Add parallel Print Page Options

20 Vinyo amachititsa munthu kukhala wonyoza ndipo chakumwa choledzeretsa chimachititsa munthu kukhala wolongolola;
    aliyense wosochera nazo zimenezi alibe nzeru.

Ukali wa mfumu uli ngati kubangula kwa mkango;
    amene amawuputa mkwiyowo amataya moyo wake.

Nʼchaulemu kwa munthu kupewa mikangano,
    koma chitsiru chilichonse chimafulumira kulongolola.

Munthu waulesi satipula mʼmunda pa nthawi yoyenera;
    kotero pa nthawi yokolola adzafunafuna zinthu koma sadzapeza kanthu kalikonse.

Zolinga za mtima wa munthu zili ngati madzi akuya,
    munthu womvetsa zinthu ndiye yekha angawatunge.

Anthu ambiri amayankhula za kukhulupirika kwawo,
    koma munthu wokhulupirika angamupeze ndani?

Munthu wolungama amakhala ndi makhalidwe abwino;
    odala ndi ana ake amene amatsanzira moyo wake.

Mfumu ikhala pa mpando wake wa chiweruzo,
    imapeta ndi maso ake anthu onse oyipa.

Ndani amene anganene kuti, “Ndawuyeretsa mtima wanga;
    ndilibe tchimo lililonse?”

10 Masikelo ndi miyeso ya zinthu imene ili yachinyengo
    zonsezi Yehova zimamunyansa.

11 Ngakhale mwana amadziwika ndi zochita zake,
    ngati zochita zake zili zoyera ndi zoyenera.

12 Makutu amene amamva ndi maso amene amaona,
    zonsezi anazilenga ndi Yehova.

13 Usakonde tulo ungasauke;
    khala maso ndipo udzakhala ndi chakudya chambiri.

14 Munthu wogula chinthu amati, “Sichabwino, sichabwino.”
    Koma akagula nʼkuchokapo amayamba kudzitama.

15 Pali golide ndi miyala yamtengowapatali,
    koma milomo yoyankhula zanzeru ndi yamtengowapatali koposa zonsezi.

16 Utenge chovala cha munthu amene waperekera mlendo chikole;
    kuti chikhale chikole chako chifukwa waperekera chikole munthu wachilendo.

17 Chakudya chochipeza mwachinyengo chimukomera munthu,
    koma pa mapeto pake chimasanduka ngati mchenga mʼkamwa mwake.

18 Zokonzekera zimapindula utafunsira uphungu;
    ndipo usanamenye nkhondo yamba wapempha malangizo oyenera.

19 Amene amanka nanena miseche amawulula zachinsinsi.
    Choncho usamagwirizane naye munthu woyankhula zopusayo.

20 Ngati munthu atemberera abambo ake kapena amayi ake,
    moyo wake udzazimitsidwa ngati nyale mu mdima wandiweyani.

21 Cholowa chochipeza mofulumira poyamba,
    sichidzakhala dalitso pa mapeto pake.

22 Usanene kuti, “Ine ndidzabwezera choyipa chimenechi!”
    Dikira Yehova, ndipo Iye adzakupulumutsa.

23 Miyeso yosintha imamunyansa Yehova;
    ndipo masikelo onyenga si abwino.

24 Mayendedwe a munthu amawalamulira ndi Yehova,
    tsono munthu angadziwe bwanji njira yake?

25 Ndi msampha kwa munthu kuyankhula mofulumira kuti “Chinthu ichi nʼchopatulika kwa Yehova,”
    popeza mwina atha kusintha maganizo utalumbira kale.

26 Mfumu ya nzeru imapeta kwathunthu
    anthu oyipa.

27 Mpweya wa munthu uli ngati nyale ya Yehova;
    imafufuza ziwalo zake zonse zamʼkati.

28 Kukoma mtima ndi kukhulupirika ndizo zimasunga mfumu;
    chilungamo chimalimbikitsa mpando wake waufumu.

29 Ulemerero wa achinyamata uli mu mphamvu zawo,
    imvi ndi ulemerero wa anthu okalamba.

30 Mikwingwirima yopweteka ndiyo imachotsa zoyipa,
    ndipo mikwapulo ndiyo imachotsa zamʼkatikati mwa munthu.