Add parallel Print Page Options

23 Yehova anawuza Mose kuti, “Yankhula ndi Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Awa ndi masiku anga osankhika a chikondwerero, masiku osankhika olemekeza Yehova amene uyenera kulengeza kuti akhale masiku opatulika a misonkhano.

Za Sabata

“ ‘Pa masiku asanu ndi limodzi muzigwira ntchito, koma tsiku lachisanu ndi chiwiri ndi Sabata lopuma, tsiku la msonkhano wopatulika. Kulikonse kumene inu mukukhala musamagwire ntchito iliyonse tsiku limeneli popeza ndi tsiku la Sabata la Yehova.

Za Paska ndi za Buledi Wopanda Yisiti

“ ‘Awa ndiwo masiku osankhidwa a zikondwerero za Yehova, masiku woyera a misonkhano amene muti mudzalengeze pa nthawi yake: Chikondwerero cha Paska chiziyamba madzulo a tsiku la 14 la mwezi woyamba. Tsiku la 15 la mwezi womwewo ndi tsiku lolemekeza Yehova ndipo muziyamba Chikondwerero cha Buledi Wopanda Yisiti. Muzidya buledi wopanda yisiti kwa masiku asanu ndi awiri. Pa tsiku loyamba muzichita msonkhano wopatulika. Musamagwire ntchito iliyonse. Pa masiku asanu ndi awiri muzipereka nsembe yopsereza kwa Yehova. Ndipo tsiku lachisanu ndi chiwiri muzikhala ndi msonkhano wopatulika ndipo musamagwire ntchito yolemetsa.’ ”

Za Zipatso Zoyambirira Kucha

Yehova anawuza Mose kuti, 10 “Yankhula ndi Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Mukakalowa mʼdziko limene ndikukupatsanilo ndi kukolola za mʼminda mwanu, mudzabwere kwa wansembe ndi mtolo wa tirigu woyambirira kucha wa mʼminda mwanu. 11 Wansembeyo auweyule mtolowo pamaso pa Yehova kotero mtolowo udzalandiridwa mʼmalo mwanu. Wansembe auweyule tsiku lotsatana ndi la Sabata. 12 Pa tsiku limene muweyula mtolowo, muperekenso mwana wankhosa wa mwamuna wa chaka chimodzi, wopanda chilema kuti akhale nsembe yopsereza ya kwa Yehova. 13 Chopereka chachakudya chake chikhale cha makilogalamu awiri a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta kuti chikhale nsembe yopsereza yopereka kwa Yehova, ya fungo lokoma. Ndipo chopereka cha chakumwa chake chikhale vinyo wa malita anayi ndi theka. 14 Musadye buledi aliyense kapena tirigu wokazinga, kapena wamuwisi mpaka tsiku limene mwabwera ndi chopereka ichi kwa Mulungu wanu. Limeneli ndi lamulo lamuyaya pa mibado yanu yonse, kulikonse kumene mukakhale.

Chikondwerero cha Masabata

15 “ ‘Kuyambira tsiku lotsatana ndi la Sabata lija, tsiku limene munabwera ndi mtolo wa nsembe yoweyula, muziwerenga masabata asanu ndi awiri athunthu. 16 Ndiye kuti muwerenge masiku makumi asanu kuchokera pa tsiku lotsatana ndi Sabata la chisanu ndi chiwiri, ndipo kenaka mupereke nsembe ya tirigu watsopano kwa Yehova. 17 Kuchokera kulikonse kumene mukukhala, mubwere pamaso pa Yehova ndi buledi muwiri wa ufa wosalala wa makilogalamu awiri, ophikidwa ndi yisiti kuti akhale nsembe yoweyula ya zakudya zoyamba kucha. 18 Pamodzi ndi bulediyu muperekenso ana ankhosa aamuna asanu ndi awiri, aliyense akhale wa chaka chimodzi ndi wopanda chilema. Pakhalenso ngʼombe yayingʼono yayimuna ndi nkhosa zazimuna ziwiri. Zimenezi zidzakhala nsembe zopsereza zopereka kwa Yehova pamodzi ndi nsembe za zakudya ndi nsembe za zakumwa. Zonsezi zikhale nsembe zopsereza za fungo lokomera Yehova. 19 Kenaka mupereke mbuzi imodzi yayimuna kuti ikhale nsembe yopepesera machimo ndiponso ana ankhosa awiri, aliyense wa chaka chimodzi kuti akhale nsembe yachiyanjano. 20 Wansembe aweyule ana ankhosa awiriwo pamaso pa Yehova monga nsembe yoweyula, pamodzi ndi buledi wa tirigu woyambirira kucha. Zimenezi ndi zopereka zopatulika za Yehova zopatsidwa kwa ansembe. 21 Pa tsiku lomwelo mulengeze za msonkhano wopatulika ndipo musagwire ntchito zolemetsa. Limeneli ndi lamulo lamuyaya pa mibado yanu yonse, kulikonse kumene mukakhale.

