Add parallel Print Page Options

Mwambo Wopatula Ansembe

29 “Pofuna kumupatula Aaroni ndi ana ake kuti akhale ansembe onditumikira Ine, uchite izi: Utenge ngʼombe yayingʼono yayimuna ndi nkhosa ziwiri zazimuna zopanda chilema. Utengenso buledi wopanda yisiti, makeke wopanda yisiti wopakidwa mafuta. Zonsezi uzipange ndi ufa wosalala wa tirigu. Uziyike mʼdengu ndipo ubwere nazo kwa Ine pamodzi ndi ngʼombe yayimuna ija ndi nkhosa ziwiri zazimuna zija. Kenaka ubwere naye Aaroni ndi ana ake pa khomo la tenti ya msonkhano ndipo uwasambitse ndi madzi. Tenga zovala ndipo umuveke Aaroni mwinjiro, mkanjo wa efodi, efodiyo ndi chovala chapachifuwa. Umumange mʼchiwuno lamba wa efodi wolukidwa mwaluso uja. Umuveke nduwira kumutu, ndiponso uyike chizindikiro chopatulika chija pa nduwirayo. Utenge mafuta wodzozera ndipo uwatsanulire pamutu pake kumudzoza. Ubwere ndi ana ake aamuna ndipo uwavekenso minjiro ndi nduwira. Kenaka umange malamba Aaroniyo pamodzi ndi ana ake ndi kuwaveka nduwira. Motero unsembe udzakhala wawo malingana ndi lamulo ili losatha.

“Umu ndi mmene udzadzozere Aaroni ndi ana ake aamuna.

10 “Ubwere ndi ngʼombe yayimuna pa khomo la tenti ya msonkhano ndipo Aaroni ndi ana ake asanjike manja awo pamutu pake. 11 Uphe ngʼombeyo pamaso pa Yehova pa khomo la tenti ya msonkhano. 12 Utenge magazi ena angʼombeyo ndi kupaka ndi chala chako pa nyanga zaguwa lansembe ndipo magazi otsalawo uwakhutulire pa tsinde laguwalo. 13 Kenaka utenge mafuta onse okuta matumbo, mafuta ophimba chiwindi ndiponso impsyo zonse ziwiri pamodzi ndi mafuta ake. Zonsezi uzitenthe pa guwapo. 14 Koma nyama yangʼombeyo, chikopa chake ndi matumbo ake uziwotche kunja kwa msasa. Iyi ndi nsembe yopepesera machimo.

15 “Utenge nkhosa yayimuna imodzi ndipo Aaroni ndi ana ake aamuna asanjike manja awo pamutu pake. 16 Uyiphe ndipo utenge magazi ake ndi kuwaza mbali zonse zaguwalo. 17 Uyidule nkhosayo nthulinthuli, kutsuka matumbo ake ndi miyendo yake. Ukatero, pamodzi ndi mutu wake, uziyike pamwamba pa nthulizo. 18 Ndipo uwotche nkhosa yonseyo pa guwa lansembe. Iyi ndi nsembe yopsereza ya kwa Yehova. Ili ndi fungo lokoma, loperekedwa pa moto kwa Yehova.

19 “Utenge nkhosa yayimuna ina ndipo Aaroni ndi ana ake aamuna asanjike manja awo pamutu pake. 20 Uyiphe ndipo utenge magazi ake ena ndi kupaka ndewere za makutu a kudzanja lamanja la Aaroni ndi ana ake aamuna. Upakenso pa zala zawo zazikulu za kudzanja lawo lamanja, ndi zala zazikulu za kuphazi lakudzanja lawo lamanja. Kenaka uwaze magazi otsalawo mbali zonse za guwalo. 21 Ndipo utenge magazi ena amene ali pa guwa lansembe komanso pa mafuta ena odzozera ndipo uwawaze pa Aaroni ndi zovala zake ndi ana ake ndi zovala zawo. Ndiye kuti iyeyo ndi ana ake aamuna adzakhala opatulika pamodzi ndi zovala zawo.

22 “Pa nkhosa yayimuna ija utengepo mafuta ake, mafuta a ku mchira wake, mafuta okuta matumbo, mafuta okuta chiwindi, impsyo zonse ziwiri ndi mafuta ake, ndiponso ntchafu yakumanja. Iyi ndi nkhosa ya mwambo wodzoza. 23 Utengenso mʼdengu la buledi wopanda yisiti limene lili pamaso pa Yehova, buledi mmodzi, buledi wokhala ndi mafuta a olivi, ndi buledi wopyapyala mmodzi. 24 Izi zonse uzipereke mʼmanja mwa Aaroni ndi ana ake, ndipo iwo aziweyule pamaso pa Yehova kuti zikhale nsembe yoweyula. 25 Kenaka uzitenge mʼmanja mwawo ndipo uzipsereze pa guwa lansembe, pamwamba penipeni pamodzi ndi nsembe yopsereza kuti ipereke fungo lokoma kwa Yehova. Ichi ndiye chopereka chachakudya kwa Yehova. 26 Kenaka utenge chidale cha nkhosa yayimuna imene inaperekedwa pamwambo wodzoza Aaroni, uchiweyule kuti chikhale nsembe yoweyula pamaso pa Yehova ndipo chidzakhala gawo lako.

