Add parallel Print Page Options

Yobu

23 Pamenepo Yobu anayankha kuti,

“Leronso kudandaula kwanga nʼkwakukulu kwambiri;
    Iye akundilanga kwambiri ngakhale ndi kubuwula.
Ndikanangodziwa kumene ndikanamupeza Mulungu;
    ndikanangopita kumene amakhalako!
Ndikanafotokoza mlandu wanga pamaso pake
    ndipo ndikanayankhula mawu odziteteza.
Ndikanadziwa mawu amene Iye akanandiyankha,
    ndi kulingalira bwino zimene akananena!
Kodi Iye akanalimbana nane mwa mphamvu zake zazikulu?
    Ayi, Iye sakanayankhula zinthu zotsutsana nane.
Kumeneko munthu wolungama akanafotokoza mlandu wake pamaso pake,
    ndipo woweruzayo akanandipeza wosalakwa nthawi zonse.

“Taonani, ndikapita kummawa, Iye kulibe kumeneko,
    ndikapita kumadzulo sinditha kumupeza kumeneko.
Akamagwira ntchito kumpoto, sindimuona kumeneko
    akapita kummwera, sindimuona.
10 Koma Iye amadziwa mmene ndimayendera;
    Iyeyo akandiyesa adzandipeza kuti ndili ngati golide.
11 Mapazi anga akhala akuponda mʼmapazi ake;
    ndasunga njira yake ndipo sindinayitaye.
12 Sindinapatuke kusiya malamulo ochokera pakamwa pake;
    ndasunga mawu a pakamwa pake kupambana chakudya changa cha tsiku ndi tsiku.

13 “Koma Iyeyo ndi wosasinthika, ndipo ndani angatsutsane naye?
    Iye amachita chilichonse chimene wafuna.
14 Iye amachita chimene watsimikiza kuti chindichitikire,
    ndipo malingaliro oterowa ali nawobe.
15 Nʼchifukwa chake ndikuchita mantha kwambiri pamaso pake;
    ndikamaganiza zonsezi ndimamuopa.
16 Mulungu walefula mtima wanga;
    Wamphamvuzonse wandiopseza kwambiri.
17 Komatu sindinachititsidwe mantha ndi mdima,
    ndi mdima wandiweyani umene waphimba nkhope yanga.