Add parallel Print Page Options

Mndandanda wa Mitundu ya Anthu

10 Nayi mbiri ya ana a Nowa, Semu, Hamu ndi Yafeti. Ana atatuwa anabereka ana awo chitatha chigumula.

Banja la Yafeti

Ana aamuna a Yafeti anali:

Gomeri, Magogi, Madai, Yavani, Tubala, Mesaki ndi Tirasi.

Ana aamuna a Gomeri anali:

Asikenazi, Rifati ndi Togarima.

Ana aamuna a Yavani anali:

Elisa, Tarisisi, Kitimu ndi Rodanimu. (Amenewa ndiwo makolo a anthu okhala mʼmphepete mwa nyanja. Awa ndi ana a Yafeti monga mwa mafuko a mu mitundu yawo, uliwonse ndi chiyankhulo chake).

Banja la Hamu

Ana aamuna a Hamu anali:

Kusi, Miziraimu, Puti ndi Kanaani.

Ana aamuna a Kusi anali:

Seba, Havila, Sabita, Raama ndi Sabiteka.

Ana aamuna a Raama anali:

Seba ndi Dedani.

Kusi anabereka Nimurodi amene anali wankhondo wamphamvu kwambiri pa dziko lapansi. Iye anali mlenje wamphamvu kwambiri pamaso pa Yehova; nʼchifukwa chake anthu ali ndi chisudzo, chakuti, “Ndiwe mlenje wamphamvu kwambiri pamaso pa Yehova monga Nimurodi.” 10 Malo oyambirira a ufumu wake anali Babeli, Ereki, Akadi ndi Kaline. Malo onsewa anali mʼdziko la Sinara. 11 Atachoka mʼdziko limeneli anapita ku Asiriya kumene anakamanga Ninive, Rehoboti-Iri, Kala, 12 ndi Reseni, mzinda waukulu umene uli pakati pa Ninive ndi Kala.

13 Igupto ndiye kholo la

Aludi, Aanami, Alehabu, Anafutu, 14 Apaturusi, Akasilu ndi Akafitori (kumene kunachokera Afilisti).

15 Kanaani anabereka mwana wake wachisamba,

Sidoni, ndipo anaberekanso Ahiti; 16 Ayebusi, Aamori, Agirigasi; 17 Ahivi, Aariki, Asini, 18 Aaravadi, Azemari ndi Ahamati.

Pambuyo pake, mafuko a Akanaani anafalikira ponseponse, 19 mpaka ku malire a Kanaani. Malirewo anachokera ku Sidoni kulowa cha ku Gerari mpaka ku Gaza, ndi kulowa ku Sodomu, Gomora, Adima ndi Zeboimu mpaka ku Lasa.

20 Amenewa ndiwo ana aamuna a Hamu monga mwa mafuko ndi ziyankhulo zawo, mʼmadera omwe amakhala ndi mitundu yawo.

Banja la Semu

21 Semu amene anali mkulu wake wa Yafeti nayenso anabereka nakhala kholo la Eberi.

22 Ana aamuna a Semu anali:

Elamu, Asuri, Aripakisadi, Ludi ndi Aramu.

23 Ana aamuna a Aramu anali:

Uzi, Huri, Geteri ndi Mesaki.

24 Aripakisadi anabereka Sela,

ndipo Selayo anabereka Eberi.

25 A Eberi anabereka ana aamuna awiri:

Wina anamutcha Pelegi chifukwa pa nthawiyo anthu a pa dziko lapansi anagawikana. Dzina la mʼbale wake linali Yokitani.

26 Yokitani anabereka

Alimodadi, Selefi, Hazari-Maveti, Yera, 27 Hadoramu, Uzali, Dikila, 28 Obali, Abimaeli, Seba, 29 Ofiri, Havila ndi Yobabu. Onsewa anali ana aamuna a Yokitani.

30 Chigawo chimene ankakhala chinayambira ku Mesa mpaka ku Seferi, ku dera la mapiri chakummawa.

31 Amenewa ndiwo ana a Semu monga mwa mafuko ndi ziyankhulo zawo, mʼmadera omwe ankakhala ndi mitundu yawo.

32 Amenewa ndiwo mafuko a ana aamuna a Nowa monga mwa mibado ya mitundu yawo. Mitundu yonse ya anthu inatuluka mwa iwowa ndi kufalikira pa dziko lonse lapansi chitatha chigumula chija.