Add parallel Print Page Options

Kubwezeretsedwa kwa Israeli

36 “Iwe mwana wa munthu, yankhula kwa mapiri a Israeli ndipo unene kuti, ‘Inu mapiri a Israeli, imvani mawu a Yehova.’ Ine Ambuye Yehova ndikuti: Mdani wanu ankanena kuti, ‘Aa! Dziko lamapiri lakalekale lija lasanduka lathu.’ Choncho nenera ndipo uwawuze kuti, ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Popeza anakusakazani ndi kukuponderezani ku mbali zonse motero kuti munakhala mʼmanja mwa anthu a mitundu ina yonse ndipo anthu ankakunenani ndi kukunyozani, choncho, inu mapiri a Israeli, imvani zimene Ine Ambuye Yehova ndikuwuza mapiri ndi magomo, zigwembe ndi zigwa, mabwinja ndi mizinda yosiyidwa imene yakhala ikufunkhidwa komanso kunyozedwa ndi anthu a mitundu ina okuzungulirani. Tsono Ine Ambuye Yehova ndikuti: Mu mkwiyo wanga woopsa ndinayankhula kuyimba mlandu mitundu ina yonse ya anthu makamaka a ku Edomu. Iwowa mwa chimwemwe chodzaza tsaya ndi mwa nkhwidzi analanda dziko langa ndi kulisandutsa lawo ndi kutengeratu dziko la msipu kukhala lawo.’ Nʼchifukwa chake, lengeza ku dziko la Israeli, ndipo uwuze mapiri ndi magomo, zigwembe ndi zigwa kuti, ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ine ndikuyankhula ndi mtima wokwiya kwambiri chifukwa inu munalandira chitonzo cha anthu a mitundu ina.’ Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ndikulumbira nditakweza dzanja langa kuti mitundu ya anthu idzatozedwanso.

“Koma Inu mapiri a Israeli mudzaphukanso nthambi ndipo mudzawabalira zipatso anthu anga a Israeli, pakuti ali pafupi kubwerera kwawo. Taonani, Ine ndili mbali yanu ndipo ndidzakukomerani mtima. Mudzalimidwa ndi kudzalidwa. 10 Ndidzachulukitsa chiwerengero cha anthu anu, nyumba yonse ya Israeli. Mʼmizinda mudzakhalanso anthu ndipo mabwinja adzamangidwanso. 11 Ndidzachulukitsa chiwerengero cha amuna pamodzi ndi ziweto zomwe, ndipo adzachuluka kwambiri ndi kubereka ana ambiri. Ndidzakhazika anthu mʼdzikomo monga analili kale, ndi kukulemeretsani kuposa kale. Pamenepo inu mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova. 12 Ndidzachititsa anthu kuyenda pa inu, ndiye kuti inu anthu anga Aisraeli. Iwowo adzakhazikika pa inu, ndipo inu mudzakhala cholowa chawo. Simudzalandanso ana awo.

13 “Ine Ambuye Yehova ndikuti: Popeza anthu amanena kuti, ndiwe dziko limene limadya anthu ake ‘kulanda ana a mtundu wake,’ 14 nʼchifukwa chake, simudzadyanso anthu kapena kulanda ana a mtundu wako. Ine Ambuye Yehova ndikutero. 15 Sindidzakulolaninso kumva mnyozo wa anthu a mitundu ina, kapena kupirira kunyogodola kwawo kapenanso kupunthwitsanso anthu a mʼdziko lako. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.”

16 Yehova anandiyankhulanso kuti: 17 “Iwe mwana wa munthu, pamene anthu a Israeli ankakhala mʼdziko lawolawo, analiyipitsa ndi makhalidwe awo ndiponso zochita zawo. Machitidwe awo pamaso panga anali onyansa pa zachipembedzo ngati msambo wa mkazi amene ali pa nthawi yake. 18 Tsono ndinawalanga chifukwa cha magazi amene anakhetsa mʼdzikomo, ndiponso chifukwa anayipitsa dziko ndi mafano awo. 19 Ndinawamwaza pakati pa anthu a mitundu ina ndipo anabalalikira mʼmayiko onse. Ndinawalanga molingana ndi makhalidwe awo ndi zochita zawo. 20 Atafika kwa anthu a mitundu ina, kulikonse kumene anapitako, anayipitsa dzina langa loyera. Zinatero popeza anthu ponena za iwo ankanena kuti, ‘Awa ndi anthu a Yehova, komatu anachotsedwa ku dziko lake.’ 21 Koma Ine ndinkadera nkhawa dzina langa loyera, limene Aisraeli analiyipitsa pakati pa anthu a mitundu ina kumene anapitako.

