Add parallel Print Page Options

Kupulumutsidwa kwa Yerusalemu

19 Mfumu Hezekiya atamva zimenezi, anangʼamba zovala zake navala chiguduli ndipo analowa mʼNyumba ya Yehova. Iye anatuma Eliyakimu, woyangʼanira nyumba ya mfumu, Sebina mlembi wa bwalo ndi ansembe akuluakulu, onse atavala ziguduli, kwa mneneri Yesaya mwana wa Amozi. Iwo anamuwuza kuti, “Hezekiya akunena kuti, ‘Lero ndi tsiku lamavuto, lachilango ndi lamanyazi. Ife lero tili ngati mayi woyembekezera amene pofika nthawi yoti achire akupezeka kuti alibe mphamvu zoberekera. Mwina Yehova Mulungu wanu adzamva mawu onse a Rabusake amene mbuye wake, mfumu ya ku Asiriya anamutuma kudzanyoza Mulungu wamoyo, ndipo Mulunguyo adzamulanga chifukwa cha mawu amene Yehova Mulungu wanu wamva. Choncho pemphererani anthu otsala amene akanali ndi moyo.’ ”

Akuluakulu a Mfumu Hezekiya atafika kwa Yesaya, Yesaya anawawuza kuti, “Kawuzeni mbuye wanu kuti, ‘Yehova akunena kuti: Usachite mantha ndi zimene wamva, mawu amene nthumwi za mfumu ya ku Asiriya zandinyoza nawo Ine. Tamverani! Ine ndidzayika mwa mfumuyo mzimu wina kotero kuti akadzamva mphekesera ya nkhondo, adzabwerera ku dziko lake ndipo Ine ndidzachititsa kuti aphedwe ndi lupanga kwawo komweko.’ ”

Rabusake atamva kuti mfumu ya ku Asiriya yachoka ku Lakisi, iye anabwerera mʼmbuyo ndipo anakapeza mfumu ikuchita nkhondo ndi mzinda wa Libina.

Nthawi imeneyi Senakeribu analandira uthenga wakuti Tirihaka, mfumu ya ku Kusi, akubwera kudzachita naye nkhondo. Choncho iye anatumanso amithenga kwa Hezekiya ndi mawu awa: 10 “Kawuzeni Hezekiya mfumu ya Yuda kuti: Usalole kuti Mulungu amene ukumudalira akupusitse ponena kuti, ‘Yerusalemu sadzaperekedwa mʼmanja mwa mfumu ya ku Asiriya.’ 11 Ndithu iwe unamva chimene mafumu a Asiriya anachita ku mayiko ena onse, kuti anawawononga kotheratu. Ndipo kodi iwe nʼkupulumuka? 12 Kodi milungu ya mitundu imene makolo anga anayigonjetsa, milungu ya anthu a ku Gozani, Harani, Rezefi ndi Aedeni amene anali ku Teli Asara, inawapulumutsa? 13 Kodi mafumu a Hamati, Aripadi ndi mafumu a mizinda ya Sefaravaimu, Hena ndi Iva, ali kuti?”

Pemphero la Hezekiya

14 Hezekiya analandira kalata kwa amithenga aja nayiwerenga. Pomwepo anapita ku Nyumba ya Yehova nayika kalatayo pamaso pa Yehova. 15 Ndipo Hezekiya anapemphera kwa Yehova nati, “Inu Yehova Mulungu wa Israeli, Inu amene mumakhala pa Akerubi, Inu nokha ndinu Mulungu wolamulira maufumu onse a dziko lapansi. Inu munalenga kumwamba ndi dziko lapansi. 16 Inu Yehova, tcherani khutu lanu ndipo mumve Yehova tsekulani maso anu ndipo muone, imvani mawu onse amene Senakeribu watumiza kunyoza Inu Mulungu wamoyo.

17 “Inu Yehova, nʼzoonadi kuti mafumu a Asiriya anawononga mitundu iyi ndi mayiko awo. 18 Iwo anaponya milungu yawo pa moto ndi kuyiwononga pakuti sinali milungu koma mitengo ndi miyala chabe, yopangidwa ndi anthu. 19 Ndipo tsopano Inu Yehova Mulungu wathu, tipulumutseni ndithu mʼdzanja lake, kuti maufumu onse a dziko lapansi adziwe kuti Inu nokha, Inu Yehova, ndinu Mulungu.”

