mzinda
    ndi nzeru kuopa dzina lanu.
    “Mverani mfumu ndi Iye amene anayikhazikitsa.
10 Inu anthu oyipa, kodi Ine nʼkuyiwala
    chuma chanu chimene munachipeza mwachinyengo,
    ndiponso muyeso wanu woperewera umene ndi wotembereredwa?
11 Kodi ndimutenge ngati wosalakwa munthu amene ali ndi sikelo yachinyengo,
    ndiponso miyeso yabodza mʼthumba lake?
12 Anthu ake olemera amachita zachiwawa;
    anthu ake ndi abodza
    ndipo pakamwa pawo pamayankhula zachinyengo.
13 Choncho, ndayamba kukuwonongani,
    kukusakazani chifukwa cha machimo anu.
14 Mudzadya, koma simudzakhuta;
    mudzakhalabe ndi njala.
Mudzasunga zinthu, koma sizidzasungika,
    chifukwa zimene mudzasunga zidzawonongedwa ndi lupanga.
15 Mudzadzala, koma simudzakolola.
    Mudzayenga mafuta a olivi, koma simudzawagwiritsa ntchito.
    Mudzaponda mphesa, koma simudzamwa vinyo wake.
16 Inu mwatsatira malangizo a Omuri
    ndiponso machitidwe onse a banja la Ahabu,
    ndi khalidwe lawo lonse.
Choncho Ine ndidzakuperekani kuti muwonongedwe
    ndiponso anthu anu kuti azunguzike mitu;
    mudzanyozedwa ndi anthu a mitundu ina.”