Add parallel Print Page Options

64 Inu Yehova, bwanji mukanangongʼamba mlengalenga ndi kutsika pansi,
    kuti mapiri agwedezeke pamaso panu!
Monga momwe moto umatenthera tchire
    ndiponso kuwiritsa madzi,
tsikani kuti adani anu adziwe dzina lanu,
    ndiponso kuti mitundu ya anthu injenjemere pamaso panu.
Pakuti nthawi ina pamene munatsika munachita zinthu zoopsa zimene sitinaziyembekezere,
    ndipo mapiri anagwedezeka pamaso panu.
Chikhalire palibe ndi mmodzi yemwe anamvapo
    kapena kuona
Mulungu wina wonga Inu,
    amene amachitira zinthu zotere amene amadikira pa Iye.
Inu mumabwera kudzathandiza onse amene amakondwera pochita zolungama,
    amene amakumbukira njira zanu.
Koma Inu munakwiya,
    ife tinapitiriza kuchimwa.
    Kodi nanga tingapulumutsidwe bwanji?
Tonsefe takhala ngati anthu amene ndi odetsedwa,
    ndipo ntchito zathu zili ngati sanza za msambo;
tonse tafota ngati tsamba,
    ndipo machimo athu akutiwuluzira kutali ngati mphepo.
Palibe amene amapemphera kwa Inu
    kutekeseka kuti apemphe chithandizo kwa Inu;
pakuti mwatifulatira
    ndi kutisiya chifukwa cha machimo athu.

Komabe, Inu Yehova ndinu Atate athu.
    Ife ndife chowumba, Inu ndinu wowumba;
    ife tonse ndi ntchito ya manja anu.
Inu Yehova, musatikwiyire kopitirira muyeso
    musakumbukire machimo athu mpaka muyaya.
Chonde, mutiganizire, ife tikupempha,
    pakuti tonsefe ndi anthu anu.
10 Mizinda yanu yopatulika yasanduka chipululu;
    ngakhaletu Ziyoni wasanduka chipululu, Yerusalemu ndi wamasiye.
11 Nyumba yanu yopatulika ndi yaulemu, kumene makolo athu ankakutamandani,
    yatenthedwa ndi moto
    ndipo malo onse amene tinkawakonda asanduka bwinja.
12 Inu Yehova, zonse zachitikazi, kodi mungokhala osatithandiza?
    Kodi mudzapitirizabe kukhala chete ndi kutilangabe mopitirira muyeso?