Add parallel Print Page Options

Kugwa kwa Babuloni

18 Zitatha izi ndinaona mngelo wina akutsika kuchokera kumwamba. Iye anali ndi ulamuliro waukulu, ndipo dziko lapansi linawala ndi ulemerero. Mngeloyo anafuwula ndi mawu amphamvu kuti:

“ ‘Wagwa! Wagwa Babuloni Wamkulu!’
    Wasandulika mokhalamo ziwanda
ndi kofikako mizimu yonse yoyipa
    ndi mbalame zonse zonyansa
    ndi zodetsedwa.
Pakuti mayiko onse amwa
    vinyo ozunguza mutu wazigololo zake.
Mafumu a dziko lapansi achita naye chigololo,
    ndipo amalonda a dziko lapansi analemera kuchokera pa zolakalaka zake zosefukira.”

Awachenjeza kuti Athawe Chiweruzo cha Babuloni

Ndiponso ndinamva mawu ena kuchokera kumwamba akuti:

“ ‘Anthu anga tulukani, mwa iye,’
    mungachimwe naye
    kuti musadzalandire nawo gawo lililonse la miliri yake;
pakuti machimo ake awunjikana mpaka kumwamba,
    ndipo Mulungu wakumbukira milandu yake.
Bwezerani Iye monga momwe iye anakuchitirani.
    Mubwezereni mowirikiza pa zimene anachita.
    Mumusakanizire magawo awiri kuchokera mʼchikho chake.
Mumuzunze, kumumvetsa chisoni kwambiri
    monga mwaulemerero ndi zolakalaka
zimene anadzaza mu mtima mwake. Iye anadzikuza nʼkumati,
    ‘Ndinakhala monga mfumu yayikazi,
ine sindine wamasiye
    ndipo sindidzalira maliro.’
Chifukwa chake miliri yake idzamugonjetsa tsiku limodzi;
    imfa, kulira maliro ndi njala.
Iye adzanyeka ndi moto
    pakuti wamphamvu ndi Mulungu Ambuye amene wamuweruza.

Tsoka la Babuloni

“Mafumu a dziko lapansi, amene anachita naye chigololo nachita naye pamodzi zosangalatsa moyo uno, akadzaona utsi wa kunyeka kwake, adzalira nakhuza maliro ake. 10 Iwo adzayima kutali nalira chifukwa choopsedwa ndi mazunzo ake.

“ ‘Tsoka! Tsoka mzinda waukulu
    iwe, Babuloni mzinda wamphamvu!
Mu ora limodzi chiwonongeko chako chafika!’

11 “Amalonda a dziko lapansi adzalira nakhuza maliro ake chifukwa palibenso amene akugula katundu wawo, 12 katundu wagolide, siliva, miyala yamtengo wapamwamba ndi ngale; nsalu zoyera kwambiri zapamwamba ndi zofiira; nsalu zasilika ndi zapepo; mitengo iliyonse yonunkhira ndi zinthu zilizonse zopangidwa ndi mnyanga, kapena matabwa ogulidwa ndi ndalama zambiri kapena mkuwa kapena chitsulo ndi mwala wonyezimira; 13 zokometsera zakudya, mure, lubani ndi zofukiza zina, vinyo ndi mafuta a olivi, ufa wosalala ndi tirigu; ngʼombe ndi nkhosa; akavalo ndi ngolo; ndi anthu adzagulitsidwa ukapolo.

14 “Iwo adzanena kuti, ‘Chipatso chimene unachilakalaka chakuchokera. Chuma chako chonse ndi ulemerero zatha, sizidzapezekanso.’ 15 Amalonda amene anagulitsa zinthu izi napeza chuma kuchokera kwa iye adzayima patali potero ataopsedwa ndi mazunzo ake. Adzalira ndi kukhuza maliro 16 ndipo adzalira mokuwa kuti,

“ ‘Tsoka! Tsoka! Mzinda waukulu,
    iwe wovala nsalu zoyera kwambiri, zapepo ndi zofiira,
    ndi wonyezimira ndi golide, miyala yamtengo wapamwamba ndi ngale!
17 Chuma chambiri choterechi chafika powonongeka mu ora limodzi!’

“Oyendetsa sitima ndi onse oyenda pa sitima ya pamadzi, ogwira ntchito mʼsitima ndi onse amene amadalira nyanja pamoyo wa tsiku ndi tsiku adzayima patali potero. 18 Akadzaona utsi wa kunyeka kwake, adzakuwa kuti, ‘Kodi panalinso mzinda wina ngati mzinda waukuluwu?’ 19 Adzathira fumbi pamitu pawo ndipo adzalira nakhuza maliro kuti,

“Tsoka! Tsoka mzinda waukulu iwe,
    kumene onse anali ndi sitima pa nyanja
    analemera kudzera mʼchuma chake!
Mu ora limodzi wawonongedwa.

20 “Kondwerani chifukwa cha iye inu kumwamba!
    Kondwerani oyera mtima
    ndi atumwi ndi aneneri!
Mulungu wamuweruza iye
    monga momwe anakuchitirani inu.”

Chiwonongeko Chotsiriza cha Babuloni

21 Kenaka mngelo wamphamvu ananyamula mwala waukulu ngati mphero yayikulu nawuponya mʼnyanja nanena kuti,

“Mwa mphamvu chonchi
    mzinda waukulu wa Babuloni udzaponyedwa pansi,
    sudzapezekanso.
22 Mwa iwe simudzamvekanso liwu la woyimba zeze, ndi akatswiri a zoyimbayimba,
    oyimba zitoliro, ndi lipenga.
Mwa iwe simudzapezekanso
    mʼmisiri wina aliyense.
Mwa iwe simudzapezekanso
    phokoso la mphero.
23 Kuwala kwa nyale
    sikudzawunikanso mwa inu.
Mawu a mkwati ndi mkwatibwi
    sadzamvekanso mwa iwe.
Amalonda anu anali akuluakulu a dziko lapansi.
    Mitundu yonse inasokonezedwa ndi zamatsenga zako.
24 Mwa iye munapezeka magazi a aneneri ndi a oyera mtima,
    ndi onse amene anaphedwa pa dziko lapansi.”