Add parallel Print Page Options

Maloto a Farao

41 Patapita zaka ziwiri zathunthu, Farao analota atayimirira mʼmbali mwa mtsinje wa Nailo, ndipo anangoona ngʼombe zazikazi zisanu ndi ziwiri zooneka bwino ndi zonenepa zikutuluka mu mtsinje muja ndi kuyamba kudya msipu wa mu mawango. Kenaka ngʼombe zina zazikazi zisanu ndi ziwiri zosaoneka bwino ndi zowonda zinatulukanso mu mtsinje wa Nailo ndipo zinayimirira pambali pa zina zija zimene zinali mʼmphepete mwa mtsinje uja. Ndipo ngʼombe zosaoneka bwino ndi zowonda zija zinadya ngʼombe zonenepa zija. Kenaka Farao anadzidzimuka.

Posakhalitsa anagonanso ndipo analota kachiwiri: Analota ngala zisanu ndi ziwiri za tirigu zathanzi labwino zitabala pa phata limodzi. Kenaka ngala zina zisanu ndi ziwiri zinaphuka. Izi zinali zowonda ndi zowauka ndi mphepo ya kummawa. Ngala zowonda zija zinameza ngala zathanzi ndi zonenepa zija. Farao anadzidzimuka ndipo anaona kuti anali maloto chabe.

Mmawa, Farao anavutika mu mtima kotero anayitanitsa amatsenga ndi anzeru onse a mu Igupto. Iwo atabwera, iye anawawuza maloto ake, koma panalibe ndi mmodzi yemwe amene anatha kutanthauzira malotowo kwa Farao.

Ndipo mkulu wa operekera zakumwa anati kwa Farao, “Lero ndakumbukira kulephera kwanga. 10 Paja nthawi ina Farao anapsera mtima antchito akefe, ndipo anatitsekera (ine ndi mkulu wa ophika buledi) mʼndende, mʼnyumba ya mkulu wa alonda. 11 Tsiku lina tonse awiri tinalota maloto, ndipo loto lililonse linali ndi tanthauzo lake. 12 Tsono momwemo munali mnyamata wina Wachihebri, wantchito wa mkulu wa alonda. Ife tinamufotokozera maloto athu, ndipo anatitanthauzira malotowo. Munthu aliyense anamupatsa tanthauzo la loto lake. 13 Ndipo zinthu zinachitikadi monga mmene anatitanthauzira. Ine anandibwezera pa ntchito yanga ndipo winayo anapachikidwa.”

14 Choncho Farao anamuyitanitsa Yosefe, ndipo mofulumira anabwera naye kuchokera mʼdzenje muja. Ndipo atameta, ndi kusintha zovala, anapita kwa Farao.

15 Farao anati kwa Yosefe, “Ndinalota maloto ndipo palibe amene watha kunditanthauzira. Tsono ndawuzidwa kuti iwe ukamva loto umadziwanso kulimasulira.”

16 Yosefe anamuyankha Farao kuti, “Sindingathe koma Mulungu apereka yankho limene Farao akufuna.”

17 Ndipo Farao anati kwa Yosefe, “Ndinalota nditayimirira mʼmphepete mwa mtsinje wa Nailo, 18 ndipo ngʼombe zisanu ndi ziwiri zonenepa ndi zooneka bwino zinatuluka mu mtsinje muja ndi kumadya msipu wa mu mawango. 19 Kenaka, ngʼombe zina zisanu ndi ziwiri zinatuluka. Izi zinali zosaoneka bwino ndiponso zowonda ndipo sindinaonepo ngʼombe zosaoneka bwino chonchi mʼdziko lonse la Igupto. 20 Ngʼombe zosaoneka bwino ndi zowonda zija zinadya zisanu ndi ziwiri zonenepa zimene zinatuluka poyamba zija. 21 Koma ngakhale ngʼombezi zinadya zinazo, palibe amene akanatha kuzindikira kuti zinatero popeza zinali zosaonekabe bwino monga poyamba. Ndipo ndinadzidzimuka.

22 “Nditagonanso kachiwiri, ndinalota ngala zisanu ndi ziwiri za tirigu zathanzi ndi zonenepa zitabala pa phata limodzi. 23 Kenaka panaphukanso ngala zina zisanu ndi ziwiri zofota, zowonda ndi zowauka ndi mphepo ya kummawa. 24 Ngala zowondazo zinameza ngala zisanu ndi ziwiri zabwino zija. Ndinawawuza amatsenga koma palibe ndi mmodzi yemwe anatha kundimasulira.”

