Add parallel Print Page Options

13 “Ndaziona ndi maso anga zonsezi,
    ndazimva ndi makutu anga ndipo ndazimvetsa.
Zimene inu mukudziwa, inenso ndimazidziwa;
    ineyo sindine munthu wamba kwa inu.
Koma ine ndikulakalaka nditayankhula ndi Wamphamvuzonse
    ndi kukamba mlandu wanga ndi Mulungu.
Koma inu mukundipaka mabodza;
    nonsenu ndinu asingʼanga opanda phindu!
Achikhala munangokhala chete nonsenu!
    Apo mukanachita zanzeru.
Tsopano imvani kudzikanira kwanga;
    imvani kudandaula kwa pakamwa panga.
Kodi inu mudzayankhula moyipa kuyankhulira Mulungu?
    Kodi mudzayankhulira Iyeyo mwachinyengo?
Kodi mudzaonetsa kuti Iyeyo ngokondera?
    Kodi inu mudzamuteteza Mulungu pa mlandu wake?
Mulungu atayangʼanitsitsa, inu nʼkukupezani wosalakwa?
    Kodi inu mungamunamize Iye monga momwe munganamizire munthu?
10 Ndithudi, Iye angathe kukudzudzulani
    ngati muchita zokondera mseri.
11 Kodi ulemerero wake sungakuopseni?
    Kodi kuopsa kwake sikungakuchititseni mantha?
12 Mawu anu anzeru ali ngati miyambi yopanda tanthauzo;
    mawu anu odzitchinjirizira ali ngati mpanda wadothi.

13 “Khalani chete ndipo ndilekeni ndiyankhule;
    tsono zimene zindichitikire zichitike.
14 Chifukwa chiyani ndikuyika moyo wanga pa chiswe
    ndi kutengera mʼmanja moyo wangawu?
15 Ngakhale Iye andiphe, komabe ndidzamukhulupirira;
    ndithu, ndidzafotokoza mlandu wanga pamaso pake.
16 Zoonadi, ichi ndiye chidzakhala chipulumutso changa
    pakuti palibe munthu wosapembedza amene angafike pamaso pake!
17 Mvetserani mosamala mawu anga;
    makutu anu amve zimene ndikunena.
18 Pakuti tsopano ndawukonzekera mlandu wanga,
    ndikudziwa ndipo adzandipeza wolungama.
19 Kodi alipo wina amene angatsutsane nane?
    ngati zili choncho, ndidzakhala chete ndi kufa.

20 “Inu Mulungu, ndipatseni zinthu ziwiri izi,
    ndipo pamenepo ine sindidzakubisalirani:
21 Muchotse dzanja lanu pa ine,
    ndipo muleke kundichititsa mantha ndi kuopsa kwanuko.
22 Tsono muyitane ndipo ndidzayankha,
    kapena mulole kuti ine ndiyankhule ndipo Inu muyankhe.
23 Kodi zolakwa zanga ndi zingati ndipo machimo anga ndi angati?
    Wonetseni kulakwa kwanga ndi machimo anga.
24 Chifukwa chiyani mukundifulatira
    ndi kundiyesa ine mdani wanu?
25 Kodi mudzazunza tsamba lowuluka ndi mphepo?
    Kodi mudzathamangitsa mungu wowuma?
26 Pakuti Inu mwalemba zinthu zowawa zonditsutsa nazo
    ndipo mukundipaka machimo a pa ubwana wanga.
27 Inu mwamanga miyendo yanga ndi maunyolo.
    Mumayangʼanitsitsa mayendedwe anga onse
    poyika zizindikiro pamene mapazi anga apondapo.

28 “Motero munthu amatha ngati chinthu chofumbwa,
    ngati chovala chodyedwa ndi njenjete.