Add parallel Print Page Options

BUKU LACHITATU

Masalimo 73–89

Salimo la Asafu.

73 Mulungu ndi wabwino ndithu kwa Israeli,
    kwa iwo amene ndi oyera mtima.

Koma kunena za ine, mapazi anga anali pafupi kuterereka;
    ndinatsala pangʼono kugwa.
Pakuti ndinkachitira nsanje odzitamandira,
    pamene ndinaona mtendere wa anthu oyipa.

Iwo alibe zosautsa;
    matupi awo ndi athanzi ndi amphamvu.
Saona mavuto monga anthu ena;
    sazunzika ngati anthu ena onse.
Nʼchifukwa chake kunyada kuli monga mkanda wa mʼkhosi mwawo;
    amadziveka chiwawa.
Mʼmitima yawo yokhota mumachokera zolakwa;
    zoyipa zochokera mʼmaganizo awo sizidziwa malire.
Iwowo amanyogodola ndi kumayankhula zoyipa;
    mwa kudzikuza kwawo amaopseza ena nʼkumati, “Tikuponderezani.”
Pakamwa pawo pamayankhula monyoza Mulungu kumwamba
    ndipo lilime lawo limayenda pa dziko lapansi.
10 Nʼchifukwa chake anthu awo amapita kwa iwowo
    ndi kumwa madzi mochuluka.
11 Iwo amati, “Kodi Mulungu angadziwe bwanji?
    Kodi Wammwambamwamba angadziwe kalikonse?”

12 Umu ndi mmene oyipa alili;
    nthawi zonse ali pabwino ndipo chuma chawo chimachulukirachulukira.

13 Ndithudi ine ndawusunga pachabe mtima wanga woyera;
    pachabe ndasamba mʼmanja mwanga mwa kusalakwa kwanga.
14 Tsiku lonse ndapeza mavuto;
    ndakhala ndi kulangidwa mmawa uliwonse.

15 Ndikanati, “Ndidzayankhula motere,”
    ndikanachita chosakhulupirika kwa ana anu.
16 Pamene ndinayesa kuti ndimvetse zonsezi,
    zinandisautsa kwambiri
17 kufikira nditalowa mʼmalo opatulika a Mulungu;
    pamenepo ndinamvetsa mathero awo.

18 Zoonadi Inu munawayika pa malo woterera;
    Mumawagwetsa pansi kuti awonongeke.
19 Mwamsangamsanga iwo amawonongedwa,
    amasesedwa kwathunthu ndi mantha!
20 Monga loto pamene wina adzuka,
    kotero pamene Inu muuka, Inu Ambuye,
    mudzawanyoza ngati maloto chabe.

21 Pamene mtima wanga unasautsidwa
    ndi kuwawidwa mu mzimu mwanga,
22 ndinali wopusa ndi wosadziwa;
    ndinali chirombo chopanda nzeru pamaso panu.

23 Komabe ineyo ndili ndi Inu nthawi zonse;
    mumandigwira dzanja langa lamanja.
24 Inu mumanditsogolera ndi malangizo anu
    ndipo pambuyo pake mudzanditenga ku ulemerero.
25 Kodi kumwamba ndili ndi yani kupatula Inu?
    Ndipo dziko lapansi lilibe chilichonse chimene ndimachilakalaka koposa Inuyo.
26 Thupi ndi mtima wanga zitha kufowoka,
    koma Mulungu ndiye mphamvu ya mtima wanga
    ndi cholandira changa kwamuyaya.

27 Iwo amene ali kutali ndi Inu adzawonongeka;
    Inu mumawononga onse osakhulupirika pamaso panu.
28 Koma kunena za Ine ndi kwabwino kukhala pafupi ndi Mulungu.
    Ndatsimikiza kuti Ambuye Yehova ndiwo pothawirapo panga
    ndipo ndidzalalika ntchito zanu zonse.