Add parallel Print Page Options

Mawu a Yobu

12 Pamenepo Yobu anayankha kuti,

“Ndithudi inuyo ndinu anthu
    ndipo nzeru zanu zidzafera nanu pamodzi!
Koma inenso ndili nazo nzeru ngati inu;
    ineyo sindine munthu wamba kwa inu.
    Ndani amene sadziwa zonse zimene mwanenazi?

“Ndasanduka chinthu choseketsa kwa abwenzi anga,
    ngakhale ndinkapemphera kwa Mulungu ndipo Iye ankandiyankha.
    Ine ndasanduka chinthu chongoseketsa, ngakhale ndili wolungama ndi wosalakwa!
Anthu amene ali pabwino amanyoza anzawo amene ali pa tsoka.
    Tsokalo limagwa pa amene wayamba kale kugwa.
Nyumba za anthu achifwamba zimakhala pa mtendere,
    ndipo anthu amene amaputa Mulungu amakhala pabwino,
    amene amanyamula milungu yawo mʼmanja.

“Koma funsa nyama zakuthengo ndipo zidzakuphunzitsa,
    kapena mbalame zamumlengalenga ndipo zidzakuwuza;
kapena uyankhule ndi dziko lapansi ndipo lidzakuphunzitsa,
    kapena ulole nsomba zamʼnyanja kuti zikufotokozere.
Kodi mwa zonsezi ndi chiti chimene sichidziwa
    kuti lachita zimenezi ndi dzanja la Yehova?
10 Mʼmanja mwake ndi mʼmene muli moyo wa cholengedwa chilichonse,
    ndiponso moyo wa anthu a mitundu yonse.
11 Kodi khutu sindiye limene limamva mawu
    monga mmene lilime limalawira chakudya?
12 Kodi nzeru sipezeka pakati pa anthu okalamba?
    Kodi moyo wautali sumabweretsa nzeru zomvetsa zinthu?

13 “Kwa Mulungu ndiye kuli nzeru ndi mphamvu;
    uphungu ndi kumvetsa zinthu ndi zake.
14 Chimene Iye wapasula palibe angachimangenso.
    Akatsekera munthu mʼndende palibe angamutulutse.
15 Iyeyo akamanga mvula dziko limawuma;
    akamasula mvulayo, madzi amasefukira pa dziko.
16 Kwa Iye kuli mphamvu ndi kupambana;
    munthu wopusitsidwa ndiponso wopusitsa onse ali mu ulamuliro wake.
17 Iye amalanda aphungu nzeru zawo
    ndipo amapusitsa oweruza.
18 Iye amachotsa zingwe zimene mafumu anawamanga nazo
    ndipo amawamanga lamba mʼchiwuno mwawo.
19 Iye amasocheretsa ansembe atawalanda nzeru zawo
    ndipo amagonjetsa anthu amphamvu amene ndi okhazikika.
20 Iye amakhalitsa chete aphungu odalirika
    ndipo amalanda chidziwitso cha anthu akuluakulu.
21 Iye amanyoza anthu otchuka
    ndipo anthu anyonga amawatha mphamvu.
22 Iye amatulutsira poyera zinthu zozama za mu mdima
    ndipo mdima wandiweyaniwo amawusandutsa kuwala.
23 Iye amakuza mitundu ya anthu ndipo amayiwononganso;
    amachulukitsa mitundu ya anthu ndipo amayimwazanso.
24 Iye amalanda nzeru za atsogoleri a dziko lapansi;
    amawayendetsa mʼthengo mopanda njira.
25 Iwo amafufuzafufuza njira mu mdima wopanda chowunikira;
    Iye amawayendetsa dzandidzandi ngati oledzera.