22 “ ‘Pamene mukukolola zinthu mʼmunda mwanu, musakolole munda wanu mpaka mʼmalire mwenimweni, ndipo musatole khunkha lake. Zimenezo musiyire anthu osauka ndi alendo. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.’ ”

Chikondwerero cha Malipenga

23 Yehova anawuza Mose kuti, 24 “Uza Aisraeli kuti, ‘Tsiku loyamba la mwezi wachisanu ndi chiwiri, likhale tsiku lopumula, la msonkhano wopatulika, mulilengeze poyimba lipenga. 25 Musagwire ntchito zolemetsa koma mupereke nsembe yopsereza kwa Yehova.’ ”

Tsiku Lopepesera Machimo

26 Yehova anawuza Mose kuti, 27 “Tsiku lakhumi la mwezi wachisanu ndi chiwiri ndi tsiku lochita Mwambo Wopepesera Machimo. Muzichita msonkhano wopatulika. Muzidzichepetsa pamaso pa Yehova ndi kupereka nsembe zopsereza kwa Yehova. 28 Tsiku limeneli musamagwire ntchito chifukwa ndi tsiku la Mwambo Wopepesera Machimo, kupepesera machimo anu pamaso pa Yehova Mulungu wanu. 29 Munthu aliyense amene sasala zakudya pa tsiku limeneli ayenera kuchotsedwa pakati pa anthu a mtundu wake. 30 Aliyense wogwira ntchito tsiku limeneli ndidzamuwononga pakati pa anthu a mtundu wake. 31 Inu musadzagwire ntchito iliyonse. Limeneli ndi lamulo lamuyaya pa mibado yanu yonse, kulikonse kumene mukakhale. 32 Limeneli kwa inu ndi tsiku la Sabata lopumula, ndipo muyenera kusala zakudya. Kuyambira madzulo a tsiku lachisanu ndi chinayi la mwezi mpaka madzulo ena otsatirawo muzisunga tsikulo ngati Sabata lanu.”

Chikondwerero cha Misasa

33 Yehova anawuza Mose kuti, 34 “Uwawuze Aisraeli kuti pa masiku asanu ndi awiri kuyambira pa tsiku la 15 la mwezi wachisanu ndi chiwiri pazikhala Chikondwerero cha Misasa cholemekeza Yehova. 35 Tsiku loyamba ndi la msonkhano wopatulika, musagwire ntchito zolemetsa. 36 Pa masiku asanu ndi awiri muzipereka nsembe zopsereza kwa Yehova. Ndipo pa tsiku lachisanu ndi chitatu muzikhala ndi msonkhano wopatulika ndipo muzipereka nsembe yopsereza kwa Yehova. Kumeneku ndi kutsekera kwa msonkhano waukulu. Musagwire ntchito zolemetsa.

37 (“ ‘Amenewa ndi masiku osankhika a chikondwerero cha Yehova, amene muziwalengeza kuti ndi nthawi ya msonkhano wopatulika. Masiku amenewa muzipereka nsembe zopsereza, nsembe za chakudya, nsembe zanyama ndi zopereka zachakumwa za tsiku ndi tsiku. 38 Zopereka zimenezi ndi zowonjezera pa zopereka za Yehova za pa Sabata, zopereka zanu zolumbira ndiponso mphatso zanu zaufulu zopereka kwa Yehova.)

