Add parallel Print Page Options

Agibiyoni Abwezera

21 Pa nthawi ya ulamuliro wa Davide kunali njala kwa zaka zitatu zotsatana. Kotero Davide anapemphera kwa Yehova. Yehova anati, “Izi zachitika chifukwa chakuti Sauli ndi banja lake akanali ndi mlandu wakupha Agibiyoni.”

Mfumu inayitanitsa Agibiyoni ndipo inayankhula nawo. (Tsono Agibiyoni sanali Aisraeli, koma otsala mwa Aamori. Aisraeli analumbira kuwasiya ndi moyo, koma Sauli chifukwa cha chikondi cha pa Israeli ndi Yuda, anafuna kuwawonongeratu). Davide anafunsa Agibiyoni kuti, “Kodi ine ndikuchitireni chiyani? Ndipepese bwanji kuti inu mudalitse cholowa cha Yehova?”

Agibiyoni anamuyankha kuti, “Ife tilibe ufulu woti nʼkulamula Sauli ndi banja lake kuti atipatse siliva kapena golide, tilibenso ufulu woti nʼkupha wina aliyense mu Israeli.”

Davide anafunsa, “Mukufuna ine ndikuchitireni chiyani?”

Iwo anayankha mfumu kuti, “Tsono za munthu amene anatiwononga ndi kukonza chiwembu choti titheretu ndi kukhala wopanda malo mu Israeli, mutipatse adzukulu ake aamuna asanu ndi awiri kuti tiwaphe ndi kuwapereka pamaso pa Yehova ku Gibeya wa Sauli, wosankhidwa wa Yehova.”

Choncho mfumu inati, “Ine ndidzakupatsani.”

Koma mfumu inasunga Mefiboseti mwana wa Yonatani, mwana wa Sauli, chifukwa cha kulumbira kumene mfumu Davide ndi Yonatani mwana wa Sauli anachita pamaso pa Yehova. Ndipo mfumu inatenga Arimoni ndi Mefiboseti, ana aamuna awiri a Rizipa, mwana wamkazi wa Ayiwa, amene anaberekera Sauli pamodzi ndi ana asanu a Merabi mwana wamkazi wa Sauli, amene anabereka Adirieli mwana wa Barizilai Mmeholati. Iye anawapereka kwa anthu a ku Gibiyoni, amene anawapha nawayika pa phiri la Yehova. Onse asanu ndi awiri anafera limodzi. Iwo anaphedwa masiku oyamba kukolola barele.

10 Rizipa mwana wamkazi wa Ayiwa anatenga chiguduli ndi kudziyalira pa mwala (pamene panali mitemboyo). Kuyambira nthawi yoyamba kukolola mpaka pamene mvula inayambanso kugwa, iye sanalole kuti mbalame zikhudze mitemboyo masana kapena nyama zakuthengo usiku. 11 Davide atawuzidwa zimene Rizipa mwana wamkazi wa Ayiwa, mzikazi wa Sauli anachita, 12 anapita kukatenga mafupa a Sauli ndi mwana wake Yonatani kwa anthu a ku Yabesi Giliyadi (iwo anawatenga mwamseri kuchoka pabwalo la ku Beti-Sani, kumene Afilisti anawapachika atapha Sauli ku Gilibowa). 13 Davide anakatenga mafupa a Sauli ndi mwana wake Yonatani kumeneko ndiponso mafupa otayidwa a amene anaphedwa nawasonkhanitsa pamodzi.

14 Iwo anayika mafupa a Sauli ndi mwana wake Yonatani mʼmanda a Kisi abambo ake a Sauli ku Zera mʼdziko la Benjamini, ndipo anachita zonse zimene mfumu inalamula. Atachita zimenezi, Mulungu anayankha pemphero lopempherera dzikolo.

Nkhondo ndi Afilisti

15 Nthawi inanso panali nkhondo pakati pa Afilisti ndi Aisraeli, Davide anapita ndi ankhondo ake kukamenyana ndi Afilisti ndipo iye anatopa kwambiri. 16 Ndipo Isibi-Benobi, mmodzi mwa zidzukulu za Rafa, amene mkondo wake unkalemera makilogalamu atatu ndi theka ndipo analinso ndi lupanga latsopano, anati adzapha Davide. 17 Koma Abisai mwana wa Zeruya anabwera kudzapulumutsa Davide. Iye anamukantha Mfilisitiyo ndi kumupha. Pamenepo asilikali a Davide analumbira kwa iye kuti, “Inu simudzapita nafenso ku nkhondo, kuti nyale ya Israeli isadzazimitsidwe.”

18 Patapita nthawi, panali nkhondo ina ndi Afilisti ku Gobu. Pa nthawi imeneyo Sibekai Mhusati anapha Safu, mmodzi mwa zidzukulu za Arefai.

19 Pa nkhondo inanso ndi Afilisti ku Gobu, Elihanani mwana wa Yaare-Oregimu wa ku Betelehemu anapha Goliati Mgiti, amene anali ndi mkondo ngati ndodo yowombera nsalu.

