Add parallel Print Page Options

Nyimbo ya Debora

“Tsiku limenelo Debora ndi Baraki mwana wa Abinoamu anayimba nyimbo iyi:

“Popeza kuti atsogoleri anatsogoleradi mʼdziko la Israeli;
    ndipo anthu anadzipereka okha mwa ufulu,
    tamandani Yehova:

“Imvani inu mafumu! Tcherani khutu, atsogoleri inu!
    Ndidzayimba nyimbo, ndidzayimbira Yehova,
    Mulungu wa Israeli nyimbo yokoma.

“Inu Yehova, pamene munkatuluka mu Seiri,
    pamene mumayenda kuchokera mʼdziko la Edomu,
dziko linagwedezeka, mitambo inasungunuka
    nigwetsa madzi.
Mapiri anagwedezeka pamaso pa Yehova,
    Mulungu wa Israeli.

“Pa nthawi ya Samugara mwana wa Anati,
    pa nthawi ya Yaeli, misewu inasiyidwa;
    alendo ankangoyenda mʼtinjira takumbali.
Anthu a ku midzi anathawa; mu Israeli munalibe midzi
    mpaka pamene iwe Debora unafika;
    unafika ngati mayi ku Israeli.
Pamene anasankha milungu ina,
    nkhondo inabwera ku zipata za mzinda,
ndipo chishango kapena mkondo sizinapezeke
    pakati pa anthu 40,000 mu Israeli.
Mtima wanga uli ndi atsogoleri a Israeli,
    uli ndi anthu amene anadzipereka okha mwaufulu pakati pa anthu.
    Tamandani Yehova!

10 “Inu okwera pa abulu oyera,
    okhala pa zishalo,
    ndi inu oyenda pa msewu,
yankhulani. 11 Ku zitsime, kutali ndi phokoso la a mauta;
    kumeneko akusimba za kuti Yehova wapambana;
    akusimba kuti Yehova walipsira anthu ake mu Israeli.

“Choncho anthu a Yehova
    anasonkhana ku zipata za mzinda.
12 Anati, ‘Tsogolera ndiwe, Debora, tsogolera;
    tsogolera ndiwe, tsogolera, imba nyimbo.
Iwe Baraki! nyamuka
    Tsogolera akapolo ako, iwe mwana wa Abinoamu.’

13 “Kenaka anthu okhulupirika anatsatira atsogoleri awo;
    anthu a Yehova anapita
kukamenyera Yehova nkhondo
    kulimbana ndi adani amphamvu.
14 Anakalowa mʼchigwa kuchokera ku Efereimu;
    akutsatira iwe Benjamini ndi abale ako.
Akulu a ankhondo anachokera ku Makiri,
    ndipo onyamula ndodo ya udindo anachokera ku Zebuloni.
15 Olamulira a Isakara anali pamodzi ndi Debora;
    inde, anthu ochokera ku Isakara anatsatanso Baraki,
    ndipo anathamangira ku chigwa akumutsatira.
Koma pakati pa mafuko a Rubeni
    panali kusinkhasinkha mtima kwambiri osadziwa chenicheni choyenera kuchita.
16 Chifukwa chiyani munangokhala ku makola a nkhosa nʼkumangomvetsera
    zitoliro zoyitanira nkhosa?
Pakati pa anthu a fuko la Rubeni
    panali kusinkhasinkha mtima kwambiri osadziwa chenicheni choyenera kuti achite.
17 Agiliyadi anatsala pa tsidya la Yorodani.
    Ndipo nʼchifukwa chiyani anthu afuko la Dani anatsarira mʼsitima za pa madzi?
Aseri anali pa gombe la Nyanja;
    anangokhala mʼmadooko mwawo.
18 Azebuloni ndi anthu amene anayika moyo wawo mʼzoopsa.
    Nawonso anthu a fuko la Nafutali anayika miyoyo yawo pa chiswe pomenya nkhondo pamwamba pa mapiri.

19 “Mafumu anabwera, anachita nkhondo;
    mafumu Akanaani anachita nkhondo
ku Tanaki pafupi ndi madzi a ku Megido,
    koma sanatengeko zofunkha zasiliva.
20 Ngakhalenso nyenyezi zakumwamba zinachita nkhondo,
    zinathira nkhondo Sisera, zikuyenda mʼnjira zake.
21 Mtsinje wa Kisoni unawakokolola,
    chigumula cha mtsinje wa Kisoni chinawakokolola.
    Mtima wanga, yenda mwamphamvu, limbika!
22 Ndipo ziboda za ngʼombe zazimuna zinachita phokoso lalikulu,
    akavalo ali pa liwiro, akuthamanga kwambiri.
23 Mngelo wa Yehova anati ‘Tembererani Merozi.’
    ‘Tembererani nzika zake mwaukali,
chifukwa sanabwere kudzathandiza Yehova,
    kulimbana ndi adani ake amphamvu.’

24 “Akhale wodala kupambana akazi onse,
    Yaeli mkazi wa Heberi Mkeni;
    inde mwa akazi onse okhala mʼdziko, akhale wodala iyeyu.
25 Munthu uja anapempha madzi akumwa, koma iye anamupatsa mkaka;
    anamupatsa chambiko mʼchikho cha wolemekezeka.
26 Anatenga chikhomo cha tenti mʼdzanja lake,
    anatenganso nyundo ndi dzanja lake lamanja.
Ndipo anakhoma nacho Sisera, anamuphwanya mutu wake,
    ndi kumubowola mu litsipa mwake.
27 Anathifukira ku mapazi a mkaziyo nagwa,
    anagwa; iye anagona pamenepo.
Anagwera pa mapazi a mkaziyo, iye anagwa;
    pamene anagwera, pamenepo anaferapo.

28 “Amayi ake a Sisera anasuzumira pa zenera;
    nafuwula mokweza kuti,
‘Nʼchifukwa chiyani galeta lake lachedwa kufika?
    Nʼchifukwa chiyani phokoso la magaleta ake silikumveka?’
29 Amayi ake anzeru kwambiri anamuyankha,
    ndithudi, mwiniwake anadziyankha yekha kuti,
30 ‘Kodi iwo sakufunafuna zofunkha kuti agawane;
    akugawana wankhondo aliyense mtsikana mmodzi kapena awiri.
    Sisera akumupatsa zofunkha:
    zovala zonyikidwa mu utoto,
    zoti ndizivala mʼkhosi
zovala zopeta zonyika mu utoto, ndi zopeta zomavala mʼkhosi?’

31 “Choncho Yehova! adani anu onse awonongeke,
    koma iwo amene amakukondani inu akhale ngati dzuwa
    pamene lituluka ndi mphamvu zake.”

Ndipo dziko linakhala pa mtendere zaka makumi anayi.