Add parallel Print Page Options

17 Nʼkwabwino kudya mkute koma pali mtendere,
    kuposa kuchita madyerero mʼnyumba mʼmene muli mikangano.

Kapolo wanzeru adzalamulira mwana wochititsa manyazi,
    ndipo kapoloyo adzagawana nawo cholowa ngati mmodzi mwa abale.

Siliva amamuyesa mʼngʼanjo ndipo golide amamuyesa mʼngʼanjo,
    koma Yehova amayesa mitima.

Munthu woyipa amamvera malangizo oyipa;
    munthu wabodza amatchera khutu mawu osakaza.

Iye amene amalalatira mʼmphawi amanyoza mlengi wake;
    amene amakondwerera tsoka la mnzake sadzakhala osalangidwa.

Zidzukulu ndiye ulemu wa anthu okalamba,
    ndipo makolo ndiye ulemerero wa ana.

Kuyankhula bwino sikuyenerana ndi chitsiru,
    nanji kuyankhula bodza kungayenerane kodi ndi mfumu?

Chiphuphu chili ngati mankhwala amwayi kwa wochiperekayo;
    kulikonse kumene amapita zinthu zimamuyendera.

Iye amene amakhululukira zolakwa za wina, amafunitsitsa chikondi;
    wobwerezabwereza nkhani amapha chibwenzi.

10 Munthu wanzeru amamva kamodzi kokha,
    munthu wopanda nzeru ndi samvamkunkhu.

11 Munthu woyipa maganizo ake ali pa kuwukira basi;
    ndipo bwana adzamutumizira wamthenga wankhanza.

12 Nʼkwabwino kukumana ndi chimbalangondo cholandidwa ana ake
    kusiyana ndi kukumana ndi chitsiru mu uchitsiru wake.

13 Ngati munthu abwezera choyipa kusinthana ndi zabwino,
    ndiye choyipa sichidzachoka mʼnyumba mwake.

14 Chiyambi cha mikangano chili ngati kukhamulira madzi,
    choncho uzichokapo mkangano usanayambe.

15 Kumasula munthu wolakwa kapena kumanga munthu wosalakwa,
    zonse ziwirizi Yehova zimamunyansa.

16 Ndalama zogulira nzeru zili ndi phindu lanji mʼmanja mwa chitsiru
    poti iyeyo mutu wake sumayenda bwino?

17 Bwenzi lako limakukonda nthawi zonse,
    ndipo mʼbale wako anabadwa kuti azikuthandiza pamavuto.

18 Munthu wopanda nzeru amavomereza zopereka chikole
    ndipo iyeyo amasanduka chikole cha mnansi wake.

19 Wokonda zolakwa amakonda mkangano,
    ndipo wokonda kuyankhula zonyada amadziyitanira chiwonongeko.

20 Munthu wamtima woyipa zinthu sizimuyendera bwino;
    ndipo woyankhula zachinyengo amagwa mʼmavuto.

21 Mwana wopusa amamvetsa chisoni abambo ake,
    abambo a chitsiru sakhala ndi chimwemwe.

22 Mtima wosangalala uli ngati mankhwala abwino,
    koma mtima wokhumudwa umafowoketsa mafupa.

23 Munthu woyipa amalandira chiphuphu chamseri
    kuti apotoze chiweruzo cholungama.

24 Munthu wozindikira zinthu, maso ake amakhala pa nzeru,
    koma chitsiru chimwazamwaza maso ake pa dziko lonse lapansi.

25 Mwana wopusa amamvetsa chisoni abambo ake
    ndipo amapweteketsa mtima amayi ake.

26 Sibwino kulipitsa munthu wosalakwa,
    kapena kulanga anthu osalakwa.

27 Munthu wosunga pakamwa ndiye wodziwa zinthu,
    ndipo wodekha mtima ndiye womvetsa bwino zinthu.

28 Ngakhale chitsiru chimakhala ngati chanzeru chikakhala chete;
    ndipo chikatseka pakamwa chimakhala ngati munthu wochenjera.