27 “Uzipatule ziwalo zonse za nkhosa ya pa mwambo wodzoza Aaroni ndi ana ake. Chidale chimene unaweyula chija ndiponso ntchafu imene inaperekedwa ija. 28 Nsembe izi ndi zimene Aisraeli azipereka kwa Aaroni ndi ana ake mwa zonse zimene azipereka nthawi zonse. Mwa zopereka za mtendere zimene ana a Aisraeli adzapereka kwa Yehova, zimenezi zikhale gawo lawo.

29 “Zovala zopatulika za Aaroni zidzakhala za ana ake aamuna iye atafa kuti adzavale podzozedwa ndi polandira udindo wawo. 30 Mwana amene adzalowa mʼmalo mwake monga wansembe pamene adzabwerera kudzalowa mu tenti ya msonkhano kudzatumikira ku malo wopatulika, adzavala zovala zimenezi masiku asanu ndi awiri.

31 “Utenge nkhosa yayimuna ya pamwambo wodzoza ansembe ndipo uyiphike pamalo opatulika. 32 Aaroni ndi ana ake adye nyama ya nkhosa yayimunayi pamodzi ndi buledi amene ali mʼdengu pa khomo la tenti ya msonkhano. 33 Adye zonse zimene anazipereka kwa Yehova pamwambo wopepesera machimo powadzoza ndi kuwapatula. Munthu wamba asadye chifukwa ndi zopatulika. 34 Ndipo ngati nyama ina ya nkhosa ya pamwambo wodzoza ansembe kapena buledi zatsala mpaka mmawa, muziwotche, asazidye chifukwa ndi zopatulika.

35 “Uchitire Aaroni ndi ana ake aamuna zonse zimene ndakulamulazi. Uchite mwambo wowapatula kukhala ansembe masiku asanu ndi awiri. 36 Tsiku lililonse uzipereka ngʼombe yayimuna ngati nsembe yopepesera machimo kuti machimowo akhululukidwe. Ndiponso upatule guwalo popereka nsembe yopepesera ndi kulidzoza mafuta kuti likhale lopatulika. 37 Pa masiku asanu ndi awiri uzipereka pa guwapo nsembe zoyeretsera guwalo, ukatero ndiye kuti uzilipatula. Ndipo guwa lansembelo lidzakhala loyera kwambiri, ndipo chilichonse chimene chidzakhudza guwalo chidzayeretsedwa.

38 “Tsiku ndi tsiku pa guwa lansembe uzipereka izi: Ana ankhosa a chaka chimodzi awiri. 39 Mmawa muzipereka mwana wankhosa mmodzi ndipo winayo madzulo. 40 Pamodzi ndi mwana wankhosa woyambayo, muzipereka kilogalamu imodzi ya ufa wosalala wosakaniza ndi lita imodzi ya mafuta a olivi pamodzi ndi lita imodzi ya vinyo ngati chopereka chachakumwa. 41 Upereke mwana wankhosa winayo madzulo pamodzi ndi chopereka chachakudya monga poyamba paja ndi chopereka chachakumwa monga mmawa kuti ikhale fungo lokoma la chopereka chachakudya kwa Yehova.

42 “Zopereka zopsereza zimenezi ziziperekedwa nthawi zonse, pa mibado yonse. Muzidzazipereka pamaso pa Yehova pa khomo la tenti ya msonkhano. Pa guwa lansembe, Yehova adzakumana nanu ndi kuyankhula nanu. 43 Pameneponso Ine ndidzakumana ndi Aisraeli, ndipo guwalo lidzakhala lopatulika chifukwa cha ulemerero wanga.

44 “Tsono Ine ndidzapatula tenti ya msonkhano ndi guwa lansembe. Ndidzapatulanso Aaroni pamodzi ndi ana ake kuti akhale ansembe anga onditumikira. 45 Ndidzakhala pakati pa Aisraeli ndikukhala Mulungu wawo. 46 Adzadziwa kuti ine ndine Mulungu wawo amene ndinawatulutsa mʼdziko la Igupto kuti ndikhale pakati pawo. Ine ndine Yehova, Mulungu wawo.”

Consecration of the Priests(A)

29 “This is what you are to do to consecrate(B) them, so they may serve me as priests: Take a young bull and two rams without defect.(C) And from the finest wheat flour make round loaves without yeast, thick loaves without yeast and with olive oil mixed in, and thin loaves without yeast and brushed with olive oil.(D) Put them in a basket and present them along with the bull and the two rams.(E) Then bring Aaron and his sons to the entrance to the tent of meeting and wash them with water.(F) Take the garments(G) and dress Aaron with the tunic, the robe of the ephod, the ephod itself and the breastpiece. Fasten the ephod on him by its skillfully woven waistband.(H) Put the turban(I) on his head and attach the sacred emblem(J) to the turban. Take the anointing oil(K) and anoint him by pouring it on his head. Bring his sons and dress them in tunics(L) and fasten caps on them. Then tie sashes on Aaron and his sons.[a](M) The priesthood is theirs by a lasting ordinance.(N)

“Then you shall ordain Aaron and his sons.

