Add parallel Print Page Options

22 Ndipo Davide anati, “Nyumba ya Yehova Mulungu idzakhala pano, ndiponso guwa lansembe zopsereza za Israeli.”

Kukonzekera Kumanga Nyumba ya Mulungu

Choncho Davide analamula kuti asonkhanitse alendo onse amene amakhala mu Israeli ndipo kuchokera pakati pawo anasankha amisiri a miyala kuti aseme miyala yomangira nyumba ya Mulungu. Ndipo anapereka zitsulo zambiri zopangira misomali ya zitseko za pa zipata ndi zolumikiza zake. Anaperekanso mkuwa wochuluka wokanika kuwuyeza. Iye anaperekanso mitengo yambiri ya mkungudza, yosawerengeka, pakuti anthu a ku Sidoni ndi a ku Turo anabweretsa yambiri kwa Davide.

Davide anati, “Mwana wanga Solomoni ndi wamngʼono ndipo sadziwa zambiri. Koma nyumba yomwe timangire Yehova iyenera kukhala yaulemerero, yotchuka ndi yokongola pamaso pa anthu a mitundu yonse. Choncho ndikonzekeratu zambiri.” Motero Davide anayikonzekera kwambiri asanamwalire.

Tsono iye anayitana Solomoni mwana wake ndipo anamulamula kuti adzamangire nyumba Yehova Mulungu wa Israeli. Davide anati kwa Solomoni, “Mwana wanga, ine ndinali ndi maganizo oti ndimangire nyumba Dzina la Yehova Mulungu wanga. Koma Yehova anandiyankhula kuti, ‘Iwe wapha anthu ambiri ndiponso wachita nkhondo zambiri. Sumangira dzina langa nyumba chifukwa wapha anthu ambiri pa dziko lapansi pamaso panga. Koma udzabala mwana wamwamuna amene adzakhala munthu wamtendere ndi wabata ndipo ndidzamupatsa mpumulo kuchokera kwa adani ake onse a mbali zonse. Dzina lake adzatchedwa Solomoni ndipo Ine ndidzapereka mtendere ndi bata kwa Israeli pa nthawi ya ulamuliro wake. 10 Iye ndiye adzandimangire nyumba. Adzakhala mwana wanga ndipo Ine ndidzakhala abambo ake. Ndipo ndidzakhazikitsa mpando wake waufumu mʼdziko la Israeli mpaka muyaya.’ ”

11 “Tsopano mwana wanga, Yehova akhale nawe ndipo upambane ndi kumanga Nyumba ya Yehova Mulungu wako, monga momwe Iye ananenera kuti udzatero. 12 Yehova akupatse nzeru ndi kumvetsetsa pamene Iye adzakuyika kukhala wolamulira Israeli, kuti udzasunge malamulo a Yehova Mulungu wako. 13 Ndipo udzapambana ngati udzamvera mosamala malangizo ndi malamulo amene Yehova anapereka kwa Aisraeli kudzera mwa Mose. Khala wamphamvu ndi wolimba mtima. Usachite mantha kapena kutaya mtima.

14 “Ine movutikira kwambiri ndapereka ku Nyumba ya Mulungu matani 3,400 agolide, matani 34,000 asiliva, ndiponso mkuwa ndi chitsulo, matabwa ndi miyala. Ndipo iwe utha kuwonjezerapo pa zimenezi. 15 Iwe uli ndi antchito ambiri: osema miyala, amisiri a miyala, ndi amisiri a matabwa, komanso anthu ambiri aluso la ntchito zosiyanasiyana, 16 zagolide ndi zasiliva, zamkuwa, zazitsulo, amisiri osawerengeka. Tsopano yamba ntchito, ndipo Yehova akhale nawe.”

17 Tsono Davide analamula atsogoleri onse a Israeli kuti athandize Solomoni mwana wake. 18 Iye anawawuza kuti, “Kodi Yehova Mulungu, sali nanu? Ndipo Iye siwakupatsani mpumulo mbali zonse? Pakuti Iyeyo wapereka eni nthaka kwa inu ndipo dziko lili pa ulamuliro wa Yehova ndi anthu ake. 19 Tsono perekani mtima wanu ndi moyo wanu kufunafuna Yehova Mulungu wanu. Yambani kumanga malo opatulika a Yehova Mulungu, kuti mubweretse Bokosi la Chipangano la Yehova ndi zinthu zopatulika za Mulungu mʼNyumba ya Mulungu imene idzamangidwa chifukwa cha dzina la Yehova.”