Add parallel Print Page Options

Mizinda Yopulumukiramo

20 Pambuyo pake Yehova anati kwa Yoswa: “Uza Aisraeli kuti apatule mizinda yopulumukiramo, monga ine ndinakulangizira kudzera mwa Mose, kuti aliyense amene wapha munthu mosazindikira osati mwadala azithawirako. Motero adzatetezedwa kwa wolipsira. Ngati munthu wathawira ku umodzi mwa mizinda imeneyi, akafike pa malo oweruzira milandu amene ali pa chipata cha mzindawo ndipo akafotokoze mlandu wake pamaso pa akuluakulu a mzindawo. Kenaka iwo adzamulola kulowa mu mzinda wawo ndi kumupatsa malo woti akhale nawo. Ngati munthu wolipsirayo amutsatira komweko atsogoleriwo asapereke munthu wakuphayo chifukwa anapha Mwisraeli mnzakeyo mosazindikira, osati mwachiwembu. Munthu wakuphayo adzakhalabe mu mzindawo mpaka atayimbidwa mlandu pamaso pa gulu lonse, ndiponso mpaka atamwalira mkulu wa ansembe amene akutumikira pa nthawiyo. Pamenepo munthuyo atha kubwereranso ku mudzi kwawo kumene anachoka mothawa kuja.”

Choncho iwo anapatula Kedesi mʼdera la Galileya ku mapiri a Nafutali, Sekemu ku mapiri a Efereimu, ndi Kiriati Ariba (ndiye Hebroni) ku mapiri a Yuda. Kummawa kwa Yorodani, mʼmapiri a chipululu a kummawa kwa Yeriko, anapatula Bezeri pakati pa dera la fuko la Rubeni. Anapatulanso Ramoti ku Giliyadi mʼdera la fuko la Gadi, ndiponso Golani ku Basani mʼdera la fuko la Manase. Imeneyi ndiyo inali mizinda yopulumukiramo ya Aisraeli onse ngakhalenso mlendo wokhala pakati pawo. Munthu aliyense wopha mnzake mwangozi ankathawira ku mizinda imeneyi. Munthu wolipsira sankaloledwa kuti aphe munthu wothawayo ngati mlandu wake sunazengedwe pamaso pa gulu lonse.