10 “Bring the bull to the front of the tent of meeting, and Aaron and his sons shall lay their hands on its head.(O) 11 Slaughter it in the Lord’s presence(P) at the entrance to the tent of meeting. 12 Take some of the bull’s blood and put it on the horns(Q) of the altar with your finger, and pour out the rest of it at the base of the altar.(R) 13 Then take all the fat(S) on the internal organs,(T) the long lobe of the liver, and both kidneys with the fat on them, and burn them on the altar. 14 But burn the bull’s flesh and its hide and its intestines(U) outside the camp.(V) It is a sin offering.[b]

15 “Take one of the rams,(W) and Aaron and his sons shall lay their hands on its head.(X) 16 Slaughter it and take the blood and splash it against the sides of the altar. 17 Cut the ram into pieces and wash(Y) the internal organs and the legs, putting them with the head and the other pieces. 18 Then burn the entire ram on the altar. It is a burnt offering to the Lord, a pleasing aroma,(Z) a food offering presented to the Lord.

19 “Take the other ram,(AA) and Aaron and his sons shall lay their hands on its head.(AB) 20 Slaughter it, take some of its blood and put it on the lobes of the right ears of Aaron and his sons, on the thumbs of their right hands, and on the big toes of their right feet.(AC) Then splash blood against the sides of the altar.(AD) 21 And take some blood(AE) from the altar and some of the anointing oil(AF) and sprinkle it on Aaron and his garments and on his sons and their garments. Then he and his sons and their garments will be consecrated.(AG)

22 “Take from this ram the fat,(AH) the fat tail, the fat on the internal organs, the long lobe of the liver, both kidneys with the fat on them, and the right thigh. (This is the ram for the ordination.) 23 From the basket of bread made without yeast, which is before the Lord, take one round loaf, one thick loaf with olive oil mixed in, and one thin loaf. 24 Put all these in the hands of Aaron and his sons and have them wave them before the Lord as a wave offering.(AI) 25 Then take them from their hands and burn them on the altar along with the burnt offering for a pleasing aroma to the Lord, a food offering presented to the Lord.(AJ) 26 After you take the breast of the ram for Aaron’s ordination, wave it before the Lord as a wave offering, and it will be your share.(AK)

27 “Consecrate those parts of the ordination ram that belong to Aaron and his sons:(AL) the breast that was waved and the thigh that was presented. 28 This is always to be the perpetual share from the Israelites for Aaron and his sons. It is the contribution the Israelites are to make to the Lord from their fellowship offerings.(AM)

29 “Aaron’s sacred garments(AN) will belong to his descendants so that they can be anointed and ordained in them.(AO) 30 The son(AP) who succeeds him as priest and comes to the tent of meeting to minister in the Holy Place is to wear them seven days.

31 “Take the ram(AQ) for the ordination and cook the meat in a sacred place.(AR) 32 At the entrance to the tent of meeting, Aaron and his sons are to eat the meat of the ram and the bread(AS) that is in the basket. 33 They are to eat these offerings by which atonement was made for their ordination and consecration. But no one else may eat(AT) them, because they are sacred. 34 And if any of the meat of the ordination ram or any bread is left over till morning,(AU) burn it up. It must not be eaten, because it is sacred.

35 “Do for Aaron and his sons everything I have commanded you, taking seven days to ordain them. 36 Sacrifice a bull each day(AV) as a sin offering to make atonement(AW). Purify the altar by making atonement for it, and anoint it to consecrate(AX) it. 37 For seven days make atonement for the altar and consecrate it. Then the altar will be most holy, and whatever touches it will be holy.(AY)

38 “This is what you are to offer on the altar regularly each day:(AZ) two lambs a year old. 39 Offer one in the morning and the other at twilight.(BA) 40 With the first lamb offer a tenth of an ephah[c] of the finest flour mixed with a quarter of a hin[d] of oil(BB) from pressed olives, and a quarter of a hin of wine as a drink offering.(BC) 41 Sacrifice the other lamb at twilight(BD) with the same grain offering(BE) and its drink offering as in the morning—a pleasing aroma, a food offering presented to the Lord.

42 “For the generations to come(BF) this burnt offering is to be made regularly(BG) at the entrance to the tent of meeting,(BH) before the Lord. There I will meet you and speak to you;(BI) 43 there also I will meet with the Israelites, and the place will be consecrated by my glory.(BJ)

44 “So I will consecrate the tent of meeting and the altar and will consecrate Aaron and his sons to serve me as priests.(BK) 45 Then I will dwell(BL) among the Israelites and be their God.(BM) 46 They will know that I am the Lord their God, who brought them out of Egypt(BN) so that I might dwell among them. I am the Lord their God.(BO)

Footnotes

  1. Exodus 29:9 Hebrew; Septuagint on them
  2. Exodus 29:14 Or purification offering; also in verse 36
  3. Exodus 29:40 That is, probably about 3 1/2 pounds or about 1.6 kilograms
  4. Exodus 29:40 That is, probably about 1 quart or about 1 liter