20 Pa nkhondo inanso imene inachitika ku Gati panali munthu wina wamtali kwambiri wa zala zisanu ndi chimodzi mʼmanja ndi mʼmapazi ndipo zonse pamodzi zinalipo 24. Iyenso anali chidzukulu cha Rafa. 21 Pamene iye ankanyoza Aisraeli, Yonatani mwana wa Simea, mʼbale wake wa Davide anamupha.

22 Anthu anayi amenewa anali zidzukulu za Rafa ku Gati, ndipo onse anaphedwa ndi Davide ndi ankhondo ake.

The Gibeonites Avenged

21 During the reign of David, there was a famine(A) for three successive years; so David sought(B) the face of the Lord. The Lord said, “It is on account of Saul and his blood-stained house; it is because he put the Gibeonites to death.”

The king summoned the Gibeonites(C) and spoke to them. (Now the Gibeonites were not a part of Israel but were survivors of the Amorites; the Israelites had sworn to spare them, but Saul in his zeal for Israel and Judah had tried to annihilate them.) David asked the Gibeonites, “What shall I do for you? How shall I make atonement so that you will bless the Lord’s inheritance?”(D)

The Gibeonites answered him, “We have no right to demand silver or gold from Saul or his family, nor do we have the right to put anyone in Israel to death.”(E)

“What do you want me to do for you?” David asked.

They answered the king, “As for the man who destroyed us and plotted against us so that we have been decimated and have no place anywhere in Israel, let seven of his male descendants be given to us to be killed and their bodies exposed(F) before the Lord at Gibeah of Saul—the Lord’s chosen(G) one.”

So the king said, “I will give them to you.”

The king spared Mephibosheth(H) son of Jonathan, the son of Saul, because of the oath(I) before the Lord between David and Jonathan son of Saul. But the king took Armoni and Mephibosheth, the two sons of Aiah’s daughter Rizpah,(J) whom she had borne to Saul, together with the five sons of Saul’s daughter Merab,[a] whom she had borne to Adriel son of Barzillai the Meholathite.(K) He handed them over to the Gibeonites, who killed them and exposed their bodies on a hill before the Lord. All seven of them fell together; they were put to death(L) during the first days of the harvest, just as the barley harvest was beginning.(M)

10 Rizpah daughter of Aiah took sackcloth and spread it out for herself on a rock. From the beginning of the harvest till the rain poured down from the heavens on the bodies, she did not let the birds touch them by day or the wild animals by night.(N) 11 When David was told what Aiah’s daughter Rizpah, Saul’s concubine, had done, 12 he went and took the bones of Saul(O) and his son Jonathan from the citizens of Jabesh Gilead.(P) (They had stolen their bodies from the public square at Beth Shan,(Q) where the Philistines had hung(R) them after they struck Saul down on Gilboa.)(S) 13 David brought the bones of Saul and his son Jonathan from there, and the bones of those who had been killed and exposed were gathered up.

14 They buried the bones of Saul and his son Jonathan in the tomb of Saul’s father Kish, at Zela(T) in Benjamin, and did everything the king commanded. After that,(U) God answered prayer(V) in behalf of the land.(W)

Wars Against the Philistines(X)

15 Once again there was a battle between the Philistines(Y) and Israel. David went down with his men to fight against the Philistines, and he became exhausted. 16 And Ishbi-Benob, one of the descendants of Rapha, whose bronze spearhead weighed three hundred shekels[b] and who was armed with a new sword, said he would kill David. 17 But Abishai(Z) son of Zeruiah came to David’s rescue; he struck the Philistine down and killed him. Then David’s men swore to him, saying, “Never again will you go out with us to battle, so that the lamp(AA) of Israel will not be extinguished.(AB)

18 In the course of time, there was another battle with the Philistines, at Gob. At that time Sibbekai(AC) the Hushathite killed Saph, one of the descendants of Rapha.

19 In another battle with the Philistines at Gob, Elhanan son of Jair[c] the Bethlehemite killed the brother of[d] Goliath the Gittite,(AD) who had a spear with a shaft like a weaver’s rod.(AE)

20 In still another battle, which took place at Gath, there was a huge man with six fingers on each hand and six toes on each foot—twenty-four in all. He also was descended from Rapha. 21 When he taunted(AF) Israel, Jonathan son of Shimeah,(AG) David’s brother, killed him.

22 These four were descendants of Rapha in Gath, and they fell at the hands of David and his men.

Footnotes

  1. 2 Samuel 21:8 Two Hebrew manuscripts, some Septuagint manuscripts and Syriac (see also 1 Samuel 18:19); most Hebrew and Septuagint manuscripts Michal
  2. 2 Samuel 21:16 That is, about 7 1/2 pounds or about 3.5 kilograms
  3. 2 Samuel 21:19 See 1 Chron. 20:5; Hebrew Jaare-Oregim.
  4. 2 Samuel 21:19 See 1 Chron. 20:5; Hebrew does not have the brother of.