Add parallel Print Page Options

Aritasasita Atumiza Nehemiya ku Yerusalemu

Pa mwezi wa Nisani, mʼchaka cha makumi awiri cha ufumu wa Aritasasita, atabwera ndi vinyo pamaso pa mfumu ine ndinatenga vinyoyo ndi kupereka kwa mfumu. Koma ndinali ndisanakhalepo ndi nkhope yachisoni pamaso pake. Tsono mfumu inandifunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani nkhope yako ikuoneka yachisoni pamene iwe sukudwala? Ichi si chinthu china koma chisoni cha mu mtima.”

Ine ndinachita mantha kwambiri. Ndinawuza mfumu kuti, “Mfumu ikhale ndi moyo wamuyaya! Kodi nkhope yanga ilekerenji kuoneka yachisoni pamene mzinda umene kuli manda a makolo anga, wasanduka bwinja ndipo zipata zake zinawonongedwa ndi moto?”

Apo mfumu inandifunsa kuti, “Tsono ukufuna kundipempha chiyani?”

Ndipo ine ndinapemphera kwa Mulungu Wakumwamba. Ndipo ndinayankha kuti, “Ngati amfumu chingakukondweretseni, ngati mungakomere mtima mtumiki wanune, mundilole kuti ndipite ku Yuda, ku mzinda kumene kuli manda a makolo anga kuti ndikawumangenso.”

Tsono mfumu, mfumukazi itakhala pambali pake, anandifunsa kuti, “Kodi kumeneko ukakhalako masiku angati ndipo udzabwera liti?” Ndinayiwuza mfumu nthawi yake ndipo inandilola kuti ndipite.

Ndipo ndinatinso kwa mfumu, “Ngati zikondweretse mfumu, mundipatse makalata oti ndikapereke kwa abwanamkubwa a ku chigawo cha Patsidya pa Yufurate, kuti akandilole kudutsa mwamtendere mpaka nditakafika ku Yuda. Mundipatsenso kalata yokapereka kwa Asafu woyangʼanira nkhalango ya mfumu, kuti akandipatse mitengo yokapangira mitanda ya zipata za nsanja yoteteza Nyumba ya Mulungu, mitanda ya khoma la mzinda ndi ya nyumba yokhalamo ine.” Mfumu indipatse zomwe ndinapempha popeza Yehova wokoma mtima anali nane. Choncho ndinanyamuka ulendo wanga ndipo ndinafika kwa abwanamkubwa a chigawo cha Patsidya pa Yufurate ndipo ndinawapatsa makalata a mfumu. Mfumu nʼkuti itatumiza akulu ankhondo ndi okwera pa akavalo kuti atsagane nane.

10 Sanibalati wa ku Horoni ndi Tobiya wa ku Amoni atamva zimenezi, iwo anayipidwa kwambiri kuti wina wabwera kudzachitira zabwino Aisraeli.

Nehemiya Ayendera Makoma a Yerusalemu

11 Ndinafika ku Yerusalemu, ndipo ndinakhala kumeneko masiku atatu. 12 Sindinawuze munthu aliyense za zimene Yehova anayika mu mtima mwanga kuti ndichitire mzinda wa Yerusalemu. Choncho ndinanyamuka usiku pamodzi ndi anthu ena owerengeka. Ndinalibe bulu wina aliyense kupatula amene ndinakwerapo.

13 Ndinatuluka usiku podzera ku Chipata cha ku Chigwa ndi kuyenda kupita ku Chitsime cha Chirombo Chamʼmadzi mpaka ku Chipata cha Zinyalala. Ndinayangʼana makoma a Yerusalemu, amene anagwetsedwa, ndi zipata zake, zimene zinawonongedwa ndi moto. 14 Kenaka ndinapita ku Chipata cha Kasupe ndi ku Dziwe la Mfumu. Koma panalibe malo okwanira akuti bulu wanga adutse. 15 Kotero usikuwo ndinapita ku chigwa, ndikuyangʼana khomalo. Pomaliza ndinabwerera ndi kukalowanso mu mzinda kudzera ku Chipata cha ku Chigwa. 16 Akuluakulu sanadziwe kumene ndinapita kapena zimene ndimachita, chifukwa pa nthawiyi nʼkuti ndisananene kalikonse kwa Ayuda kapena ansembe, anthu olemekezeka kapena akuluakulu, kapena wina aliyense amene anali woyenera kugwira ntchitoyi.

17 Ndinawawuza kuti, “Inu mukuona mavuto amene tili nawo. Mukuona kuti mzinda wa Yerusalemu wasanduka bwinja ndipo zipata zake zatenthedwa ndi moto. Tsono tiyeni timangenso makoma a Yerusalemu ndipo sitidzachitanso manyazi.” 18 Ndinawawuza za mmene Yehova Mulungu wanga anandichitira zabwino ndiponso mawu amene mfumu inandiwuza.

Tsono anati, “Tiyeni tiyambenso kumanga.” Kotero analimbitsana mtima kuti ayambenso ntchito yabwinoyi.

19 Koma Sanibalati wa ku Horoni, Tobiya wa ku Amoni ndi Gesemu Mwarabu atamva zimenezi, anatiseka ndi kutinyoza. Iwo anafunsa kuti, “Kodi muti ndi chiyani chimene mukuchitachi? Kodi mufuna kuwukira mfumu?”

20 Koma ndinawayankha kuti, “Mulungu Wakumwamba atithandiza kuti zinthu zitiyendere bwino. Ife antchito ake tiyambapo kumanga. Koma inu mulibe gawo lanu muno mu Yerusalemu. Mulibe chokuyenerezani kulandira malo ano. Mulibenso chilichonse muno chokumbutsa za inu.”