25 Ndipo Yosefe anati kwa Farao, “Maloto awiriwa ndi ofanana ndipo ali ndi tanthauzo limodzi. Mulungu waululira Farao chimene atachite. 26 Ngʼombe zisanu ndi ziwiri zabwinozo ndi zaka zisanu ndi ziwiri. Ndipo ngala zisanu ndi ziwiri zabwinozo ndi zaka zisanu ndi ziwiri. Kutanthauza kwa maloto nʼkumodzi. 27 Ngʼombe zisanu ndi ziwiri zowonda ndi zosaoneka bwino zimene zinatuluka pambuyozo ndiponso ngala zisanu ndi ziwiri zachabechabe, zowauka ndi mphepo ya kummawa zija ndi zaka zisanu ndi ziwiri za njala.

28 “Tsono ndi monga ndafotokozeramu kuti Mulungu wakuwuziranitu zimene adzachite. 29 Zaka zisanu ndi ziwiri za zokolola zochuluka zikubwera mu dziko lonse la Igupto, 30 koma zidzatsatana ndi zaka zina zisanu ndi ziwiri za njala. Chakudya chochuluka cha mu Igupto chija chidzayiwalika ndipo njalayo idzawononga dziko. 31 Zakudya zochuluka za mʼdzikomo zija sizidzakumbukirikanso chifukwa njala imene iti idzabwereyo idzakhala yoopsa. 32 Popeza kuti malotowa aperekedwa kwa inu Mfumu kawiri, ndiye kuti Mulungu watsimikiza kuti adzachitadi zimenezi posachedwapa.

33 “Tsopano Farao apezeretu munthu wozindikira ndi wanzeru ndipo amuyike kukhala woyangʼanira dziko lonse la Igupto. 34 Asankhenso akuluakulu a mʼdziko lino. Iwowa azitenga ndi kuyika padera limodzi la magawo asanu aliwonse a zokolola za mʼdziko muno mu zaka zonse zisanu ndi ziwiri za chakudya chochuluka. 35 Iwo asonkhanitse zakudya zonse za mʼzaka zabwino zikubwerazi. Pansi pa ulamuliro wa Farao, akuluakuluwo asonkhanitse ndi kusunga bwino tirigu mʼmizinda yonse. 36 Chakudya chimenechi chisungidwe kuti chidzagwiritsidwe ntchito mʼzaka zisanu ndi ziwiri za njala imene ikubwerayo mu Igupto, kuti anthu a mʼdzikoli asadzafe ndi njalayo.”

37 Farao ndi nduna zake anagwirizana nawo malangizo a Yosefe. 38 Choncho Farao anafunsa nduna zake nati, “Kodi tingathe kumupeza munthu wina ngati uyu, amene ali ndi mzimu wa Mulungu?”

39 Farao anati kwa Yosefe, “Pakuti Mulungu wakudziwitsa iwe zonsezi, palibe wina wodziwa zinthu ndi wanzeru ngati iwe. 40 Iwe ukhala nduna yayikulu mu dziko langa ndipo anthu onse adzamvera zimene walamula. Ine ndekha ndiye amene ndidzakuposa mphamvu chifukwa ndimakhala pa mpando waufumu.”

Yosefe Alamulira Dziko la Igupto

41 Choncho Farao anati kwa Yosefe, “Ine ndikukuyika iwe kukhala nduna yoyangʼanira dziko lonse la Igupto.” 42 Ndipo Farao anavula mphete ku chala chake nayiveka ku chala cha Yosefe. Anamuvekanso mkanjo wonyezimira ndi nkufu wagolide mʼkhosi mwake. 43 Anamukweza Yosefe pa galeta ngati wachiwiri pa ulamuliro. Ndipo anthu anafuwula pamaso pake nati, “Mʼgwadireni!” Motero anakhala nduna yayikulu ya dziko lonse la Igupto.

44 Kenaka Farao anati kwa Yosefe, “Ine ndine Farao; tsono iwe ukapanda kulamula, palibe amene akhoza kuchita chilichonse ngakhale kuyenda kumene mʼdziko lonse la Igupto.” 45 Farao anamupatsa Yosefe dzina lakuti Zafenati-Panea ndipo anamupatsanso Asenati mwana wa mkazi wa Potifara, wansembe wa Oni, kuti akhale mkazi wake. Choncho Yosefe anayendera dziko lonse la Igupto.

46 Yosefe anali ndi zaka 30 pamene amayamba ntchito kwa Farao, mfumu ya ku Igupto. Ndipo Yosefe anachoka pa maso pa Farao nayendera dziko lonse la Igupto. 47 Mʼzaka zisanu ndi ziwiri za zokolola zambiri zija, anthu mʼdzikomo anakolola zochuluka. 48 Yosefe anasonkhanitsa zakudya zonse zokololedwa mʼzaka zisanu ndi ziwiri zija ndipo anazisunga mʼmizinda. Mu mzinda uliwonse anayikamo chakudya chimene chinalimidwa mʼminda yozungulira komweko. 49 Yosefe anasunga tirigu wochuluka kwambiri ngati mchenga wa ku nyanja. Kunali tirigu wochuluka kwambiri motero kuti analeka nʼkulembera komwe.

