Add parallel Print Page Options

Israeli Adzawonongedwa

Ine ndinaona Ambuye atayima pambali pa guwa lansembe, ndipo anati:

“Kantha mitu ya nsanamira
    kuti ziwundo za nyumba zigwedezeke.
Muzigwetsere pa mitu ya anthu onse,
    onse amene atsalira ndidzawapha ndi lupanga.
Palibe ndi mmodzi yemwe amene adzathawe,
    palibe amene adzapulumuke.
Ngakhale atakumba pansi mpaka ku malo a anthu akufa,
    dzanja langa lidzawatulutsa kumeneko.
Ngakhale atakwera kumwamba
    Ine ndidzawatsakamutsa kumeneko.
Ngakhale atakabisala pamwamba pa phiri la Karimeli,
    Ine ndidzawasaka kumeneko ndi kuwagwira.
Ngakhale atakabisala pansi pa nyanja yayikulu,
    ndidzalamula njoka kuti iwalume kumeneko.
Ngakhale adani awo awakusire ku ukapolo,
    ndidzalamula lupanga kuti liwaphe kumeneko.
Ndidzawayangʼanitsitsa
    kuti zoyipa ziwagwere; osati zabwino.”

Ambuye Yehova Wamphamvuzonse
    amene amakhudza dziko lapansi ndipo dzikolo limasungunuka,
    onse amene amakhala mʼmenemo amalira.
Dziko lonse lidzadzaza ngati mtsinje wa Nailo,
    kenaka nʼkuphwera ngati mtsinje wa ku Igupto.
Iye amene amamanga malo ake okhalamo kumwamba,
    ndi kuyika maziko ake pa dziko lapansi,
Iye amene amayitana madzi a ku nyanja
    ndikuwakhuthulira pa dziko lapansi,
    dzina lake ndiye Yehova.

“Kodi kwa Ine, inu Aisraeli, simuli
    chimodzimodzi ndi Akusi?”
            Akutero Yehova.
“Kodi sindine amene ndinatulutsa Israeli ku Igupto,
    Afilisti ku Kafitori
    ndi Aaramu ku Kiri?

“Taonani, maso a Ambuye Yehova
    ali pa ufumu wochimwawu.
Ndidzawufafaniza
    pa dziko lapansi.
Komabe sindidzawononga kotheratu
    nyumba ya Yakobo,”
            akutero Yehova.
“Pakuti ndidzalamula,
    ndipo ndidzagwedeza nyumba ya Israeli
    pakati pa mitundu yonse ya anthu
monga momwe amasefera ufa mʼsefa,
    koma palibe nʼkamwala kamodzi komwe kamene kadzagwe pansi.
10 Anthu onse ochimwa pakati pa anthu anga
    adzaphedwa ndi lupanga,
onse amene amanena kuti,
    ‘Tsoka silidzatigwera ife kapena kutiwononga.’

Kubwezeretsedwa kwa Israeli

11 “Tsiku limenelo ndidzabwezeretsa
    nyumba ya Davide imene inagwa.
Ndidzakonzanso malo amene anagumuka,
    ndi kuyimanganso
    monga inalili poyamba,
12 kuti adzatengenso otsala a Edomu
    ndi mitundu yonse imene imatchedwa ndi dzina langa,”
            akutero Yehova amene adzachita zinthu izi.

13 Yehova akunena kuti

“Nthawi ikubwera pamene mlimi wotipula adzapyola wokolola
    ndipo woponda mphesa adzapyola wodzala mbewu.
Mapiri adzachucha vinyo watsopano
    ndi kuyenderera pa zitunda zonse.
14 Ndidzawabwezeranso pabwino anthu anga Aisraeli;
    mizinda imene inali mabwinja idzamangidwanso ndipo azidzakhalamo.
Adzalima minda ya mpesa ndipo adzamwa vinyo wake;
    adzalima minda ndipo adzadya zipatso zake.
15 Ndidzakhazika Aisraeli mʼdziko mwawo,
    ndipo sadzachotsedwamonso mʼdziko
    limene Ine ndawapatsa,”

            akutero Yehova Mulungu wako.