22 “Nʼchifukwa chake awuze Aisraeliwo kuti Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ine ndidzachita zimene ndidzachitezo osati chifukwa cha inuyo Aisraelinu ayi, koma chifukwa cha dzina langa, limene mwaliyipitsa pakati pa anthu a mitundu ina kumene munapitako. 23 Ndidzaonetsa chiyero cha dzina langa lotchuka, limene layipitsidwa pakati pawo. Anthu a mitundu inayo atadzazindikira kuti ndaonetsa kudzera mwa inu kuti dzina langa ndi loyera, iwo adzadziwanso kuti Ine ndine Yehova. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.

24 “Pakuti Ine ndidzakuchotsani pakati pa anthu a mitundu ina. Ndidzakusonkhanitsani kuchoka ku mayiko onse ndi kukubwezerani ku dziko lanulanu. 25 Ndidzakuwazani madzi oyera, ndipo mudzakhala oyera mtima. Zonse zimene zimakuyipitsani zidzachoka. Ndidzakuyeretsani pochotsa mafano anu onse. 26 Ndidzakupatsani mtima watsopano ndi kulowetsa mzimu watsopano mwa inu. Ndidzachotsa mwa inu mtima wanu wowuma ngati mwala ndi kukupatsani mtima wofewa ngati mnofu. 27 Ndipo ndidzayika Mzimu wanga mwa inu ndipo ndidzakuthandizani kutsatira malangizo anga ndi kukusungitsani mosamala kwambiri malamulo anga. 28 Mudzakhala mʼdziko limene ndinapatsa makolo anu. Mudzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wanu. 29 Ndidzakupulumutsani ku zonse zokuyipitsani. Ndidzakuchulukitsirani tirigu ndipo sindidzakugwetseraninso njala. 30 Ndidzachulukitsa zipatso za mʼmitengo yanu ndi zokolola za mʼmunda mwanu, kotero kuti simudzanyozedwanso pakati pa anthu a mitundu ina chifukwa cha njala. 31 Pamenepo mudzakumbukira makhalidwe anu oyipa ndi ntchito zanu zoyipa. Machimo anu ndi ntchito zanu zonyansa zidzakuchititsa nokha manyazi. 32 Tsono dziwani kuti Ine sindidzachita zimenezi chifukwa cha inuyo ayi, ndikutero Ine Ambuye Wamphamvuzonse. Ndiyetu chitani manyazi ndipo mugwetse nkhope zanu, inu Aisraeli chifukwa cha makhalidwe anu!

33 “Ine Ambuye Yehova ndikuti: Pa tsiku limene ndidzayeretse machimo anu onse, ndidzayikamonso anthu mʼmizinda yanu, ndipo ndidzamanganso nyumba pa mabwinja. 34 Dziko limene linasanduka chipululu lizidzalimidwanso. Mʼmalo moti aliyense wopitamo alione dzikolo ngati chipululu tsopano adzaliona lolimidwa. 35 Iwo adzati, ‘Dziko ili, limene linali chipululu, lasanduka munda wa Edeni. Mizinda imene inali mabwinja osiyidwa ndi owonongedwa, tsopano ndi yotetezedwa ndi yokhalamo anthu. 36 Ndipo anthu a mitundu ina okhala pafupi nanu amene anatsala adzadziwa kuti Ine Yehova ndine amene ndinamanganso mizinda yowonongeka ndi kudzalanso zinthu zatsopano mʼmalo mʼmene munali chipululu. Ine Yehova ndayankhula ndipo ndidzazichitadi.’

37 “Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ndidzalolanso Aisraeli kuti andipemphe zoti ndiwachitire: Ndidzachulukitsa anthu awo ngati nkhosa. 38 Adzachulukadi ngati nkhosa zomwe ankapereka ngati nsembe ku Yerusalemu pa nthawi za chikondwerero. Choncho mizinda ya mabwinja idzadzaza ndi anthu. Zikadzatero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”

Hope for the Mountains of Israel

36 “Son of man, prophesy to the mountains of Israel(A) and say, ‘Mountains of Israel, hear the word of the Lord. This is what the Sovereign Lord says:(B) The enemy said of you, “Aha!(C) The ancient heights(D) have become our possession.(E)”’ Therefore prophesy and say, ‘This is what the Sovereign Lord says: Because they ravaged(F) and crushed you from every side so that you became the possession of the rest of the nations and the object of people’s malicious talk and slander,(G) therefore, mountains of Israel, hear the word of the Sovereign Lord: This is what the Sovereign Lord says to the mountains and hills, to the ravines and valleys,(H) to the desolate ruins(I) and the deserted(J) towns that have been plundered and ridiculed(K) by the rest of the nations around you(L) this is what the Sovereign Lord says: In my burning(M) zeal I have spoken against the rest of the nations, and against all Edom, for with glee and with malice in their hearts they made my land their own possession so that they might plunder its pastureland.’(N) Therefore prophesy concerning the land of Israel and say to the mountains and hills, to the ravines and valleys: ‘This is what the Sovereign Lord says: I speak in my jealous wrath because you have suffered the scorn of the nations.(O) Therefore this is what the Sovereign Lord says: I swear with uplifted hand(P) that the nations around you will also suffer scorn.(Q)

