Add parallel Print Page Options

“Nena kwa abale ako kuti, ‘Ndinu anthu anga,’ kwa alongo ako kuti ‘Ndinu okondedwa anga.’ ”

Kulangidwa ndi Kubwezeretsedwa kwa Israeli

“Dzudzulani amayi anu, adzudzuleni iwo,
    pakuti si mkazi wanga,
    ndipo ine sindine mwamuna wake.
Iyeyo achotse maonekedwe adama pa nkhope yake,
    ndi kusakhulupirika pa mawere ake.
Akapanda kutero ndidzamuvula,
    ndipo adzakhala wamaliseche monga tsiku limene anabadwa;
ndidzamuwumitsa ngati chipululu,
    adzakhala ngati dziko lopanda madzi,
    ndi kumupha ndi ludzu.
Sindidzaonetsa chikondi changa pa ana ake,
    chifukwa ndi ana a mʼchiwerewere.
Amayi awo akhala akuchita zachiwerewere
    ndipo anawabereka anawo akuchita zinthu zochititsa manyazi.
Iwo anati, ‘Ine ndidzatsatira zibwenzi zanga,
    zimene zimandipatsa chakudya ndi madzi,
    ubweya ndi thonje, mafuta ndi chakumwa.’
Choncho njira yake ndidzayitseka ndi minga;
    ndidzamuzinga ndi khoma kotero kuti sadzapezanso njira yotulukira.
Adzathamangira zibwenzi zake koma sadzazipeza;
    adzazifunafuna koma sadzazipeza.
Pamenepo iye adzati,
    ‘Ndibwerera kwa mwamuna wanga woyamba uja,
    pakuti ndinali pabwino ndi iyeyo kusiyanitsa ndi pano.’
Iye sanazindikire kuti ndine amene
    ndinkamupatsa tirigu, vinyo watsopano ndi mafuta.
Ndine amene ndinkamukhuthulira siliva ndi golide,
    zimene ankapangira mafano a Baala.

“Choncho Ine ndidzamulanda tirigu wanga pa nthawi yokolola,
    ndi vinyo wanga watsopano pa nthawi yopsinya mphesa.
Ndidzamulanda ubweya ndi thonje langa,
    zomwe akanaphimba nazo umaliseche wake.
10 Motero tsopano ndidzaonetsa maliseche ake
    pamaso pa zibwenzi zake;
    palibe ndi mmodzi yemwe adzamupulumutse mʼmanja mwanga.
11 Ndidzathetsa zikondwerero zake zonse:
    zikondwerero zake za chaka ndi chaka, za mwezi watsopano,
    za pa masiku a Sabata ndi maphwando ake onse a pa masiku okhazikitsidwa.
12 Ndidzawononga mitengo yake ya mpesa ndi mitengo yake yamkuyu,
    imene iye ankanena kuti inali malipiro ake ochokera kwa zibwenzi zake.
Ndidzayisandutsa chithukuluzi,
    ndipo zirombo zakuthengo zidzadya zipatsozo.
13 Ndidzamulanga chifukwa cha masiku
    amene anafukiza lubani kwa Abaala;
anadzikongoletsa povala mphete ndi mikanda yamtengowapatali
    ndipo anathamangira zibwenzi zake,
    koma Ine anandiyiwala,”
            akutero Yehova.

14 “Koma tsopano ndidzamukopa mkaziyo;
    ndidzapita naye ku chipululu
    ndipo ndidzamuyankhula mwachikondi.
15 Kumeneko ndidzamubwezera minda yake ya mpesa,
    ndipo ndidzasandutsa Chigwa cha Akori kukhala khomo la chiyembekezo.
Kumeneko iye adzayimba nyimbo monga mʼmasiku a ubwana wake,
    monga tsiku limene anatuluka ku Igupto.

16 “Tsiku limeneli,” Yehova akuti,
    “udzandiyitana kuti, ‘Amuna anga;’
    sudzandiyitananso kuti, ‘Mbuye wanga.’
17 Ndidzachotsa mayina a Abaala pakamwa pake;
    sadzatchulanso mayina awo popemphera.
18 Tsiku limenelo ndidzachita pangano
    ndi zirombo zakuthengo ndi mbalame zamumlengalenga
    ndiponso zolengedwa zokwawa pansi kuti ziyanjane ndi anthu anga.
Ndidzachotsa mʼdzikomo uta,
    lupanga ndi zida zonse zankhondo,
    kuti onse apumule mwamtendere.
19 Ndidzakutomera kuti ukhale mkazi wanga mpaka muyaya;
    ndidzakutomera mwachilungamo, mwaungwiro,
    mwachikondi ndi mwachifundo.
20 Ndidzakutomera mokhulupirika
    ndipo udzadziwa Yehova.

21 “Tsiku limenelo Ine ndidzayankha,”
    akutero Yehova.
“Ndidzayankha mlengalenga pempho lake lofuna mitambo
    ndipo mvula idzagwa pa dziko lapansi;
22 ndipo nthaka idzamvera kupempha kwa tirigu,
    vinyo ndi mafuta,
    ndipo zidzamvera Yezireeli.
23 Ndidzadzala Israeli mʼdziko kuti akhale wanga:
    ndidzaonetsa chikondi changa kwa anthu amene ndinkawatchula dzina loti, ‘Sakondedwa.’
Ndidzawawuza amene ndinkawatchula dzina loti, ‘Si anthu anga,’ kuti, ‘Ndinu anthu wanga;’
    ndipo adzanena kuti, ‘ndinu Mulungu wathu,’ ”