Yankho la Mulungu Kudzera mwa Yesaya

20 Ndipo Yesaya mwana wa Amozi anatumiza uthenga kwa Hezekiya wakuti, “Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Ndamva pemphero lako lonena za Senakeribu mfumu ya ku Asiriya.’ ” 21 Mawu amene Yehova wayankhula wotsutsana naye ndi awa:

“Namwali wa Ziyoni
    akukunyoza ndi kukuseka iwe.
Mwana wamkazi wa Yerusalemu
    akupukusa mutu wake kumbuyo kwako.
22 Kodi iweyo wanyoza ndi kuchitira chipongwe yani?
    Kodi ndani amene wamufuwulira mawu ako
ndi kumuyangʼana monyada?
    Wachitiratu izi Woyera wa Israeli!
23 Kudzera mwa amithenga ako
    wonyoza Ambuye.
Ndipo wanena kuti,
    ‘Ndi magaleta ochuluka
ndinakwera mapiri ataliatali,
    pa msonga za mapiri a Lebanoni.
Ndigwetsa mitengo yake ya mkungudza yayitali kwambiri,
    mitengo yake ya payini yabwino kwambiri.
Ndalowanso mʼkati mwake mwenimweni,
    mwa nkhalango yake yowirira kwambiri.
24 Ndakumba zitsime ku mayiko achilendo
    ndipo ndinamwa madzi a kumeneko.
Ndi mapazi anga
    ndawumitsa mitsinje yonse ya ku Igupto.’ ”

25 “ ‘Kodi sunamvepo?
    Zimenezi ndinazikhazikitsa kalekale.
Ndinazikonzeratu masiku amakedzana;
    tsopano ndachita kuti zichitikedi,
iwe kwako kunali kungosandutsa mizinda yotetezedwa
    kukhala milu ya miyala.
26 Anthu a kumeneko ndi opanda mphamvu,
    athedwa nzeru ndipo ali ndi manyazi.
Ali ngati mbewu za mʼmunda,
    ngati udzu wanthete,
ali ngati udzu womera pa denga,
    umene umawuma usanakule nʼkomwe.’ ”

27 “ ‘Koma Ine ndimadziwa kukhala kwako,
    kutuluka kwako ndi kulowa kwako,
    ndi mkwiyo wako pa Ine.
28 Chifukwa chakuti wandikwiyira
    ndipo ndamva za mwano wako,
ndidzakola mphuno yako ndi mbedza
    ndi kuyika chitsulo changa mʼkamwa mwako,
ndipo ndidzakubweza pokudzeretsa
    njira yomwe unadzera pobwera.’

29 “Koma iwe Hezekiya, chizindikiro chako chidzakhala ichi:

“Chaka chino mudzadya tirigu wamphulumukwa,
    ndipo chaka chamawa mudzadya tirigu wongodzimerera.
Koma chaka chachitatu mudzadzala ndi kukolola,
    mudzawoka mphesa ndipo mudzadya zipatso zake.
30 Anthu a nyumba ya Yuda amene adzatsale
    adzazika mizu ndi kubereka zipatso.
31 Pakuti ku Yerusalemu kudzachokera anthu otsala,
    ndi ku phiri la Ziyoni kudzachokera gulu la anthu opulumuka.”

“Changu cha Yehova Wamphamvuzonse chidzachita zimenezi.

32 “Choncho chimene Yehova akunena za mfumu ya ku Asiriya ndi ichi:

“ ‘Iye sadzalowa mu mzinda umenewu
    kapena kuponyamo muvi.
Sadzayandikira mzindawu ndi zishango zake
    kapena kumanga nthumbira ya nkhondo.
33 Adzabwerera potsata njira imene anadzera pobwera;
    sadzalowa mu mzinda umenewu,
            akutero Yehova.
34 Ndidzateteza mzinda umenewu kuwupulumutsa,
    chifukwa cha Ine mwini ndiponso chifukwa cha Davide mtumiki wanga.’ ”

35 Usiku umenewo mngelo wa Yehova anapita ku misasa ya ku Asiriya ndi kupha ankhondo 185,000. Ndipo pamene anthu anadzuka mmawa, taonani, mitembo inali ngundangunda! 36 Choncho Senakeribu mfumu ya ku Asiriya anapasula misasa ndi kuchoka. Anabwerera ku Ninive nakakhala kumeneko.

37 Tsiku lina, pamene Senakeribu ankapembedza mʼnyumba ya Nisiroki mulungu wake, ana ake Adirameleki ndi Sarezeri anamupha ndi lupanga ndipo anathawira ku dziko la Ararati. Tsono Esrahadoni, mwana wake, analowa ufumu mʼmalo mwake.