Add parallel Print Page Options

148 Tamandani Yehova.

Tamandani Yehova, inu a kumwamba,
    mutamandeni Iye, inu a mlengalenga.
Mutamandeni, inu angelo ake onse,
    mutamandeni, mutamandeni, inu zolengedwa za mmwamba.
Mutamandeni, inu dzuwa ndi mwezi,
    mutamandeni, inu nonse nyenyezi zowala.
Mutamandeni, inu thambo la kumwambamwamba
    ndi inu madzi a pamwamba pa thambo.
Zonse zitamande dzina la Yehova
    pakuti Iye analamula ndipo zinalengedwa.
Iye anaziyika pa malo ake ku nthawi za nthawi;
    analamula ndipo sizidzatha.

Tamandani Yehova pa dziko lapansi,
    inu zolengedwa zikuluzikulu za mʼnyanja, ndi nyanja zonse zakuya,
inu zingʼaningʼani ndi matalala, chipale ndi mitambo,
    mphepo yamkuntho imene imakwaniritsa mawu ake,
inu mapiri ndi zitunda zonse,
    inu mitengo ya zipatso ndi mikungudza yonse,
10 inu nyama zakuthengo ndi ngʼombe zonse,
    inu zolengedwa zingʼonozingʼono ndi mbalame zowuluka.
11 Inu mafumu a dziko lapansi ndi anthu a mitundu yonse,
    inu akalonga ndi olamulira a dziko lapansi.
12 Inu anyamata ndi anamwali,
    inu nkhalamba ndi ana omwe.

13 Onsewo atamande dzina la Yehova
    pakuti dzina lake lokha ndi lolemekezeka;
    ulemerero wake ndi woopsa pa dziko lapansi pano ndi kumwamba komwe.
14 Iye wakwezera nyanga anthu ake,
    matamando a anthu ake onse oyera mtima,
    Aisraeli, anthu a pamtima pake.

Tamandani Yehova.