Add parallel Print Page Options

Inu Yehova, kumbukirani zimene zinatichitikira;
    yangʼanani ndipo muone kunyozeka kwathu.
Apereka cholowa chathu kwa obwera,
    nyumba zathu kwa alendo.
Takhala amasiye ndi wopanda abambo,
    amayi athu ali ngati akazi amasiye.
Tiyenera kugula madzi amene timamwa,
    nkhuni zathunso nʼzogula.
Otilondola atigwira pakhosi;
    tafowoka ndipo sakutilola kupumula.
Tinadzipereka kwa Aigupto ndi kwa Asiriya
    kuti tipeze chakudya.
Makolo athu anachimwa ndipo anafa kale,
    koma chilango chawo chili pa ife.
Akapolo akutilamulira,
    ndipo palibe ndi mmodzi yemwe angatimasule mʼdzanja lawo.
Timapeza chakudya chathu poyika miyoyo yathu pa chiswe
    chifukwa cha lupanga mʼchipululu.
10 Khungu lathu latentha ngati uvuni mʼngʼanjo,
    chifukwa cha kuwawa kwa njala.
11 Amayi agwiriridwa mu Ziyoni,
    ndi anamwali mʼmizinda ya Yuda.
12 Akalonga athu akuwapachika pomangirira manja awo,
    akuluakulu sakuwalemekeza.
13 Achinyamata akukakamizidwa kupera tirigu;
    anyamata akudzandira ndi mitolo ya nkhuni.
14 Akuluakulu anachokapo pa chipata cha mzinda;
    achinyamata aleka nyimbo zawo.
15 Chimwemwe chachoka mʼmitima yathu;
    kuvina kwathu kwasanduka maliro.
16 Chipewa chathu chaufumu chagwa pamutu pathu.
    Tsoka kwa ife, chifukwa tachimwa!
17 Mitima yathu yakomoka chifukwa cha zimenezi,
    chifukwa cha zinthu zimenezi maso athu sakuona bwino,
18 pakuti phiri la Ziyoni, limene lasanduka bwinja,
    nkhandwe zikungoyendayendapo.

19 Inu Yehova, lamulirani kwamuyaya;
    mpando wanu waufumu udzakhalabe ku mibadomibado.
20 Chifukwa chiyani mumatiyiwala nthawi zonse?
    Chifukwa chiyani mwatitaya nthawi yayitali chotere?
21 Yehova mutitembenuzire kwa Inu, kuti tibwerere;
    mukonzenso masiku athu akhale monga akale,
22 pokhapokha ngati mwatitaya kotheratu,
    ndi kuti mwatikwiyira kobzola muyeso.