39 “ ‘Choncho kuyambira pa tsiku la 15 la mwezi wachisanu ndi chiwiri, mutakolola zinthu mʼmunda mwanu, muchite chikondwerero cha Yehova kwa masiku asanu ndi awiri. Tsiku loyamba ndi tsiku lopumula, ndipo tsiku lachisanu ndi chitatu ndi lopumulanso. 40 Pa tsiku loyamba muzitenga zipatso zabwino kwambiri zothyola mʼmitengo, nthambi za kanjedza, nthambi zazikulu za mitengo ya masamba ambiri, ndi za misondozi yakumtsinje, ndipo muzikondwera pamaso pa Yehova Mulungu wanu kwa masiku asanu ndi awiri. 41 Chaka chilichonse muzichita chikondwerero cha Yehova kwa masiku asanu ndi awiri. Limeneli ndi lamulo lamuyaya pa mibado yanu yonse. Muzichita chikondwerero chimenechi mwezi wachisanu ndi chiwiri. 42 Muzikhala mʼmisasa masiku asanu ndi awiri. Onse amene ali mbadwa mʼdziko la Israeli azikhala mʼmisasa 43 kuti zidzukulu zanu zidzadziwe kuti ndine amene ndinakhazika Aisraeli mʼmisasa nditawatulutsa ku Igupto. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.’ ”

44 Choncho Mose analengeza kwa Aisraeli masiku osankhika a zikondwerero za Yehova.

The Appointed Festivals

23 The Lord said to Moses, “Speak to the Israelites and say to them: ‘These are my appointed festivals,(A) the appointed festivals of the Lord, which you are to proclaim as sacred assemblies.(B)

The Sabbath

“‘There are six days when you may work,(C) but the seventh day is a day of sabbath rest,(D) a day of sacred assembly. You are not to do any work;(E) wherever you live, it is a sabbath to the Lord.

The Passover and the Festival of Unleavened Bread(F)

“‘These are the Lord’s appointed festivals, the sacred assemblies you are to proclaim at their appointed times:(G) The Lord’s Passover(H) begins at twilight on the fourteenth day of the first month.(I) On the fifteenth day of that month the Lord’s Festival of Unleavened Bread(J) begins; for seven days(K) you must eat bread made without yeast. On the first day hold a sacred assembly(L) and do no regular work. For seven days present a food offering to the Lord.(M) And on the seventh day hold a sacred assembly and do no regular work.’”

Offering the Firstfruits

The Lord said to Moses, 10 “Speak to the Israelites and say to them: ‘When you enter the land I am going to give you(N) and you reap its harvest,(O) bring to the priest a sheaf(P) of the first grain you harvest.(Q) 11 He is to wave the sheaf before the Lord(R) so it will be accepted(S) on your behalf; the priest is to wave it on the day after the Sabbath. 12 On the day you wave the sheaf, you must sacrifice as a burnt offering to the Lord a lamb a year old(T) without defect,(U) 13 together with its grain offering(V) of two-tenths of an ephah[a](W) of the finest flour mixed with olive oil—a food offering presented to the Lord, a pleasing aroma—and its drink offering(X) of a quarter of a hin[b] of wine.(Y) 14 You must not eat any bread, or roasted or new grain,(Z) until the very day you bring this offering to your God.(AA) This is to be a lasting ordinance for the generations to come,(AB) wherever you live.(AC)

The Festival of Weeks(AD)

15 “‘From the day after the Sabbath, the day you brought the sheaf of the wave offering, count off seven full weeks. 16 Count off fifty days up to the day after the seventh Sabbath,(AE) and then present an offering of new grain to the Lord. 17 From wherever you live, bring two loaves made of two-tenths of an ephah(AF) of the finest flour, baked with yeast, as a wave offering of firstfruits(AG) to the Lord. 18 Present with this bread seven male lambs, each a year old and without defect, one young bull and two rams. They will be a burnt offering to the Lord, together with their grain offerings and drink offerings(AH)—a food offering, an aroma pleasing to the Lord. 19 Then sacrifice one male goat for a sin offering[c] and two lambs, each a year old, for a fellowship offering. 20 The priest is to wave the two lambs before the Lord as a wave offering,(AI) together with the bread of the firstfruits. They are a sacred offering to the Lord for the priest. 21 On that same day you are to proclaim a sacred assembly(AJ) and do no regular work.(AK) This is to be a lasting ordinance for the generations to come, wherever you live.