50 Zisanafike zaka zanjala, Yosefe anabereka ana aamuna awiri mwa Asenati mwana wa mkazi wa Potifara, wansembe wa Oni. 51 Yosefe anamutcha mwana wake woyamba, Manase popeza anati, “Mulungu wandiyiwalitsa zovuta zanga zija ndiponso banja la abambo anga.” 52 Mwana wachiwiri wa mwamuna anamutcha Efereimu popeza anati, “Mulungu wandipatsa ana mʼdziko la masautso anga.”

53 Zaka zisanu ndi ziwiri za zokolola zochuluka zija zinatha, 54 ndipo zaka zisanu ndi ziwiri za njala zija zinayamba monga ananenera Yosefe. Njalayi inafika ku mayiko ena onse koma ku dziko lonse la Igupto kunali chakudya. 55 Pamene njala ija inakwanira dziko lonse la Igupto anthu analilira Farao kuti awapatse chakudya. Koma Farao anawawuza kuti, “Pitani kwa Yosefe ndipo mukachite zimene akakuwuzeni.”

56 Pamene njala inafalikira dziko lonse, Yosefe anatsekula nkhokwe za zakudya namagulitsa tirigu kwa anthu a ku Igupto aja, pakuti njala inafika poyipa kwambiri mu Igupto monse. 57 Anthu ankabwera ku Igupto kuchokera ku mayiko ena onse kudzagula tirigu kwa Yosefe, chifukwa njala inafika poyipa kwambiri pa dziko lonse lapansi.

Pharaoh’s Dreams

41 When two full years had passed, Pharaoh had a dream:(A) He was standing by the Nile,(B) when out of the river there came up seven cows, sleek and fat,(C) and they grazed among the reeds.(D) After them, seven other cows, ugly and gaunt, came up out of the Nile and stood beside those on the riverbank. And the cows that were ugly and gaunt ate up the seven sleek, fat cows. Then Pharaoh woke up.(E)

He fell asleep again and had a second dream: Seven heads of grain,(F) healthy and good, were growing on a single stalk. After them, seven other heads of grain sprouted—thin and scorched by the east wind.(G) The thin heads of grain swallowed up the seven healthy, full heads. Then Pharaoh woke up;(H) it had been a dream.

In the morning his mind was troubled,(I) so he sent for all the magicians(J) and wise men of Egypt. Pharaoh told them his dreams, but no one could interpret them for him.(K)

Then the chief cupbearer said to Pharaoh, “Today I am reminded of my shortcomings.(L) 10 Pharaoh was once angry with his servants,(M) and he imprisoned me and the chief baker in the house of the captain of the guard.(N) 11 Each of us had a dream the same night, and each dream had a meaning of its own.(O) 12 Now a young Hebrew(P) was there with us, a servant of the captain of the guard.(Q) We told him our dreams, and he interpreted them for us, giving each man the interpretation of his dream.(R) 13 And things turned out exactly as he interpreted them to us: I was restored to my position, and the other man was impaled.(S)

14 So Pharaoh sent for Joseph, and he was quickly brought from the dungeon.(T) When he had shaved(U) and changed his clothes,(V) he came before Pharaoh.

15 Pharaoh said to Joseph, “I had a dream, and no one can interpret it.(W) But I have heard it said of you that when you hear a dream you can interpret it.”(X)

16 “I cannot do it,” Joseph replied to Pharaoh, “but God will give Pharaoh the answer he desires.”(Y)

17 Then Pharaoh said to Joseph, “In my dream I was standing on the bank of the Nile,(Z) 18 when out of the river there came up seven cows, fat and sleek, and they grazed among the reeds.(AA) 19 After them, seven other cows came up—scrawny and very ugly and lean. I had never seen such ugly cows in all the land of Egypt. 20 The lean, ugly cows ate up the seven fat cows that came up first. 21 But even after they ate them, no one could tell that they had done so; they looked just as ugly as before. Then I woke up.

