Add parallel Print Page Options

16 Anthu a ku Mowabu
    atumiza mphatso za ana ankhosa onenepa,
kuchokera ku Sela kudutsa chipululu
    mpaka kukafika ku phiri la Ziyoni.
Monga momwe mbalame zimawulukira uku ndi uku
    akazimwaza mʼchisa,
momwemonso akazi a ku Mowabu
    akuyendayenda ku madooko a Arinoni.

Amowabu aja anawuza a ku Yuda kuti,
    “Tiwuzeni chochita, gamulani zoti tichite.
Inu mutiteteze kwa adani anthu.
    Mukhale ngati mthunzi wathu dzuwa lili pa liwombo.
Mutibise,
    musatipereke ife othawa nkhondo kwa adani athu.
Lolani kuti anthu othawa nkhondo a ku Mowabu azikhala pakati panu;
    mukhale populumukira pawo kwa wowonongayo.”

Nthawi idzafika ndipo wozunzayo sadzakhalaponso,
    kuwononga kudzaleka;
    waukaliyo adzachoka mʼdzikomo.
Mpando waufumu udzakhazikitsidwa mwachikondi;
    mmodzi mwa zidzukulu za Davide adzakhalapo mokhulupirika.
Iyeyo poweruza adzatsata chilungamo
    ndipo adzalimbikitsa kuchita zachilungamo.

Tinamva kuti Mowabu anadzikuza kwambiri.
    Kunyada kwawo
ndi kunyogodola kwawo ndi kudzitama kwawo,
    zonse ndi zopanda phindu.
Nʼchifukwa chake Amowabu akulira kwambiri;
    iwo akulirira dziko lawo.
Akubuma momvetsa chisoni
    chifukwa cha makeke a mphesa a ku Kiri Hareseti.
Minda ya ku Hesiboni yauma,
    minda ya mpesa ya ku Sibina yaguga.
Atsogoleri a mitundu ina anapondaponda
    minda ya mpesa wabwino,
imene nthambi zake zinakafika ku Yazeri,
    mpaka kutambalalira ku chipululu.
Mizu yake inakafika
    mpaka ku tsidya la nyanja.
Kotero Ine ndikulira, monga mmene akulirira anthu a ku Yazeri,
    chifukwa cha minda ya mpesa ya ku Sibima.
Inu anthu a ku Hesiboni, inu anthu a ku Eleali,
    ndikukunyowetsani ndi misozi!
Mwalephera kupeza zokolola,
    chifukwa cha nkhondo imene inawononga zokolola zonse.
10 Chimwemwe ndi chisangalalo zalekeka ku minda yanu ya zipatso;
    palibe amene akuyimba kapena kufuwula mʼminda ya mpesa;
palibe amene akupsinya vinyo ku malo opsinyira mphesa,
    pakuti ndathetsa kufuwula.
11 Chifukwa chake moyo wanga ukulira ngati pangwe kulirira Mowabu,
    mtima wanga ukubuwula chifukwa cha Kiri Hareseti.
12 Ngakhale anthu a ku Mowabu
    apite ku malo awo achipembedzo
koma amangodzitopetsa ndi kutaya nthawi chabe
    chifukwa sizidzatheka.

13 Awa ndi mawu amene Yehova wayankhula kale zokhudza Mowabu. 14 Koma tsopano Yehova akuti, “Zisanathe zaka zitatu, potsata mʼmene munthu waganyu amawerengera, ulemerero wa Mowabu udzakhala utatheratu ndipo anthu ake ambiri adzakhala atawonongeka, ndipo opulumuka ake adzakhala ochepa ndi ofowoka.”