Add parallel Print Page Options

Apirikitsa Mitundu Ina ya Anthu

Pamene Yehova Mulungu wanu wakufikitsani mʼdziko limene mukukalowa ndi kulilanda ndi kuthamangitsa pamaso panu mitundu ya anthu iyi: Ahiti, Agirigasi, Aamori, Akanaani, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi; yomwe ndi mitundu isanu ndi iwiri yayikulu ndi yamphamvu kuposa inu; Yehova Mulungu wanu akadzawapereka mʼmanja mwanu, ndipo inu mukadzawagonjetsa, mudzawawononge kwathunthu. Musadzachite mgwirizano ndi anthuwo ndiponso musadzawachitire chifundo. Musadzakwatirane nawo. Musadzapereke ana anu aakazi kwa ana awo aamuna kapena kutenga ana anu aamuna ndi kuwapereka kwa ana awo aakazi. Mukadzatero, iwo adzasocheretsa ana anu aamuna kuti asanditsatire ndi kutumikira milungu ina. Motero Yehova adzakukwiyirani ndi kukuwonongani mwachangu. Koma mukachite izi: Mukagumule maguwa awo ansembe, mukaswe miyala yawo yachipembedzo, mukadule mitengo yawo ya Asera, ndi kutentha mafano awo pa moto. Pakuti inu ndinu anthu opatulika kwa Yehova Mulungu wanu. Yehova Mulungu wanu anakusankhani pakati pa anthu onse pa dziko lapansi kuti mukhale ake, chuma chake cha mtengo wapatali.

Yehova sanakukondeni chifukwa choti munali ochuluka kuposa ena pakuti inuyo ndiye munali ochepetsetsa mwa anthu onse. Koma chifukwa chakuti Yehova anakukondani nasunga lumbiro lake limene analumbira kwa makolo anu. Ndi chifukwa chake anakutulutsani ndi mphamvu yake yopanda malire ndi kukupulumutsani ku dziko la ukapolo, kuchoka mʼmanja mwa Farao mfumu ya ku Igupto. Choncho dziwani kuti Yehova Mulungu wanu, ndi Mulungu. Iye ndi Mulungu wokhulupirika, wosunga pangano lake la chikondi chosasinthika ku mibadomibado, kwa iwo amene amamukonda nasunga malamulo ake. 10 Koma

iwo amene amamuda adzawabwezera powawononga pamaso pawo;
    sadzachedwa kuwabwezera iwo amene amadana naye.

11 Choncho muziyesetsa kusunga malamulo, malangizo ndi maphunziro amene ndikukulamulani lero lino kuti muchite.

12 Mukamvera malamulo amenewa, ndi kusamala kuwatsata, ndiye kuti Yehova Mulungu wanu adzasunga pangano lake la chikondi chosasinthika ndi inu, monga analumbira kwa makolo anu. 13 Iye adzakukondani nakudalitsani ndi kukuchulukitsani. Adzadalitsa chipatso cha mʼmimba mwanu, zokolola za mʼdziko mwanu, tirigu wanu, vinyo wanu ndi mafuta anu, ana angʼombe zanu ndi ana ankhosa zanu mʼdziko limene analumbirira kwa makolo anu kuti akupatseni inu. 14 Inu mudzadalitsika kuposa mtundu wina uliwonse wa anthu ndipo palibe mwamuna kapena mkazi aliyense pakati panu amene adzakhale wosabereka. Ziweto zanu nazonso, sipadzapezeka zosabereka. 15 Yehova adzakupewetsani ku matenda aliwonse. Sadzakugwetserani matenda owopsa aja munawadziwa ku Igupto, koma adzawagwetsera pa odana nanu. 16 Muwononge anthu onse amene Yehova Mulungu wanu awapereka kwa inu. Musawamvere chisoni ndipo musatumikire milungu yawo pakuti umenewo udzakhala msampha kwa inu.

17 Mukhoza kunena kuti, “Anthu awa ndi amphamvu kuposa ifeyo. Nanga tingawapirikitse bwanji?” 18 Koma musachite nawo mantha, kumbukirani bwino zimene Yehova Mulungu wanu anachita ndi Farao pamodzi ndi Igupto yense. 19 Munadzionera nokha ndi maso anu mayesero aakulu, zizindikiro zozizwitsa ndi zodabwitsa, mphamvu yake yopanda malire imene Yehova Mulungu wanu anakutulutsirani. Yehova Mulungu adzachita zimenezo ndi anthu onse amene muwaopa tsopano. 20 Kuwonjezera apo, Yehova Mulungu wanu adzatumiza mavu pakati pawo mpaka atamaliza onse amene adzakubisalirani. 21 Musaopsedwe nawo pakuti Yehova Mulungu wanu, amene ali pakati panu, ndi Mulungu wamkulu ndi woopsa. 22 Yehova Mulungu wanu adzapirikitsa anthu a mitundu yonse pamaso panu, pangʼonopangʼono. Sadzakulolani kuti muwathe nthawi imodzi, kuti nyama zakuthengo zingadzaswane mokuzungulirani. 23 Koma Yehova Mulungu wanu adzawapereka kwa inu, adzawasokoneza kufikira atawonongedwa. 24 Iye adzapereka mafumu awo mʼdzanja lanu, ndipo adzafafaniza mayina awo pa dziko lapansi. Palibe amene adzalimbana nanu, inu mudzawawononga. 25 Muwawotche pa moto mafano a milungu yawo. Musasirire siliva ndi golide amene ali pa mafanoyo. Musamutenge kuti akhale wanu chifukwa mukatero mudzakodwa naye ngati msampha, pakuti Yehova Mulungu wanu amanyansidwa nazo. 26 Musabweretse chinthu chonyansa mʼnyumba mwanu kuopa kuwonongedwa ngati chonyasacho. Muziyipidwa ndi kunyansidwa nacho kwambiri pakuti chidzawonongedwanso.

