Add parallel Print Page Options

Pangano la Mdulidwe

17 Pamene Abramu anali ndi zaka 99, Yehova anamuonekera nati, “Ine ndine Mulungu Wamphamvuzonse. Ukhale munthu wochita zolungama nthawi zonse. Ndipo Ine ndikulonjeza kuti ndidzakupatsa zidzukulu zambiri.”

Pomwepo Abramu anadziponya pansi ndipo Mulungu anati kwa iye, “Pangano langa ndi iwe ndi ili: Udzakhala kholo la mitundu yambiri ya anthu. Sudzatchedwanso Abramu; dzina lako lidzakhala Abrahamu, chifukwa ndakusandutsa kukhala kholo la mitundu yambiri ya anthu. Ndidzakupatsa zidzukulu zambiri motero kuti mitundu yambiri ya anthu idzatuluka mwa iwe. Mafumunso adzatuluka mwa iwe. Pangano langa ndi iwe pamodzi ndi zidzukulu za mibado ya mʼtsogolo lidzakhala la muyaya. Ndidzakhala Mulungu wako ndi Mulungu wa zidzukulu zako. Dziko lonse la Kanaani, limene iwe ukukhala tsopano, ndalipereka kwa iwe ndi kwa zidzukulu zako kuti likhale chuma chanu mpaka muyaya. Ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wa zidzukulu zako.”

Kenaka Mulungu anati kwa Abrahamu, “Koma iwe pamodzi ndi zidzukulu zako zobwera pambuyo pako mʼmibado ya mʼtsogolomo, sungani pangano langali. 10 Iwe pamodzi ndi zidzukulu zako zobwera pambuyo pako muzisunga pangano ili loti mwamuna aliyense pakati panupa azichita mdulidwe. 11 Kuyambira tsopano muzichita mdulidwe ndipo ichi chidzakhala chizindikiro cha pangano langa ndi iwe. 12 Kuyambira tsopano mpaka mibado ya mʼtsogolomo mwana wamwamuna aliyense pakati panu amene wakwana masiku asanu ndi atatu ayenera kuchita mdulidwe. Awa ndi ana obadwa mʼbanja lako, kapena akapolo ochita kugula ndi ndalama, mlendo osakhala wa mʼmbumba yako. 13 Achite mdulidwe ndithu mwana wamwamuna aliyense, mbadwa ngakhale kapolo wochita kugula ndi ndalama, ndipo ichi chidzakhala chizindikiro pa thupi lanu cha pangano langa lamuyaya. 14 Mwamuna aliyense amene adzakhala wosachita mdulidwe adzachotsedwa pakati pa anthu ake chifukwa sanasunge pangano langa.”

15 Mulungu anatinso kwa Abrahamu, “Sarai mkazi wako, sudzamutchanso Sarai; dzina lake lidzakhala Sara. 16 Ndidzamudalitsa ndipo adzakubalira mwana wamwamuna. Ndidzamudalitsa kuti akhale mayi wa mitundu ya anthu; mafumu a anthuwo adzachokera mwa iye.”

17 Abrahamu anadzigwetsa pansi pamaso pa Yehova, Iye anaseka nati, “Kodi munthu wa zaka 100 nʼkubala mwana? Kodi Sara adzabereka mwana pa msinkhu wa zaka makumi asanu ndi anayi?” 18 Ndipo Abrahamu anati kwa Mulungu, “Bwanji mumudalitse Ismaeli.”

19 Koma Mulungu anati, “Ayi, koma mkazi wako Sara adzakubalira mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha Isake. Ndidzasunga pangano langa losatha ndi iyeyu komanso ndi zidzukulu zobwera pambuyo pake. 20 Koma za Ismaeli, ndamva. Ndidzamudalitsadi, ndipo adzakhala ndi zidzukulu zambiri. Iye adzakhala kholo la mafumu khumi ndi awiri ndipo mwa iye mudzatuluka mtundu waukulu wa anthu. 21 Koma ndidzasunga pangano langali ndi Isake amene Sara adzakubalira pofika nthawi ngati ino chaka chamawa.” 22 Atatha kuyankhula, Mulungu anamuchokera Abrahamu.

23 Tsono Abrahamu anachita mdulidwe mwana wake Ismaeli ndi onse amene anali mʼbanja lake, mbadwa ngakhale kapolo ochita kugula ndi ndalama, monga mmene Mulungu analamulira. 24 Abrahamu anali ndi zaka 99 pamene anachita mdulidwe, 25 ndipo mwana wake Ismaeli anali ndi zaka khumi ndi zitatu; 26 Onse, Abrahamu ndi mwana wake Ismaeli, anachita mdulidwe tsiku limodzi. 27 Aliyense wamwamuna wa pa banja pa Abrahamu, kuphatikizapo iwo amene anabadwira pa banja pomwepo kapena akapolo ogula ndi ndalama kwa alendo, anachita mdulidwe.