Add parallel Print Page Options

Mawu a Yobu

19 Pamenepo Yobu anayankha kuti,

“Kodi mudzakhala mukundizunza mpaka liti,
    ndi kundilasa ndi mawu anuwo?
Inuyo mwandinyoza kwambiri;
    mwanditsutsa mopanda manyazi.
Ngati ndi zoona kuti ine ndasochera,
    cholakwachotu nʼchanga.
Ngati ndithudi mukudziyika nokha pamwamba panga,
    ndi kugwiritsa ntchito kunyozedwa kwanga polimbana nane,
pamenepa dziwani kuti Mulungu wandilakwira
    ndipo wandizinga ukonde wake.

“Ngakhale ndifuwule kuti, ‘Akundizunza!’ Palibe wondiyankha;
    ngakhale ndipemphe thandizo, palibe wondichitira zolungama.
Mulungu wanditsekera njira yanga kotero sindingathe kudutsa;
    waphimba njira zanga ndi mdima.
Iye wandilanda ulemu wanga
    ndipo wandivula chipewa chaufumu pamutu panga.
10 Wandiphwanyaphwanya mbali zonse ndipo ndatheratu;
    Iye wazula chiyembekezo changa ngati mtengo.
11 Wandikwiyira ndipo
    akundiyesa mmodzi mwa adani ake.
12 Ankhondo ake akubwera kwa ine mwamphamvu,
    akonzekera zodzalimbana nane
    ndipo azungulira nyumba yanga.

13 “Mulungu wandisiyanitsa ndi abale anga;
    wasandutsa odziwana nane kukhala achilendo kwa ine.
14 Abale anga andithawa;
    abwenzi anga andiyiwala.
15 Anthu odzacheza ku nyumba kwanga ndiponso antchito anga aakazi andisandutsa mlendo;
    ndasanduka mlendo mʼmaso mwawo.
16 Ndikayitana wa ntchito wanga, iye sandiyankha,
    ngakhale ndikapempha ndi pakamwa panga sandichitira kanthu.
17 Mpweya wanga umamunyansa mkazi wanga;
    ndine chinthu chonyansa kwa abale anga a mimba imodzi.
18 Inde, ngakhale ana amandinyoza;
    akandiona amandinyodola.
19 Anzanga onse apamtima amanyansidwa nane;
    iwo amene ndinkawakonda andiwukira.
20 Ndangotsala khungu ndi mafupa okhaokha;
    ndapulumuka lokumbakumba.

21 “Mvereni chisoni, inu abwenzi anga, mvereni chisoni,
    pakuti dzanja la Mulungu landikantha.
22 Chifukwa chiyani mukundilondola ngati Mulungu?
    Kodi simunatope nalo thupi langa?

23 “Aa, achikhala mawu anga analembedwa,
    achikhala analembedwa mʼbuku,
24 akanalembedwa pa mwala ndi chitsulo,
    akanalembedwa pa thanthwe kuti sangathe kufufutidwa!
25 Koma ndikudziwa kuti mpulumutsi wanga ali ndi moyo,
    ndipo pa nthawi yomaliza adzabwera kudzanditeteza.
26 Ndipo khungu langa litatha nʼkuwonongeka,
    mʼthupi langa lomweli ndidzamuona Mulungu.
27 Ine ndemwe ndidzamuona Iye
    ndi maso angawa, ineyo, osati wina ayi.
    Ndithu mtima wanga ukufunitsitsadi!

28 “Koma inu mukuti, ‘Haa! Tingamuzunze bwanji,
    popeza kuti zonsezi zaoneka chifukwa cha iye yemweyo?’
29 Inu muyenera kuopa lupanga;
    pakuti mkwiyo wake umalangadi ndi lupanga;
    zikadzatero muzadziwa kuti chiweruzo chilipo ndithu.”