Add parallel Print Page Options

Guwa Lansembe ku Phiri la Ebala

27 Mose ndi akuluakulu a Israeli analamula anthu kuti, “Sungani malamulo onse amene ndikukupatsani lero lino. Mukawoloka mtsinje wa Yorodani kulowa mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani, muyimiritse miyala ingapo ikuluikulu ndi kuyikulungiza. Mulembepo mawu onse a malamulo amenewa pamene muwoloka kulowa mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani, dziko loyenda mkaka ndi uchi, monga momwe Yehova Mulungu wa makolo anu anakulonjezerani. Ndipo mukawoloka Yorodani muyimike miyala iyi pa Phiri la Ebala monga momwe ndikukulamulirani lero lino ndipo muyikulungize. Pamenepo mumange guwa lansembe la miyala la Yehova Mulungu wanu. Musagwiritse ntchito chida chilichonse chachitsulo pa miyalapo. Mumange guwa lansembe la Yehova Mulungu wanu ndi miyala yakutchire ndi kuperekerapo nsembe yopsereza kwa Yehova Mulungu wanu. Muperekerepo nsembe zopereka za chiyanjano, muzidye ndi kukondwera pamaso pa Yehova Mulungu wanu. Ndipo pa miyalapo mudzalembepo mawu onse a malamulo ndi malemba akuluakulu.”

Matemberero Kuchokera ku Phiri la Ebala

Kenaka Mose ndi ansembe, amene ndi Alevi anati kwa Aisraeli onse, “Khalani chete Aisraeli inu ndipo mumvetsere! Tsopano inu ndinu anthu a Yehova Mulungu wanu. 10 Muzimvera Yehova Mulungu wanu ndi kutsata malamulo ake ndi malangizo ake omwe ndikukupatsani lero lino.”

11 Tsiku lomwelo Mose analamula anthu kuti:

12 Mukawoloka Yorodani, mafuko awa akayimirire pa Phiri la Gerizimu ndi kudalitsa anthu: Simeoni, Levi, Yuda, Isakara, Yosefe ndi Benjamini. 13 Ndipo mafuko awa akayimirire pa Phiri la Ebala ndi kutchula matemberero: Rubeni, Gadi, Aseri, Zebuloni, Dani ndi Nafutali.

14 Alevi adzayankhula mokweza kwa Aisraeli onse kuti:

15 “Ndi wotembereredwa munthu amene asema chifanizo kapena kupanga fano, ndi kuchiyika mobisa, pakuti chimenechi ndi chinthu chodetsedwa pamaso pa Yehova, ntchito za manja a anthu.”

Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!”

16 “Ndi wotembereredwa munthu amene sachitira ulemu abambo ake kapena amayi ake.”

Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!”

17 “Ndi wotembereredwa munthu amene amasuntha mwala wa malire wa mnzake.”

Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!”

18 “Ndi wotembereredwa munthu amene amasocheretsa munthu wosaona pa msewu.”

Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!”

19 “Ndi wotembereredwa munthu amene sachitira chilungamo mlendo, ana amasiye kapena mkazi wamasiye.”

Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!”

20 “Ndi wotembereredwa munthu amene agonana ndi mkazi wa abambo ake pakuti iye sachitira ulemu pogona pa abambo ake.”

Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!”

21 “Ndi wotembereredwa munthu amene achita chigololo ndi nyama ya mtundu uli wonse.”

Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!”

22 “Ndi wotembereredwa munthu amene agonana ndi mlongo wake, mwana wamkazi wa abambo ake kapena mwana wamkazi wa amayi ake.”

Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!”

23 “Ndi wotembereredwa munthu amene agonana ndi apongozi ake.”

Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!”

24 “Ndi wotembereredwa munthu amene apha mnzake mwachinsinsi.”

Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!”

25 “Ndi wotembereredwa munthu amene alandira chiphuphu kuti aphe munthu wosalakwa.”

Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!”

26 “Ndi wotembereredwa aliyense amene sachita kapena sasunga mawu a malamulo awa.”

Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!”

The Altar on Mount Ebal

27 Moses and the elders of Israel commanded the people: “Keep all these commands(A) that I give you today. When you have crossed the Jordan(B) into the land the Lord your God is giving you, set up some large stones(C) and coat them with plaster.(D) Write on them all the words of this law when you have crossed over to enter the land the Lord your God is giving you, a land flowing with milk and honey,(E) just as the Lord, the God of your ancestors, promised you. And when you have crossed the Jordan, set up these stones on Mount Ebal,(F) as I command you today, and coat them with plaster. Build there an altar(G) to the Lord your God, an altar of stones. Do not use any iron tool(H) on them. Build the altar of the Lord your God with fieldstones and offer burnt offerings on it to the Lord your God. Sacrifice fellowship offerings(I) there, eating them and rejoicing(J) in the presence of the Lord your God.(K) And you shall write very clearly all the words of this law on these stones(L) you have set up.”(M)

Curses From Mount Ebal

Then Moses and the Levitical(N) priests said to all Israel, “Be silent, Israel, and listen! You have now become the people of the Lord your God.(O) 10 Obey the Lord your God and follow his commands and decrees that I give you today.”

11 On the same day Moses commanded the people:

12 When you have crossed the Jordan, these tribes shall stand on Mount Gerizim(P) to bless the people: Simeon, Levi, Judah, Issachar,(Q) Joseph and Benjamin.(R) 13 And these tribes shall stand on Mount Ebal(S) to pronounce curses: Reuben, Gad, Asher, Zebulun, Dan and Naphtali.

14 The Levites shall recite to all the people of Israel in a loud voice:

15 “Cursed is anyone who makes an idol(T)—a thing detestable(U) to the Lord, the work of skilled hands—and sets it up in secret.”

Then all the people shall say, “Amen!”(V)

16 “Cursed is anyone who dishonors their father or mother.”(W)

Then all the people shall say, “Amen!”

17 “Cursed is anyone who moves their neighbor’s boundary stone.”(X)

Then all the people shall say, “Amen!”

18 “Cursed is anyone who leads the blind astray on the road.”(Y)

Then all the people shall say, “Amen!”

19 “Cursed is anyone who withholds justice from the foreigner,(Z) the fatherless or the widow.”(AA)

Then all the people shall say, “Amen!”

20 “Cursed is anyone who sleeps with his father’s wife, for he dishonors his father’s bed.”(AB)

Then all the people shall say, “Amen!”

21 “Cursed is anyone who has sexual relations with any animal.”(AC)

Then all the people shall say, “Amen!”

22 “Cursed is anyone who sleeps with his sister, the daughter of his father or the daughter of his mother.”(AD)

Then all the people shall say, “Amen!”

23 “Cursed is anyone who sleeps with his mother-in-law.”(AE)

Then all the people shall say, “Amen!”

24 “Cursed is anyone who kills(AF) their neighbor secretly.”(AG)

Then all the people shall say, “Amen!”

25 “Cursed is anyone who accepts a bribe to kill an innocent person.”(AH)

Then all the people shall say, “Amen!”

26 “Cursed is anyone who does not uphold the words of this law by carrying them out.”(AI)

Then all the people shall say, “Amen!”(AJ)