22 “‘When you reap the harvest(AL) of your land, do not reap to the very edges of your field or gather the gleanings of your harvest.(AM) Leave them for the poor and for the foreigner residing among you.(AN) I am the Lord your God.’”

The Festival of Trumpets(AO)

23 The Lord said to Moses, 24 “Say to the Israelites: ‘On the first day of the seventh month you are to have a day of sabbath rest, a sacred assembly(AP) commemorated with trumpet blasts.(AQ) 25 Do no regular work,(AR) but present a food offering to the Lord.(AS)’”

The Day of Atonement(AT)

26 The Lord said to Moses, 27 “The tenth day of this seventh month(AU) is the Day of Atonement.(AV) Hold a sacred assembly(AW) and deny yourselves,[d] and present a food offering to the Lord. 28 Do not do any work(AX) on that day, because it is the Day of Atonement, when atonement is made for you before the Lord your God. 29 Those who do not deny themselves on that day must be cut off from their people.(AY) 30 I will destroy from among their people(AZ) anyone who does any work on that day. 31 You shall do no work at all. This is to be a lasting ordinance(BA) for the generations to come, wherever you live. 32 It is a day of sabbath rest(BB) for you, and you must deny yourselves. From the evening of the ninth day of the month until the following evening you are to observe your sabbath.”(BC)

The Festival of Tabernacles(BD)

33 The Lord said to Moses, 34 “Say to the Israelites: ‘On the fifteenth day of the seventh(BE) month the Lord’s Festival of Tabernacles(BF) begins, and it lasts for seven days. 35 The first day is a sacred assembly;(BG) do no regular work.(BH) 36 For seven days present food offerings to the Lord, and on the eighth day hold a sacred assembly(BI) and present a food offering to the Lord.(BJ) It is the closing special assembly; do no regular work.

37 (“‘These are the Lord’s appointed festivals, which you are to proclaim as sacred assemblies for bringing food offerings to the Lord—the burnt offerings and grain offerings, sacrifices and drink offerings(BK) required for each day. 38 These offerings(BL) are in addition to those for the Lord’s Sabbaths(BM) and[e] in addition to your gifts and whatever you have vowed and all the freewill offerings(BN) you give to the Lord.)

39 “‘So beginning with the fifteenth day of the seventh month, after you have gathered the crops of the land, celebrate the festival(BO) to the Lord for seven days;(BP) the first day is a day of sabbath rest, and the eighth day also is a day of sabbath rest. 40 On the first day you are to take branches(BQ) from luxuriant trees—from palms, willows and other leafy trees(BR)—and rejoice(BS) before the Lord your God for seven days. 41 Celebrate this as a festival to the Lord for seven days each year. This is to be a lasting ordinance for the generations to come; celebrate it in the seventh month. 42 Live in temporary shelters(BT) for seven days: All native-born Israelites are to live in such shelters 43 so your descendants will know(BU) that I had the Israelites live in temporary shelters when I brought them out of Egypt. I am the Lord your God.’”

44 So Moses announced to the Israelites the appointed festivals of the Lord.

Footnotes

  1. Leviticus 23:13 That is, probably about 7 pounds or about 3.2 kilograms; also in verse 17
  2. Leviticus 23:13 That is, about 1 quart or about 1 liter
  3. Leviticus 23:19 Or purification offering
  4. Leviticus 23:27 Or and fast; similarly in verses 29 and 32
  5. Leviticus 23:38 Or These festivals are in addition to the Lord’s Sabbaths, and these offerings are