Add parallel Print Page Options

Mulungu Ayitana Abramu

12 Tsiku lina Yehova anamuwuza Abramu kuti, “Tuluka mʼdziko lako. Siya abale ako ndi banja la abambo ako ndipo pita ku dziko limene ndidzakusonyeza.

“Ndidzakusandutsa kholo la mtundu waukulu wa anthu
    ndipo ndidzakudalitsa;
ndi kukusandutsa wotchuka kotero kuti
    udzakhala dalitso kwa anthu ambiri.
Ndidzadalitsa amene adzadalitsa iwe,
    ndi kutemberera amene adzatemberera iwe;
ndipo mafuko onse a pa dziko lapansi
    adzadalitsika kudzera mwa iwe.”

Choncho Abramu ananyamuka monga momwe Yehova anamuwuzira, napita pamodzi ndi Loti. Pamene Abramu amachoka ku Harani nʼkuti ali ndi zaka 75. Abramu anatenga mkazi wake Sarai, Loti, mwana wamngʼono wake, pamodzi ndi chuma chawo chimene anapeza ndi antchito amene anali nawo ku Harani. Iwo ananyamuka ulendo mpaka kukafika ku dziko la Kanaani.

Abramu anadutsa mʼdzikomo mpaka kukafika ku Sekemu pa mtengo wa thundu wa ku More. Nthawi imeneyo Akanaani analipobe mʼdzikomo. Yehova anadza kwa Abramu nati, “Kwa zidzukulu zako ndidzapereka dziko limeneli.” Choncho Abramu anamangira Yehova amene anadza kwa iye, guwa lansembe.

Atachoka pamenepo analowera cha ku mapiri a kummawa kwa Beteli namangako tenti yake pakati pa Beteli chakumadzulo ndi Ai chakummawa. Kumeneko anamangira Yehova guwa lansembe napemphera mʼdzina la Yehovayo. Kenaka Abramu ananyamuka kumalowera cha ku Negevi.

Abramu ku Igupto

10 Kunagwa njala yayikulu mʼdzikomo, ndipo Abramu anapita ku Igupto kukakhala ngati mlendo kwa kanthawi kochepa popeza njalayo inakula kwambiri. 11 Atatsala pangʼono kulowa mu Igupto, Abramu anamuwuza mkazi wake Sarai kuti, “Ndimadziwa kuti ndiwe mkazi wokongola kwambiri. 12 Tsono Aigupto akakuona adzanena kuti ‘Ameneyu ndi mkazi wake.’ Tsono adzandipha ine nakusiya iwe ndi moyo. 13 Tsono udzikawawuza kuti iwe ndiwe mlongo wanga. Ukatero zidzandiyendera bwino ndipo ndidzapulumuka chifukwa cha iwe.”

14 Pamene Abramu anafika ku Igupto, Aigupto aja anaona kuti Sarai anali mkazi wokongoladi. 15 Pamene akuluakulu a ku nyumba ya Farao anamuona, anakamuyamikira pamaso pa Farao ndipo ananka naye ku nyumba ya Farao. 16 Abramu naye zinthu zinkamuyendera bwino chifukwa cha Sarai. Farao anamupatsa nkhosa, ngʼombe, abulu aamuna ndi abulu aakazi, antchito aakazi pamodzi ndi ngamira.

17 Koma Yehova anabweretsa matenda owopsa pa Farao pamodzi ndi banja lake lonse chifukwa cha Sarai mkazi wa Abramu. 18 Choncho Farao anayitanitsa Abramu namufunsa kuti, “Nʼchiyani wandichitirachi? Nʼchifukwa chiyani sunandiwuze kuti ameneyu ndi mkazi wako? 19 Nʼchifukwa chiyani unati ndi mlongo wako, mpaka ine ndinamutenga kukhala mkazi wanga? Eko mkazi wako. Mutenge uzipita!” 20 Farao analamula asilikali ake ndipo iwo anamutulutsa Abramu pamodzi ndi mkazi wake ndi zonse anali nazo.

The Call of Abram

12 The Lord had said to Abram, “Go from your country, your people and your father’s household(A) to the land(B) I will show you.(C)

“I will make you into a great nation,(D)
    and I will bless you;(E)
I will make your name great,
    and you will be a blessing.[a](F)
I will bless those who bless you,
    and whoever curses you I will curse;(G)
and all peoples on earth
    will be blessed through you.(H)[b]

So Abram went, as the Lord had told him; and Lot(I) went with him. Abram was seventy-five years old(J) when he set out from Harran.(K) He took his wife Sarai,(L) his nephew Lot, all the possessions they had accumulated(M) and the people(N) they had acquired in Harran, and they set out for the land of Canaan,(O) and they arrived there.

Abram traveled through the land(P) as far as the site of the great tree of Moreh(Q) at Shechem.(R) At that time the Canaanites(S) were in the land. The Lord appeared to Abram(T) and said, “To your offspring[c] I will give this land.(U)(V) So he built an altar there to the Lord,(W) who had appeared to him.

From there he went on toward the hills east of Bethel(X) and pitched his tent,(Y) with Bethel on the west and Ai(Z) on the east. There he built an altar to the Lord and called on the name of the Lord.(AA)

Then Abram set out and continued toward the Negev.(AB)

Abram in Egypt(AC)

10 Now there was a famine in the land,(AD) and Abram went down to Egypt to live there for a while because the famine was severe.(AE) 11 As he was about to enter Egypt, he said to his wife Sarai,(AF) “I know what a beautiful woman(AG) you are. 12 When the Egyptians see you, they will say, ‘This is his wife.’ Then they will kill me but will let you live. 13 Say you are my sister,(AH) so that I will be treated well for your sake and my life will be spared because of you.”

14 When Abram came to Egypt, the Egyptians saw that Sarai was a very beautiful woman.(AI) 15 And when Pharaoh’s officials saw her, they praised her to Pharaoh, and she was taken into his palace. 16 He treated Abram well for her sake, and Abram acquired sheep and cattle, male and female donkeys, male and female servants, and camels.(AJ)

17 But the Lord inflicted(AK) serious diseases on Pharaoh and his household(AL) because of Abram’s wife Sarai. 18 So Pharaoh summoned Abram. “What have you done to me?”(AM) he said. “Why didn’t you tell me she was your wife?(AN) 19 Why did you say, ‘She is my sister,’(AO) so that I took her to be my wife? Now then, here is your wife. Take her and go!” 20 Then Pharaoh gave orders about Abram to his men, and they sent him on his way, with his wife and everything he had.

Footnotes

  1. Genesis 12:2 Or be seen as blessed
  2. Genesis 12:3 Or earth / will use your name in blessings (see 48:20)
  3. Genesis 12:7 Or seed