“‘But you, mountains of Israel, will produce branches and fruit(R) for my people Israel, for they will soon come home. I am concerned for you and will look on you with favor; you will be plowed and sown,(S) 10 and I will cause many people to live on you—yes, all of Israel. The towns will be inhabited and the ruins(T) rebuilt.(U) 11 I will increase the number of people and animals living on you, and they will be fruitful(V) and become numerous. I will settle people(W) on you as in the past(X) and will make you prosper more than before.(Y) Then you will know that I am the Lord. 12 I will cause people, my people Israel, to live on you. They will possess you, and you will be their inheritance;(Z) you will never again deprive them of their children.

13 “‘This is what the Sovereign Lord says: Because some say to you, “You devour people(AA) and deprive your nation of its children,” 14 therefore you will no longer devour people or make your nation childless, declares the Sovereign Lord. 15 No longer will I make you hear the taunts of the nations, and no longer will you suffer the scorn of the peoples or cause your nation to fall, declares the Sovereign Lord.(AB)’”

Israel’s Restoration Assured

16 Again the word of the Lord came to me: 17 “Son of man, when the people of Israel were living in their own land, they defiled it by their conduct and their actions. Their conduct was like a woman’s monthly uncleanness(AC) in my sight.(AD) 18 So I poured out(AE) my wrath on them because they had shed blood in the land and because they had defiled it with their idols. 19 I dispersed them among the nations, and they were scattered(AF) through the countries; I judged them according to their conduct and their actions.(AG) 20 And wherever they went among the nations they profaned(AH) my holy name, for it was said of them, ‘These are the Lord’s people, and yet they had to leave his land.’(AI) 21 I had concern for my holy name, which the people of Israel profaned among the nations where they had gone.(AJ)

22 “Therefore say to the Israelites, ‘This is what the Sovereign Lord says: It is not for your sake, people of Israel, that I am going to do these things, but for the sake of my holy name,(AK) which you have profaned(AL) among the nations where you have gone.(AM) 23 I will show the holiness of my great name,(AN) which has been profaned(AO) among the nations, the name you have profaned among them. Then the nations will know that I am the Lord,(AP) declares the Sovereign Lord, when I am proved holy(AQ) through you before their eyes.(AR)

24 “‘For I will take you out of the nations; I will gather you from all the countries and bring you back into your own land.(AS) 25 I will sprinkle(AT) clean water on you, and you will be clean; I will cleanse(AU) you from all your impurities(AV) and from all your idols.(AW) 26 I will give you a new heart(AX) and put a new spirit in you; I will remove from you your heart of stone(AY) and give you a heart of flesh.(AZ) 27 And I will put my Spirit(BA) in you and move you to follow my decrees(BB) and be careful to keep my laws.(BC) 28 Then you will live in the land I gave your ancestors; you will be my people,(BD) and I will be your God.(BE) 29 I will save you from all your uncleanness. I will call for the grain and make it plentiful and will not bring famine(BF) upon you. 30 I will increase the fruit of the trees and the crops of the field, so that you will no longer suffer disgrace among the nations because of famine.(BG) 31 Then you will remember your evil ways and wicked deeds, and you will loathe yourselves for your sins and detestable practices.(BH) 32 I want you to know that I am not doing this for your sake, declares the Sovereign Lord. Be ashamed(BI) and disgraced for your conduct, people of Israel!(BJ)

33 “‘This is what the Sovereign Lord says: On the day I cleanse(BK) you from all your sins, I will resettle your towns, and the ruins(BL) will be rebuilt.(BM) 34 The desolate land will be cultivated instead of lying desolate in the sight of all who pass through it. 35 They will say, “This land that was laid waste has become like the garden of Eden;(BN) the cities that were lying in ruins, desolate and destroyed, are now fortified and inhabited.(BO) 36 Then the nations around you that remain will know that I the Lord have rebuilt what was destroyed and have replanted what was desolate. I the Lord have spoken, and I will do it.’(BP)

37 “This is what the Sovereign Lord says: Once again I will yield to Israel’s plea(BQ) and do this for them: I will make their people as numerous as sheep,(BR) 38 as numerous as the flocks for offerings(BS) at Jerusalem during her appointed festivals. So will the ruined cities be filled with flocks of people. Then they will know that I am the Lord.(BT)