22 “In my dream I saw seven heads of grain, full and good, growing on a single stalk. 23 After them, seven other heads sprouted—withered and thin and scorched by the east wind. 24 The thin heads of grain swallowed up the seven good heads. I told this to the magicians, but none of them could explain it to me.(AB)

25 Then Joseph said to Pharaoh, “The dreams of Pharaoh are one and the same.(AC) God has revealed to Pharaoh what he is about to do.(AD) 26 The seven good cows(AE) are seven years, and the seven good heads of grain are seven years; it is one and the same dream. 27 The seven lean, ugly cows that came up afterward are seven years, and so are the seven worthless heads of grain scorched by the east wind: They are seven years of famine.(AF)

28 “It is just as I said to Pharaoh: God has shown Pharaoh what he is about to do.(AG) 29 Seven years of great abundance(AH) are coming throughout the land of Egypt, 30 but seven years of famine(AI) will follow them. Then all the abundance in Egypt will be forgotten, and the famine will ravage the land.(AJ) 31 The abundance in the land will not be remembered, because the famine that follows it will be so severe. 32 The reason the dream was given to Pharaoh in two forms is that the matter has been firmly decided(AK) by God, and God will do it soon.(AL)

33 “And now let Pharaoh look for a discerning and wise man(AM) and put him in charge of the land of Egypt.(AN) 34 Let Pharaoh appoint commissioners(AO) over the land to take a fifth(AP) of the harvest of Egypt during the seven years of abundance.(AQ) 35 They should collect all the food of these good years that are coming and store up the grain under the authority of Pharaoh, to be kept in the cities for food.(AR) 36 This food should be held in reserve for the country, to be used during the seven years of famine that will come upon Egypt,(AS) so that the country may not be ruined by the famine.”

37 The plan seemed good to Pharaoh and to all his officials.(AT) 38 So Pharaoh asked them, “Can we find anyone like this man, one in whom is the spirit of God[a]?”(AU)

39 Then Pharaoh said to Joseph, “Since God has made all this known to you,(AV) there is no one so discerning and wise as you.(AW) 40 You shall be in charge of my palace,(AX) and all my people are to submit to your orders.(AY) Only with respect to the throne will I be greater than you.(AZ)

Joseph in Charge of Egypt

41 So Pharaoh said to Joseph, “I hereby put you in charge of the whole land of Egypt.”(BA) 42 Then Pharaoh took his signet ring(BB) from his finger and put it on Joseph’s finger. He dressed him in robes(BC) of fine linen(BD) and put a gold chain around his neck.(BE) 43 He had him ride in a chariot(BF) as his second-in-command,[b](BG) and people shouted before him, “Make way[c]!”(BH) Thus he put him in charge of the whole land of Egypt.(BI)

44 Then Pharaoh said to Joseph, “I am Pharaoh, but without your word no one will lift hand or foot in all Egypt.”(BJ) 45 Pharaoh gave Joseph(BK) the name Zaphenath-Paneah and gave him Asenath daughter of Potiphera, priest(BL) of On,[d](BM) to be his wife.(BN) And Joseph went throughout the land of Egypt.

46 Joseph was thirty years old(BO) when he entered the service(BP) of Pharaoh king of Egypt. And Joseph went out from Pharaoh’s presence and traveled throughout Egypt. 47 During the seven years of abundance(BQ) the land produced plentifully. 48 Joseph collected all the food produced in those seven years of abundance in Egypt and stored it in the cities.(BR) In each city he put the food grown in the fields surrounding it. 49 Joseph stored up huge quantities of grain, like the sand of the sea;(BS) it was so much that he stopped keeping records because it was beyond measure.

50 Before the years of famine came, two sons were born to Joseph by Asenath daughter of Potiphera, priest of On.(BT) 51 Joseph named his firstborn(BU) Manasseh[e](BV) and said, “It is because God has made me forget all my trouble and all my father’s household.” 52 The second son he named Ephraim[f](BW) and said, “It is because God has made me fruitful(BX) in the land of my suffering.”

53 The seven years of abundance in Egypt came to an end, 54 and the seven years of famine(BY) began,(BZ) just as Joseph had said. There was famine in all the other lands, but in the whole land of Egypt there was food. 55 When all Egypt began to feel the famine,(CA) the people cried to Pharaoh for food. Then Pharaoh told all the Egyptians, “Go to Joseph and do what he tells you.”(CB)

56 When the famine had spread over the whole country, Joseph opened all the storehouses and sold grain to the Egyptians,(CC) for the famine(CD) was severe throughout Egypt.(CE) 57 And all the world came to Egypt to buy grain from Joseph,(CF) because the famine was severe everywhere.(CG)

Footnotes

  1. Genesis 41:38 Or of the gods
  2. Genesis 41:43 Or in the chariot of his second-in-command; or in his second chariot
  3. Genesis 41:43 Or Bow down
  4. Genesis 41:45 That is, Heliopolis; also in verse 50
  5. Genesis 41:51 Manasseh sounds like and may be derived from the Hebrew for forget.
  6. Genesis 41:52 Ephraim sounds like the Hebrew for twice fruitful.