Driving Out the Nations

When the Lord your God brings you into the land you are entering to possess(A) and drives out before you many nations(B)—the Hittites,(C) Girgashites,(D) Amorites,(E) Canaanites, Perizzites,(F) Hivites(G) and Jebusites,(H) seven nations larger and stronger than you— and when the Lord your God has delivered(I) them over to you and you have defeated them, then you must destroy(J) them totally.[a](K) Make no treaty(L) with them, and show them no mercy.(M) Do not intermarry with them.(N) Do not give your daughters to their sons or take their daughters for your sons, for they will turn your children away from following me to serve other gods,(O) and the Lord’s anger will burn against you and will quickly destroy(P) you. This is what you are to do to them: Break down their altars, smash their sacred stones, cut down their Asherah poles[b](Q) and burn their idols in the fire.(R) For you are a people holy(S) to the Lord your God.(T) The Lord your God has chosen(U) you out of all the peoples on the face of the earth to be his people, his treasured possession.(V)

The Lord did not set his affection on you and choose you because you were more numerous(W) than other peoples, for you were the fewest(X) of all peoples.(Y) But it was because the Lord loved(Z) you and kept the oath he swore(AA) to your ancestors that he brought you out with a mighty hand(AB) and redeemed(AC) you from the land of slavery,(AD) from the power of Pharaoh king of Egypt. Know therefore that the Lord your God is God;(AE) he is the faithful God,(AF) keeping his covenant of love(AG) to a thousand generations(AH) of those who love him and keep his commandments.(AI) 10 But

those who hate him he will repay to their face by destruction;
    he will not be slow to repay to their face those who hate him.(AJ)

11 Therefore, take care to follow the commands, decrees and laws I give you today.

12 If you pay attention to these laws and are careful to follow them, then the Lord your God will keep his covenant of love with you, as he swore to your ancestors.(AK) 13 He will love you and bless you(AL) and increase your numbers.(AM) He will bless the fruit of your womb,(AN) the crops of your land—your grain, new wine(AO) and olive oil(AP)—the calves of your herds and the lambs of your flocks in the land he swore to your ancestors to give you.(AQ) 14 You will be blessed more than any other people; none of your men or women will be childless, nor will any of your livestock be without young.(AR) 15 The Lord will keep you free from every disease.(AS) He will not inflict on you the horrible diseases you knew in Egypt,(AT) but he will inflict them on all who hate you.(AU) 16 You must destroy all the peoples the Lord your God gives over to you.(AV) Do not look on them with pity(AW) and do not serve their gods,(AX) for that will be a snare(AY) to you.

17 You may say to yourselves, “These nations are stronger than we are. How can we drive them out?(AZ) 18 But do not be afraid(BA) of them; remember well what the Lord your God did to Pharaoh and to all Egypt.(BB) 19 You saw with your own eyes the great trials, the signs and wonders, the mighty hand(BC) and outstretched arm, with which the Lord your God brought you out. The Lord your God will do the same to all the peoples you now fear.(BD) 20 Moreover, the Lord your God will send the hornet(BE) among them until even the survivors who hide from you have perished. 21 Do not be terrified by them, for the Lord your God, who is among you,(BF) is a great and awesome God.(BG) 22 The Lord your God will drive out those nations before you, little by little.(BH) You will not be allowed to eliminate them all at once, or the wild animals will multiply around you. 23 But the Lord your God will deliver them over to you, throwing them into great confusion until they are destroyed.(BI) 24 He will give their kings(BJ) into your hand,(BK) and you will wipe out their names from under heaven. No one will be able to stand up against you;(BL) you will destroy them.(BM) 25 The images of their gods you are to burn(BN) in the fire. Do not covet(BO) the silver and gold on them, and do not take it for yourselves, or you will be ensnared(BP) by it, for it is detestable(BQ) to the Lord your God. 26 Do not bring a detestable thing into your house or you, like it, will be set apart for destruction.(BR) Regard it as vile and utterly detest it, for it is set apart for destruction.

Footnotes

  1. Deuteronomy 7:2 The Hebrew term refers to the irrevocable giving over of things or persons to the Lord, often by totally destroying them; also in verse 26.
  2. Deuteronomy 7:5 That is, wooden symbols of the goddess Asherah; here and elsewhere in Deuteronomy