Add parallel Print Page Options

Konda Yehova Mulungu Wako

Awa ndi malamulo, malangizo ndi ziphunzitso zimene Yehova Mulungu wanu anandilamula kuti ndikuphunzitseni kuti mukawatsatire mʼdziko limene mukuwolokera Yorodani kuti mukalitenge, kuti inuyo, ana anu, ndi zidzukulu zanu mʼtsogolomo mudzaope Yehova Mulungu wanu moyo wanu wonse posunga malangizo ndi malamulo ake onse amene ndinakupatsani inu kuti musangalale ndi moyo wautali. Mvera Israeli ndipo usamalitse kuchita malamulowa kuti zinthu zikuyendere bwino mʼdziko ndi kuti muchuluke kwambiri mʼdziko loyenda mkaka ndi uchi monga momwe Yehova Mulungu wa makolo anu anakulonjezerani.

Tamvani inu Aisraeli, Yehova Mulungu wathu, Yehova ndi mmodzi. Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu zako zonse. Malamulo amene ndakupatsani lero ayenera kukhala mu mtima mwanu. Muziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu. Muzikamba za malamulowa pamene muli mʼnyumba zanu, pamene mukuyenda mʼnjira, pamene mukugona ndi pamene mukudzuka. Muwamange ngati zizindikiro pa manja anu ndi kuwamangirira pa zipumi zanu. Muwalembe pa mphuthu za nyumba zanu ndi pa zipata zanu.

10 Pamene Yehova Mulungu wanu akukulowetsani ndi kukupatsani dziko limene analumbirira makolo anu Abrahamu, Isake ndi Yakobo, dziko lokhala ndi mizinda ikuluikulu imene inu simunamange, 11 nyumba zodzaza ndi zinthu za mitundu yonse zimene inu simunayikemo, zitsime zimene inu simunakumbe, minda ya mpesa ndi mitengo ya olivi zimene inuyo simunadzale, tsono mukadya ndi kukhuta, 12 samalani kuti mungayiwale Yehova amene anakutulutsani ku Igupto, kukuchotsani mu ukapolo.

13 Muziopa Yehova Mulungu wanu ndi kumutumikira Iye yekha, ndipo muzilumbira pa dzina lake. 14 Musamatsatire milungu ina, milungu ya anthu ena okuzungulirani, 15 pakuti Yehova Mulungu wanu amene ali pakati panu, ndi Mulungu wansanje ndipo adzakukwiyirani kwambiri ndi kukuwonongani, kukufafanizani mʼdziko. 16 Musamuyese Yehova Mulungu wanu monga munachitira ku Masa. 17 Onetsetsani kuti mukusunga malamulo a Yehova Mulungu wanu, malangizo ake ndi zikhazikitso zake zimene anakulamulirani. 18 Chitani zoyenera ndi zabwino pamaso pa Yehova, kuti zikuyendereni bwino ndi kuti mukhoza kukalowa ndi kulanda dziko labwinolo limene Yehova analonjeza molumbira kwa makolo anu, 19 kupirikitsiratu adani anu onse, monga Yehova wanenera.

20 Mʼtsogolo muno, ana anu akadzakufunsani kuti, “Kodi tanthauzo la ndondomeko, malangizo, zikhazikitso ndi malamulo amene Yehova Mulungu wathu anakulamulani nʼchiyani?” 21 Inu mudzawawuze kuti, “Ife tinali akapolo a Farao ku Igupto, koma Yehova anatitulutsa ku Igupto ndi dzanja lamphamvu. 22 Ifeyo tikuona Yehova anatumiza zizindikiro zozizwitsa ndi zodabwitsa, zazikulu ndi zoopsa, pa Aigupto ndi Farao pamodzi ndi banja lake lonse. 23 Koma anatitulutsa kumeneko ndi kutilowetsa kuno natipatsa dziko limene analonjeza mwa lumbiro kwa makolo athu. 24 Yehova anatilamula kuti tizimvera malamulo onsewa, kuti tizimuopa kuti zinthu zizitiyendera bwino pa moyo wathu monga momwe zilili leromu. 25 Ndipo ngati tisamala kumvera malamulo onsewa pamaso pa Yehova Mulungu wathu monga momwe anatilamulira ife, chimenecho chidzakhala chilungamo chathu.”

Love the Lord Your God

These are the commands, decrees and laws the Lord your God directed me to teach you to observe in the land that you are crossing the Jordan to possess, so that you, your children and their children after them may fear(A) the Lord your God as long as you live(B) by keeping all his decrees and commands(C) that I give you, and so that you may enjoy long life.(D) Hear, Israel, and be careful to obey(E) so that it may go well with you and that you may increase greatly(F) in a land flowing with milk and honey,(G) just as the Lord, the God of your ancestors, promised(H) you.

Hear, O Israel: The Lord our God, the Lord is one.[a](I) Love(J) the Lord your God with all your heart(K) and with all your soul and with all your strength.(L) These commandments that I give you today are to be on your hearts.(M) Impress them on your children. Talk about them when you sit at home and when you walk along the road, when you lie down and when you get up.(N) Tie them as symbols on your hands and bind them on your foreheads.(O) Write them on the doorframes of your houses and on your gates.(P)

10 When the Lord your God brings you into the land he swore to your fathers, to Abraham, Isaac and Jacob, to give you—a land with large, flourishing cities you did not build,(Q) 11 houses filled with all kinds of good things you did not provide, wells you did not dig,(R) and vineyards and olive groves you did not plant—then when you eat and are satisfied,(S) 12 be careful that you do not forget(T) the Lord, who brought you out of Egypt, out of the land of slavery.

13 Fear the Lord(U) your God, serve him only(V) and take your oaths(W) in his name.(X) 14 Do not follow other gods, the gods of the peoples around you; 15 for the Lord your God(Y), who is among you, is a jealous God and his anger will burn against you, and he will destroy you from the face of the land. 16 Do not put the Lord your God to the test(Z) as you did at Massah. 17 Be sure to keep(AA) the commands of the Lord your God and the stipulations and decrees he has given you.(AB) 18 Do what is right and good in the Lord’s sight,(AC) so that it may go well(AD) with you and you may go in and take over the good land the Lord promised on oath to your ancestors, 19 thrusting out all your enemies(AE) before you, as the Lord said.

20 In the future, when your son asks you,(AF) “What is the meaning of the stipulations, decrees and laws the Lord our God has commanded you?” 21 tell him: “We were slaves of Pharaoh in Egypt, but the Lord brought us out of Egypt with a mighty hand.(AG) 22 Before our eyes the Lord sent signs and wonders—great and terrible—on Egypt and Pharaoh and his whole household. 23 But he brought us out from there to bring us in and give us the land he promised on oath to our ancestors. 24 The Lord commanded us to obey all these decrees and to fear the Lord our God,(AH) so that we might always prosper and be kept alive, as is the case today.(AI) 25 And if we are careful to obey all this law(AJ) before the Lord our God, as he has commanded us, that will be our righteousness.(AK)

Footnotes

  1. Deuteronomy 6:4 Or The Lord our God is one Lord; or The Lord is our God, the Lord is one; or The Lord is our God, the Lord alone